Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Titus 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 But as for you, speak what is fitting for sound teaching. Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.
2 Older men are to be sober-minded, dignified, self-controlled, sound in faith, love, and patient endurance. Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.
3 Older women likewise: deeply respectful in behavior, not slanderers, not enslaved to much wine, but teachers of what is good, Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino.
4 so that they may train the young women to love their husbands and to love their children, Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo.
5 self-controlled, pure, working at home, good, submissive to their own husbands, so our Father's word isn't insulted. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.
6 Likewise urge the younger men to be self-controlled. Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa.
7 In everything be an example of good works, with integrity and dignity in your teaching, Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako.
8 healthy words beyond criticism, so any opponent is ashamed, with nothing bad to say about us. Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.
9 Slaves must submit to their own masters in everything, pleasing them, not talking back, Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo
10 not stealing, but showing complete, good faithfulness, so they adorn, in everything, the teaching of our Father, our Savior. kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.
11 For the grace of our Father has appeared, bringing salvation to all people, Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse.
12 teaching us to reject wickedness and worldly desires, and live self-controlled, upright, and godly lives in this present age, Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino,
13 waiting for the blessed hope and glorious appearing of our great God and Savior, Jesus Christ, pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,
14 who gave himself for us to redeem us from all lawlessness and purify for himself a people of his own, eager for good works. amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
15 Declare these things; encourage and rebuke with all authority. Let no one disregard you. Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]