Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Hebrews 1 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Mnungu wakamba ni wandhu kwa kupitila Mwanawake

1Kale Mnungu wadakamba ni azee wathu kwa kupitila alosi wake. Wadachita chimwecho ndhawi zambili. 2Nambho masiku yano yothela wakamba niife kwa kupitila mwanawake. Kwa kupitila iye Mnungu wadaumba jhiko, wadamsanghula dala vonjhe vikhale vake. 3Mwana ni mng'azikilo wa ukulu wa Mnungu, ni iye watilangiza umo wali Mnungu, kwa kupitila mawu lake la mbhavu wachita vindhu vonjhe viyendekele kukhala ngati mumujha vili. Pambuyo pa kwayelecha wandhu machimo yawo, wakhala kumwamba kwa Mnungu, malo ya ulemelelo ya Mnungu.

Ukulu wa Mwana wa Mnungu

4Mnungu wadamchita mwana wake wakhale wamkulu kupitilila atumiki wake akumwamba, ni wadampacha jhina lalikulu kupitilila mayina ya atumiki amenewo. 5Pakuti Mnunngu siwadamkambilepo ata mmojhi wa atumiki wake akumwamba kuti,“Iwe ni mwana wangaine lelo nakhala Tate wako.”Nisiwadakambepo kwa nghani ya mtumiki waliyonjhe wa kumwamba kuti,“Ine sinikhale tate wakeniiye siwakhale mwana wanga”

6Nambho Mnungu yapo wamamtuma mwana wake wachisamba kujha pajhiko wadakamba kuti,“Atumiki wonjhe akumwamba Amnungu ifunika amlambile.”

7Nambho kwa nghani za atumiki akumwamba Amnungu, Mnungu wadakamba kuti,“Waachita atumiki wonjhe akumwamba Amnungu kukhala mbhepo,ni atumiki wake achameneo kukhala malilime ya moto.”

8Nambho kwa nghani za mwana Mnungu wadakamba kuti,“Iwe ni Mnungu ni siulamulile ngati mfumu muyaya!Iwe siwalamulile bwino wandhu wanu.

9Pakuti ukonda kuchita yovomelezeka ni uyipila kuchita yoipa.Ndendande Mnungu wako wakupatula ni voipani wakupacha kukondwa ni ulemelelo kupitilila achanjako.”

10Iye wadakambanjho,“Ambuye, imwe poyambila mudaumba jhiko,ni kwa manja yanu mdaumba kumwamba.

11Vimenevo sivichoke, nambho imwe simukhalile muyaya,vimenevo vonjhe sivithe ngati njhalu.

12Siuvikwinyekwinye ngati khoti,navo siving'anamulidwe ngati vovala.nambho iwe ni yuyujha siku zonjheni umoyo wako siukhala ni pothela”

13Mnungu siwadamkambilepo ata mmojhi wa atumiki wake wa kumwamba kuti,“Khala kumalo yanga ya ulemu,mbaka yapo sinikuthangatile kwaakhoza adani wako ni kwalamulila.”

14Atumiki akumwamba Amnungu nichiyani? Nambho ni mizimu iyo yatumikila Amnungu yawo atumidwa kwathangatila wandhu yawo salandile uwomboli.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]