Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Lamentations 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Remember, our Father, what has happened to us; look and see our disgrace. Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira; yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.
2 Our inheritance has been turned over to strangers, our homes to foreigners. Apereka cholowa chathu kwa obwera, nyumba zathu kwa alendo.
3 We have become orphans, fatherless; our mothers are like widows. Takhala amasiye ndi wopanda abambo, amayi athu ali ngati akazi amasiye.
4 We pay for our own water to drink; even firewood costs us money. Tiyenera kugula madzi amene timamwa, nkhuni zathunso nʼzogula.
5 Our pursuers are at our necks; we are worn out and given no rest. Otilondola atigwira pakhosi; tafowoka ndipo sakutilola kupumula.
6 We submitted to Egypt and Assyria just to get enough bread. Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya kuti tipeze chakudya.
7 Our ancestors sinned, and are no more; and we bear their punishment. Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale, koma chilango chawo chili pa ife.
8 Slaves rule over us; there is no one to free us from their grip. Akapolo akutilamulira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.
9 We risk our lives to get our bread, because of the sword in the wilderness. Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe chifukwa cha lupanga mʼchipululu.
10 Our skin is hot as an oven, scorched by the burning heat of famine. Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo, chifukwa cha kuwawa kwa njala.
11 Women are violated in Zion, virgins in the cities of Judah. Amayi agwiriridwa mu Ziyoni, ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.
12 Princes are hung up by their hands; the elders receive no respect. Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo, akuluakulu sakuwalemekeza.
13 Young men toil at the millstones; boys stagger under loads of wood. Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu; anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.
14 The elders have left the city gate, the young men their music. Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda; achinyamata aleka nyimbo zawo.
15 The joy of our hearts has ceased; our dancing has turned to mourning. Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu; kuvina kwathu kwasanduka maliro.
16 The crown has fallen from our head. Woe to us, for we have sinned! Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!
17 Because of this our heart has grown faint; because of these things our eyes have grown dim. Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi, chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,
18 For Mount Zion lies desolate; jackals prowl over it. pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja, nkhandwe zikungoyendayendapo.
19 You, our Father, are enthroned forever; your throne endures from generation to generation. Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya; mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.
20 Why do you forget us forever, forsake us for so many days? Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse? Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?
21 Restore us to yourself, our Father, and we will return; renew our days as they once were, Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere; mukonzenso masiku athu akhale monga akale,
22 unless you have utterly rejected us, and are angry with us beyond measure. pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu, ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]