Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Job 27 OCCL

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

2“Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama,Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,

3nthawi zonse pamene ndili ndi moyo,mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,

4pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa,lilime langa silidzayankhula zachinyengo.

5Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona;mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.

6Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere;chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.

7“Mdani wanga akhale ngati woyipa,wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!

8Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa,pamene Mulungu achotsa moyo wake?

9Kodi Mulungu amamva kulira kwakepamene zovuta zamugwera?

10Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse?Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?

11“Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndiposindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.

12Inu mwadzionera nokha zonsezi.Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?

13“Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa,cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.

14Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipozidzukulu zake zidzasowa zakudya.

15Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri,ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.

16Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,ndi kukundika zovala ngati mchenga,

17zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale,ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.

18Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche,ili ngati msasa umene mlonda amamanga.

19Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko;akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.

20Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula;mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.

21Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipoimamuchotsa pamalo pake.

22Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni,pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.

23Mphepoyo imamuwomba ndithundipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]