Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Titus 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Paul, servant of our Father and apostle of Jesus Christ, for the faith of our Father's chosen ones and knowledge of truth leading to devotion to God, Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu
2 in the hope of eternal life, which our Father, who never lies, promised before the ages began, ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe.
3 and at his own time he revealed his word through the message entrusted to me by command of our Father, our Savior. Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.
4 To Titus, my true child in shared faith: grace and peace from our Father and Christ Jesus our Savior. Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
5 I left you in Crete for this reason: to finish what remained and appoint elders in every town, as I instructed you. Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira.
6 An elder must be blameless, husband of one wife, with faithful children not accused of wild living or rebellion. Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera.
7 For an overseer, as our Father's steward, must be blameless—not arrogant, not quick-tempered, not a drunkard, not violent, not greedy for dishonest gain, Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo.
8 but hospitable, a lover of what is good, self-controlled, upright, holy, and disciplined. Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo.
9 He must hold firmly to the trustworthy message as taught, so he can encourage with sound teaching and refute those who oppose it. Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.
10 For many are rebellious, talking nonsense and misleading others—especially the circumcision group. Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo.
11 They must be silenced, because they wreck whole households, teaching what they shouldn't, for shameful profit. Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo.
12 One of their own prophets said it: "Cretans are always liars, evil beasts, lazy gluttons." Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.”
13 This testimony is true. Therefore rebuke them sharply, so that they will be sound in the faith, Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona,
14 and ignore Jewish myths and rules from those who reject the truth. kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi.
15 Everything is pure to the pure; but for the corrupted and unbelieving, nothing is pure—both mind and conscience made unclean. Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa.
16 They claim to know our Father, but deny him by their actions—detestable, disobedient, unfit for any good work. Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]