Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 8 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Our Father said to me, "Take a large tablet and write on it plainly: 'Belonging to Maher-shalal-hash-baz.'" Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.
2 So I called reliable witnesses to attest for me—Uriah the priest and Zechariah son of Jeberechiah. Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”
3 Then I went to the prophetess; she conceived and bore a son, and our Father said to me, "Name him Maher-shalal-hash-baz. Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’
4 Before the boy knows how to cry 'My father' or 'My mother,' Damascus's wealth and Samaria's plunder will be carried off before Assyria's king." Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
5 Our Father spoke to me yet again: Yehova anayankhulanso ndi Ine;
6 "Because this people has refused the gently flowing waters of Shiloah and rejoices over Rezin and the son of Remaliah, “Popeza anthu a dziko ili akana madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu, ndipo akukondwerera Rezini ndi mwana wa Remaliya,
7 therefore the Sovereign Father is about to bring up against them the mighty floodwaters of the River—the king of Assyria and all his glory. It will rise over all its channels and overflow all its banks, nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo; mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo. Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse ndi mʼmagombe ake onse.
8 and it will sweep on into Judah, flooding and passing through, reaching up to the neck; and its outstretched wings will fill the breadth of your land, Immanuel." Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira, adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi. Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse, iwe Imanueli!”
9 Be shattered, you peoples, and be broken! Listen, all you distant lands! Strap on your armor and be broken; strap on your armor and be broken! Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere! Tamverani, inu mayiko onse akutali. Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere! Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
10 Devise your plan, but it will come to nothing; speak your word, but it will not stand—for our Father is with us. Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu, kambiranani zochita, koma zidzalephereka, pakuti Mulungu ali nafe.
11 For this is what our Father told me, his strong hand on me, warning me not to walk this people's way: Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:
12 "Do not call conspiracy everything this people calls conspiracy; do not fear what they fear, and do not be terrified. “Usamanene kuti ndi chiwembu, chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu usamaope zimene anthuwa amaziopa, ndipo usamachite nazo mantha.
13 The Father of heaven's armies—he is the one you should regard as holy. Let him be your fear; let him be your dread. Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
14 He will become a sanctuary; but to both houses of Israel he will be a stone that makes them stumble and a rock that makes them fall, and to the inhabitants of Jerusalem a trap and a snare. ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika; koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala mwala wopunthwitsa, mwala umene umapunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
15 Many among them will stumble; they will fall and be broken, they will be snared and captured." Anthu ambiri adzapunthwapo adzagwa ndi kuthyokathyoka, adzakodwa ndi kugwidwa.”
16 Preserve the testimony; seal the teaching among my disciples. Manga umboniwu ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
17 I will wait for our Father, who is hiding his face from the house of Jacob; I will hope in him. Ndidzayembekezera Yehova, amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo. Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.
18 Here am I, and the children our Father gave me—signs and wonders in Israel from the Father of heaven's armies, who lives on Mount Zion. Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.
19 When they tell you, "Ask the mediums and those who consult spirits, who whisper and mutter," should a people not ask their Father? Should they consult the dead for the living? Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo,
20 To the teaching and the testimony! If they don't speak according to this word, they have no light of dawn. kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.
21 Distressed and hungry, they will roam the land; when famished, they will rage and curse their king and their Father, and look up. Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo.
22 They will look to the earth and see only distress and darkness, the gloom of anguish; and they will be driven into thick darkness. Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]