Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Lamentations 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 I am the man who has seen affliction under the rod of his wrath. Ine ndine munthu amene ndaona masautso ndi ndodo ya ukali wake.
2 He has driven me away and made me walk in darkness without any light. Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa mu mdima osati mʼkuwala;
3 Surely against me he turns his hand again and again, all day long. zoonadi anandikantha ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.
4 He has worn away my flesh and my skin; he has broken my bones. Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo waphwanya mafupa anga.
5 He has besieged me and surrounded me with bitterness and hardship. Wandizinga ndi kundizungulira ndi zowawa ndi zolemetsa.
6 He has made me dwell in darkness like those long dead. Wandikhazika mu mdima ngati amene anafa kale.
7 He has walled me in so I cannot escape; he has weighed down my chains. Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe, wandimanga ndi maunyolo.
8 Even when I call out and cry for help, he shuts out my prayer. Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo, amakana pemphero langa.
9 He has blocked my ways with cut stones; he has made my paths crooked. Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema; ndipo wakhotetsa tinjira tanga.
10 He is a bear lying in wait for me, a lion in hiding. Wandidikirira ngati chimbalangondo, wandibisalira ngati mkango.
11 He drove me off my path and tore me to pieces; he has made me desolate. Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba, ndipo wandisiya wopanda thandizo.
12 He bent his bow and set me as the target for his arrow. Wakoka uta wake ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.
13 He drove the arrows of his quiver into my vitals. Walasa mtima wanga ndi mivi ya mʼphodo mwake.
14 I have become the laughingstock of all my people, their mocking song all day long. Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse; amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.
15 He has filled me with bitterness; he has sated me with bitterness. Wandidyetsa zowawa ndipo wandimwetsa ndulu.
16 He has made my teeth grind on gravel, and made me cower in the dust. Wathyola mano anga ndi miyala; wandiviviniza mʼfumbi;
17 My soul has lost all peace; I have forgotten what happiness is. Wandichotsera mtendere; ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.
18 So I say, "My endurance has perished, and so has my hope from our Father." Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”
19 Remember my affliction and my wandering, the bitterness and the gall! Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala, zili ngati zowawa ndi ndulu.
20 My soul continually remembers it and is bowed down within me. Ine ndikuzikumbukira bwino izi, ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.
21 But this I call to mind, and therefore I have hope: Komabe ndimakumbukira zimenezi, nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.
22 The covenant love of our Father never ceases; his mercies never come to an end; Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha.
23 they are new every morning; great is your faithfulness. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
24 "Our Father is all I need," says my soul, "therefore I will hope in him." Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse; motero ndimamuyembekezera.”
25 Our Father is good to those who wait for him, to the soul who seeks him. Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye, kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;
26 It is good to wait quietly for the salvation of our Father. nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha Yehova modekha.
27 It is good for a man to bear the yoke in his youth. Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli pamene ali wamngʼono.
28 Let him sit alone in silence when it is laid on him; Akhale chete pa yekha, chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.
29 let him put his mouth in the dust—there may yet be hope; Abise nkhope yake mʼfumbi mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.
30 let him give his cheek to the one who strikes, and be filled with insults. Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye, ndipo amuchititse manyazi.
31 For the Sovereign Father will not abandon forever. Chifukwa Ambuye satayiratu anthu nthawi zonse.
32 Though he causes grief, he will have compassion according to the abundance of his covenant love; Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo, chifukwa chikondi chake ndi chosatha.
33 for he does not willingly afflict or grieve people. Pakuti sabweretsa masautso mwadala, kapena zowawa kwa ana a anthu.
34 To crush underfoot all the prisoners of the earth, Kuphwanya ndi phazi a mʼndende onse a mʼdziko,
35 to deny a man justice in the sight of the Most High, kukaniza munthu ufulu wake pamaso pa Wammwambamwamba,
36 to deprive a man of justice in his case—the Sovereign Father does not approve. kumana munthu chiweruzo cholungama— kodi Ambuye saona zonsezi?
37 Who has spoken and it came to pass, unless the Sovereign Father has commanded it? Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika ngati Ambuye sanavomereze?
38 Is it not from the mouth of the Most High that both calamity and good come? Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?
39 Why should a living man complain about the punishment for his sins? Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula akalangidwa chifukwa cha machimo ake?
40 Let us examine and test our ways, and return to our Father! Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu, ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.
41 Let us lift up our hearts and our hands to our Father in heaven: Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:
42 "We have sinned and rebelled, and you have not forgiven. “Ife tachimwa ndi kuwukira ndipo inu simunakhululuke.
43 You have wrapped yourself in anger and pursued us, killing without pity; “Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo mwatitha mopanda chifundo.
44 you have wrapped yourself with a cloud so that no prayer can pass through. Mwadzikuta mu mtambo kotero mapemphero athu sakukufikani.
45 You have made us scum and refuse among the peoples. Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala pakati pa mitundu ya anthu.
46 All our enemies open their mouths against us; “Adani anthu atitsekulira pakamwa.
47 panic and pitfall have come upon us, devastation and destruction." Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje, tapasuka ndi kuwonongedwa.”
48 My eyes flow with streams of water over the destruction of my people. Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe chifukwa anthu anga akuwonongedwa.
49 My eyes will flow without ceasing, without respite, Misozi idzatsika kosalekeza, ndipo sidzasiya,
50 until our Father looks down and sees from heaven. mpaka Yehova ayangʼane pansi kuchokera kumwamba ndi kuona.
51 My eyes bring grief to my soul at the fate of all the daughters of my city. Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.
52 I have been hunted like a bird by those who were my enemies without cause; Akundisaka ngati mbalame, amene anali adani anga, popanda chifukwa.
53 they flung me alive into a pit and cast stones on me; Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje ndi kundiponya miyala;
54 water closed over my head; I said, "I am lost." madzi anamiza mutu wanga ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.
55 I called on your name, my Father, from the depths of the pit; Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova, kuchokera mʼdzenje lozama.
56 you heard my plea: "Do not turn a deaf ear to my cry for help!" Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere kulira kwanga kopempha thandizo.”
57 You came near on the day I called on you; you said, "Do not fear!" Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani, ndipo munati, “Usaope.”
58 You have taken up my cause, Sovereign Father; you have redeemed my life. Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga; munapulumutsa moyo wanga.
59 You have seen the wrong done to me, my Father; judge my cause. Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira. Mundiweruzire ndinu!
60 You have seen all their vengeance, all their plots against me. Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine.
61 You have heard their taunts, my Father, all their plots against me, Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo, chiwembu chawo chonse pa ine,
62 the lips and thoughts of my assailants against me all day long. manongʼonongʼo a adani anga ondiwukira ine tsiku lonse.
63 Watch their every move; I am the object of their mocking song. Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira, akundinyoza mu nyimbo zawo.
64 You will repay them, my Father, according to the work of their hands. Inu Yehova, muwabwezere chowayenera, chifukwa cha zimene manja awo achita.
65 You will give them hardness of heart; your curse will be on them. Phimbani mitima yawo, ndipo matemberero anu akhale pa iwo!
66 You will pursue them in anger and destroy them from under the heavens of our Father. Muwalondole mwaukali ndipo muwawonongeretu pa dziko lapansi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]