Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Titus 1 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Ine Poolo nalemba Kalata ino, ine ni mtumiki wa Mnungu ni mtumwi wa Yesu Kilisito. Ine nasanghidwa dala nathangatile wandhu aendekele bwino pakumkhulupilila Mnungu ni kwaachogoza aujhiwe uzene dala amjhiwe Yesu ni akhoze kukhala kwa kumkwadilicha Mnungu,

2pa yameneyo akhala ni chikhulupi chopata umoyo wa muyaya. Mnungu uyo siwakamba unami, wadakamba kuti siwatipache umoyo umenewo yapo jhiko likali losaumbidwe, 3nindhawi ya Mnungu yajha, wadaujhiwicha pa uthenga wake. Ine nidapachidwa uthenga umenewo, nilalikile kwa lamulo la Mnungu olamicha wathu.

4Nikulembela iwe Tito, mwanawanga wokondedwa pachikhulupi pakuti iwe ni ine taonjhe timkhulupilila Kilisito. Nimpembha Mnungu wakuchitileni vabwino ni mtendele kuchokela kwa Mnungu Atate, ni kuchokela kwa Kilisito Yesu mwomboli wathu.

Njhito ya Tito ku mujhi wa Kilete

5Nidakusiya ku mujhi wa Kilete dala uike bwino yajha siyadaikidwe bwino, ni kwasanghula azee achogoleli aghulu la wandhu amkhulupilila Kilisito mumijhi yonjhe. Chita chimwecho ngati umo nidakuagiza, 6Mzee mchogoleni wa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito ifunika wakhale mundhu uyo wakambidwa bwino, wali ni wamkazi mmojhipe, ni wana wake afunika akhale okhulupilila ni sadakhala andewo kapina ambwinya, 7pakuti mchogoleli wagulu la wandhu amkhulupilila Kilisito wapota njhito ya Mnungu, wafunika wakhale mundhu walibe volakwa. Siwadakhala wadama, siwadakhala mundhu okwiya chisanga, wakumwa mowa, wandewo kapina wokonda kupata ndalama kupunda. 8Nambho wafunika wakhale mundhu wolandila alendo ni uyo wakonda kuchita vindhu kwa ubwino. Wafunika wakhale mundhu uyo siwafuna ndewo, wokhulupilika niuyo wali ni ulemu. 9Mcholeli ifunika wagwile mokwanila uthenga ujha wazene ngati umo udayaluzidwa. Ndeumo siukhozele kwatila wina mtima kwa mayaluzo yazene ni kuvumbula volakwa va wajha achucha mayaluzo yameneyo.

10Pakuti alipo wandhu ambili anyiyawo savela, asa Ayahudi yawo akali kugwilila chikhalidwe chawo, awananga wandhu kwa mawu ya chisabobwa ni yonyenga. 11Tito wakanize kuyaluza, pakuti awananga gulu lonjhe kwa kuyaluza vindhu ivo safunika kuyaluza, achita chimwecho kwa maganizo yoyipa ya kupata ndalama. 12Ata mmojhi wa alosi wao, uyo wadali mundhu wa kumujhi wa Kilete wadakamba, “Akilete akamba unami siku zonjhe, ngati zinyama zoipa aludyo ni alesi!” 13Niiye wadakamba uzene, nikwandande imeneyo, ufunika kwanyindila mokalipa, dala akhale ni chikhulupi cha zene. 14Sadayendekela kugwililila mayu yopande mate ya Ayahudi ni maganizo ya wandhu, yayo yakambidwa ni wandhu yawo aukana uzene. 15Vindhu vonjhe ni vabwino kwa wandhu yawo ali abwino, nambo palibe chalichonjhe icho chali chabwino kwa wandhu yawo adechedwa ni yawo sadakhulupilile, pakuti mitima yawo ni njelu zawo zadechedwa. 16Wandhu ngati amenewo ajhidama kuti amjhiwa Mnungu, nambho kwa vichito vawo amkana. Niwandhu yawo atiipicha kupunda ni amtafu, safunika kwa chindhu chalichonjhe chabwino.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]