Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Philemon 1 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Ine Poolo omangidwa ndande ya Yesu Kilisito, ni mbale wathu Timoseo nilinayo pano. Nikulembela Filimoni okondwendwa wathu ni uyo tichita njhito pamojhi ni ife,

2ni kwa mlongo wathu Afia, ni Alikipo ochita njhito mnjathu, nighulu la wandhu amkhulupilila Yesu akomanilana mnyumba yako Filimoni.

3Nikupembhelani kwa Mnungu Tate ni Mbuye wathu Yesu Kilisito akuchitileni ubwino ni mtendele.

Chikondi ni chikhulupi cha Filimoni

4Siku zonjhe niyamika Mnungu yapo nikukumbukila mmapembhelo yanga. 5Nivela nghani za chikhulupi ni chikondi chako kwa Ambuye Yesu ni kwa wandhu wonjhe a Mnungu. 6Nipembhela dala kukhulupilila kwako uko ugwilizana niife kukukozeche kujhiwa mwawi wonjhe tilinawo kwa kumkhulupilila Kilisito. 7Chikondi chako chanikondwecha ni kunithila mtima, ni wakondwecha mitima ya wandhu a Mnungu.

Poolo wapembha Onesimo walekeleledwe

8Pandande iyi kuchokana ni ulamuli napachidwa Kilisito, nidakakhoza kukutuma kuchita chimenecho ufunika kuchita. 9Nambho nikupembha kwa chikondi. Ine Poolo nili mzee ni chipano namangidwa ndande nimamuzila Yesu. 10Nikupembha ndande ya mwanawanga Onesimo, uyo wali mwanawanga kwa kumkulupilila Kilisito Yesu, ndande nakhala tate wake nili mndende. 11Mmayambo wadalibe mthandizo kwako, chipano wakhala mthandizo kwako ni kwanga.

12Nambho chipano nimbweza kwa iwe Onesimo, uyu nimkonda kwa mtima wanga wonjhe. 13Nidakakonda wakhale pano, wanithangatile pamalo pako ndhawi iyo nali mndende ndande ya Uthenga wa Wabwino. 14Nambho sinidafune kuchita chalichonjhe popande kulolezedwa niiwe, sinifuna kukukakamiza unithangatile, dala kila chindhu chako chabwino chichitike kwa kukonda kwako.

15Ikhozeka Onesimo wadachoka kwako kwa ndhawi yochepa dala ukhoze kukhala nayonjho masiku yonjhe. 16Ni chipano iye osati kapolo, nambho chipano wakhala kapolo wabwino, ine nimkonda kupunda, nambho iwe siumkonde kupitilila, iye siwakuchitile njhito ngati kapolo ni kwatumikila Ambuye ngati umo iwe wachitila Ambuye.

17Chimwecho, ngati ujhiwa ine ni iwe tikhulupilila chindhu chimojhi, basi mlandile Onesimo ngati umo udakanilandila ine. 18Ngati wakulakwila chalichonjhe, kapina ngati uliningawa ni ine. 19Ine Poolo nilemba chikalakala ichi kwa jhanja langa kuti sinikulipa. Ndipo nilibe ndande ya kukamba kuti iwe uli ni ngawa kwa ine. 20Nchimwecho mbale wanga, nichitile ubwino uwu ndande ya Ambuye, ukondweleche mtima wanga ngati mbale wanga pakumkhulupila Kilisito.

21Nikulembela yaya ndande nijhiwa kuti siuyavele ni siuchite kupitilila yayo nikupembha. 22Pamojhi ni yaya, niikile chumba chofikila, ndande nikhulupila kwa mapembhelo yanu, Mnungu siwanithangatile nijhenjho kwanu.

Moni zomalizila

23Epafula, uyo wadali mndende pamojhi ni ine ndande ya kumuuzila Kilisito Yesu, wakulonjela. 24Naonjho ochita njhito anjanga, Maluko ni Alisitako ni Dema ni Luka, akulonjela.

25Nikupembhelani Ambuye Yesu Kilisito akuchitileni vabwino.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]