Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 9 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 But there will be no gloom for her that was in anguish. Earlier he humbled the land of Zebulun and Naphtali, but later he honored the way of the sea, beyond the Jordan, Galilee of the nations. Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.
2 The people walking in darkness have seen a great light; on those who lived in a land of deep darkness, a light has shone. Anthu oyenda mu mdima awona kuwala kwakukulu; kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani kuwunika kwawafikira.
3 You have multiplied the nation; you have increased its joy. They rejoice before you as with joy at the harvest, as men are glad when they divide the plunder. Inu mwauchulukitsa mtundu wanu ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo. Iwo akukondwa pamaso panu, ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola, ngatinso mmene anthu amakondwera pamene akugawana zolanda ku nkhondo.
4 For the yoke of his burden, and the bar across his shoulder, the rod of his oppressor, you have shattered as on the day of Midian. Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani, inu mwathyola goli limene limawalemera, ndodo zimene amamenyera mapewa awo, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.
5 For every boot of the trampling warrior in the din of battle, and every garment soaked in blood, will be burned as fuel for the fire. Nsapato iliyonse ya munthu wankhondo, ndiponso chovala chilichonse chodonthekera magazi zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni.
6 For to us a child is born, to us a son is given; and the government will be upon his shoulder. And his name will be called Wonderful Counselor, Mighty God, Everlasting Father, Prince of Peace. Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
7 There will be no end to the increase of his government and peace, on the throne of David and over his kingdom, to establish it and to uphold it with justice and with righteousness from now on and forevermore. The zeal of the Father of heaven's armies will accomplish this. Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.
8 The Sovereign Father has sent a word against Jacob, and it has fallen on Israel. Ambuye atumiza mawu otsutsa Yakobo; ndipo mawuwo agwera pa Israeli.
9 And all the people will know it—Ephraim and the inhabitants of Samaria—who say with proud and arrogant hearts: Anthu onse okhala mu Efereimu ndi okhala mu Samariya, adzadziwa zimenezi. Iwo amayankhula modzikuza kuti,
10 "The bricks have fallen, but we will rebuild with cut stones; the sycamores have been cut down, but we will put cedars in their place." “Ngakhale njerwa zagumuka, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema. Mitanda ya mkuyu yagwetsedwa, koma ife tidzayika mitanda ya mkungudza mʼmalo mwake.”
11 So our Father raises against them the adversaries of Rezin, and stirs up their enemies. Koma Yehova wadzutsa adani kuti alimbane nawo ndipo wawafulumiza adani awo kuti amenyane nawo.
12 Aram from the east and the Philistines from the west have devoured Israel with open mouth. For all this his anger has not turned away, and his hand is still outstretched. Asiriya ochokera kummawa ndi Afilisti ochokera kumadzulo ndipo ayasama pakamwa kuti adye a Israeli. Komabe, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
13 Yet the people did not turn to the one who struck them, nor did they seek the Father of heaven's armies. Koma anthu sanabwerere kwa amene anawakantha uja, ngakhale kufunafuna Yehova Wamphamvuzonse.
14 So our Father cut off from Israel both head and tail, palm branch and reed, in a single day, Choncho Yehova adzadula mutu wa Israeli pamodzi ndi mchira womwe, nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe tsiku limodzi;
15 the elder and the honored man are the head, and the prophet who teaches lies is the tail. mutuwo ndiye akuluakulu ndi olemekezeka, mchira ndiye aneneri ophunzitsa zabodza.
16 For those who guide this people lead them astray, and those who are guided by them are swallowed up. Amene amatsogolera anthuwa ndiwo amawasocheretsa, ndipo otsogoleredwa amatayika.
17 Therefore the Sovereign Father does not rejoice over their young men, and has no compassion on their orphans and their widows; for everyone is godless and an evildoer, and every mouth speaks foolishness. For all this his anger has not turned away, and his hand is still outstretched. Nʼchifukwa chake Ambuye adzakondwera nawo achinyamata, ngakhale kuwachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye, pakuti aliyense ndi wosapembedza Mulungu ndiponso ndi wochimwa ndipo aliyense amayankhula zopusa. Komabe, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
18 For wickedness burns like a fire; it consumes briers and thorns; it kindles the thickets of the forest, and they roll upward in a column of smoke. Ndithu kuyipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto; moto wake umanyeketsa mkandankhuku ndi minga, umayatsa nkhalango yowirira, ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo.
19 Through the wrath of the Father of heaven's armies, the land is scorched, and the people have become like fuel for the fire; no one spares his brother. Dziko lidzatenthedwa ndi ukali wa Yehova Wamphamvuzonse, dziko lidzatenthedwa ndipo anthu adzakhala ngati nkhuni zosonkhera moto; palibe munthu amene adzachitire chifundo mʼbale wake.
20 They carve on the right, but are still hungry; they devour on the left, but are not satisfied; each devours the flesh of his own arm. Kudzanja lamanja adzapeza chakudya nʼkudya, koma adzakhalabe ndi njala; kudzanja lamanzere adzapeza chakudya nʼkudya, koma sadzakhuta. Aliyense azidzadya ana ake omwe.
21 Manasseh devours Ephraim, and Ephraim Manasseh, and together they are against Judah. For all this his anger has not turned away, and his hand is still outstretched. Manase adzadya Efereimu ndipo Efereimu adzadya Manase; onsewa pamodzi adzadya Yuda. Komabe pa zonsezi, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]