Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Lamentations 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 How the Sovereign Father in his anger has shrouded daughter Zion in a cloud! He has hurled down from heaven to earth the splendor of Israel; he has not remembered his footstool in the day of his anger. Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo wa mkwiyo wake! Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli kuchoka kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso popondapo mapazi ake.
2 The Sovereign Father has swallowed up without mercy all the dwellings of Jacob; in his wrath he has torn down the strongholds of daughter Judah. He has brought down to the ground in dishonor her kingdom and its rulers. Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo; mu mkwiyo wake anagwetsa malinga a mwana wamkazi wa Yuda. Anagwetsa pansi mochititsa manyazi maufumu ndi akalonga ake.
3 In fierce anger he has stripped Israel of all her strength; he has withdrawn his right hand and left them exposed to the enemy. He has burned in Jacob like a flaming fire that consumes on every side. Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola nyanga iliyonse ya Israeli. Anabweza dzanja lake lamanja pamene mdani anamuyandikira. Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.
4 He has bent his bow like an enemy, his right hand poised like a foe; and he has killed all who were lovely to see. In the tent of daughter Zion he has poured out his fury like fire. Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani; wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani, ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira. Ukali wake ukuyaka ngati moto pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.
5 The Sovereign Father has become like an enemy; he has swallowed up Israel. He has swallowed up all her palaces and laid in ruins her strongholds, and he has heaped mourning and lamentation on daughter Judah. Ambuye ali ngati mdani; wawonongeratu Israeli; wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu ndipo wawononga malinga ake. Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira kwa mwana wamkazi wa Yuda.
6 He has stripped his shelter like a garden, he has ruined his appointed place. Our Father has made Zion forget appointed feast and sabbath, and in his fierce anger he has spurned king and priest. Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda; wawononga malo ake a msonkhano. Yehova wayiwalitsa Ziyoni maphwando ake oyikika ndi masabata ake. Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza mfumu ndi wansembe.
7 The Sovereign Father has rejected his altar, disowned his sanctuary; he has handed over to the enemy the walls of her palaces. They raised a shout in the house of our Father as on a day of festival. Ambuye wakana guwa lake la nsembe ndipo wasiya malo ake opatulika. Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu kwa mdani wake; adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.
8 Our Father determined to lay in ruins the wall of daughter Zion. He stretched out the measuring line; he did not hold back his hand from destroying. He made rampart and wall lament; together they fell to ruin. Yehova anatsimikiza kugwetsa makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni. Anawayesa ndi chingwe ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa. Analiritsa malinga ndi makoma; onse anawonongeka pamodzi.
9 Her gates have sunk into the ground; he has ruined and broken her bars. Her king and her princes are among the nations; the law is no more, and her prophets find no vision from our Father. Zipata za Yerusalemu zalowa pansi; wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake. Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu, palibenso lamulo, ndipo aneneri ake sakupeza masomphenya kuchokera kwa Yehova.
10 The elders of daughter Zion sit on the ground in silence; they have thrown dust on their heads and put on mourning clothes. The young women of Jerusalem have bowed their heads to the ground. Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala chete pansi; awaza fumbi pa mitu yawo ndipo avala ziguduli. Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo pansi.
11 My eyes are worn out from weeping; my stomach churns; my heart is poured out on the ground because of the destruction of the daughter of my people, as children and infants faint in the streets of the city. Maso anga atopa ndi kulira, ndazunzika mʼmoyo mwanga, mtima wanga wadzaza ndi chisoni chifukwa anthu anga akuwonongeka, chifukwa ana ndi makanda akukomoka mʼmisewu ya mu mzinda.
12 They cry to their mothers, "Where is bread and wine?" as they faint like the wounded in the streets of the city, as their life is poured out in their mothers' arms. Anawo akufunsa amayi awo kuti, “Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?” pamene akukomoka ngati anthu olasidwa mʼmisewu ya mʼmizinda, pamene miyoyo yawo ikufowoka mʼmanja mwa amayi awo.
13 What can I say for you, to what can I compare you, daughter Jerusalem? What can I liken to you, that I may comfort you, virgin daughter Zion? For your ruin is vast as the sea; who can heal you? Ndinganene chiyani za iwe? Ndingakufanizire ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu? Kodi ndingakufanizire ndi yani kuti ndikutonthoze, iwe namwali wa Ziyoni? Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja, kodi ndani angakuchiritse?
14 Your prophets have seen for you false and deceptive visions; they did not expose your guilt to restore your fortunes, but have seen for you oracles that are false and misleading. Masomphenya a aneneri ako anali abodza ndi achabechabe. Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo poyika poyera mphulupulu zako. Mauthenga amene anakupatsa anali achabechabe ndi osocheretsa.
15 All who pass by clap their hands at you; they hiss and shake their heads at daughter Jerusalem: "Is this the city that was called the perfection of beauty, the joy of all the earth?" Onse oyenda mʼnjira yako akukuwombera mʼmanja; akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu: “Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa wokongola kotheratu, chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”
16 All your enemies open their mouths against you; they hiss and gnash their teeth and cry, "We have swallowed her! This is the day we longed for; we have found it, we have seen it!" Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza; iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo, ndipo akuti, “Tamumeza. Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera; tili ndi moyo kuti tilione.”
17 Our Father has done what he purposed; he has carried out his word which he commanded long ago. He has torn down without pity; he has let the enemy gloat over you and raised up the power of your foes. Yehova wachita chimene anakonzeratu; wakwaniritsa mawu ake, amene anatsimikiza kale lomwe. Wakuwononga mopanda chifundo, walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako, wakweza mphamvu za adani ako.
18 The people's heart cried out to the Sovereign Father. Wall of daughter Zion, let tears stream down like a torrent day and night! Give yourself no rest, your eyes no relief. Mitima ya anthu ikufuwulira Ambuye. Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni, misozi yako itsike ngati mtsinje usana ndi usiku; usadzipatse wekha mpumulo, maso ako asaleke kukhetsa misozi.
19 Arise, cry out in the night at the start of each night watch! Pour out your heart like water before the Sovereign Father! Lift your hands to him for the lives of your children, who faint from hunger at every street corner. Dzuka, fuwula usiku, pamene alonda ayamba kulondera; khuthula mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye. Kweza manja ako kwa Iye chifukwa cha miyoyo ya ana ako, amene akukomoka ndi njala mʼmisewu yonse ya mu mzinda.
20 Look, our Father, and consider: whom have you ever treated like this? Should women eat their offspring, the children they have cradled? Should priest and prophet be killed in the sanctuary of the Sovereign Father? Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani: kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi? Kodi amayi adye ana awo, amene amawasamalira? Kodi ansembe ndi aneneri awaphere mʼmalo opatulika a Ambuye?
21 Young and old lie on the ground in the streets; my young women and my young men have fallen by the sword. You have killed them in the day of your anger, slaughtering without pity. Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda; anyamata anga ndi anamwali anga aphedwa ndi lupanga. Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu; mwawapha mopanda chifundo.
22 You summoned, as to a festival day, terrors on every side; and on the day of our Father's anger no one escaped or survived. My enemy has destroyed those I cradled and raised. Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando, chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse. Pa tsiku limene Yehova wakwiya palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo; mdani wanga wawononga onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]