Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Woe to those who enact unjust decrees, to the writers who issue oppressive laws, Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,
2 to deprive the poor of justice and rob the needy among my people of their rights, making widows their plunder and orphans their prey. kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.
3 What will you do on the day of reckoning, when devastation comes from afar? To whom will you flee for help? Where will you leave your wealth? Kodi mudzatani pa tsiku la chilango, pofika chiwonongeko chochokera kutali? Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
4 Nothing remains but to crouch among the captives or fall among the slain. Yet for all this his anger has not turned away; his hand is still stretched out. Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
5 "Woe to Assyria, the rod of my anger, in whose hand is the club of my fury! “Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga, iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
6 I send him against a godless nation; against the people of my wrath I command him, to seize spoil and carry off plunder, to trample them down like mud in the streets." Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu, ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine, kukafunkha ndi kulanda chuma, ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
7 But this is not what he intends; this is not what his heart plans. His purpose is to destroy, to cut off nation after nation. Koma izi si zimene akufuna kukachita, izi si zimene zili mʼmaganizo mwake; cholinga chake ndi kukawononga, kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
8 For he says, "Are not all my commanders kings? Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
9 Is Calno not like Carchemish? Is Hamath not like Arpad? Is Samaria not like Damascus? ‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi, nanga Samariya sali ngati Damasiko?
10 As my hand seized the kingdoms of the idols, whose carved images surpassed those of Jerusalem and Samaria, Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano, mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;
11 will I not deal with Jerusalem and her images as I dealt with Samaria and her idols?" nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’ ”
12 When the Sovereign Father has finished all his work against Mount Zion and Jerusalem, I will punish the fruit of the king of Assyria's arrogant heart and the haughty pride of his eyes. Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake.
13 For he says: "By the strength of my hand I have done this, and by my wisdom, for I have understanding. I removed the boundaries of peoples and plundered their treasures; I brought down those enthroned like a mighty one. Pakuti mfumuyo ikuti, “ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa, ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu. Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu, ndinafunkha chuma chawo; ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
14 My hand reached into the wealth of the peoples as into a nest; as one gathers abandoned eggs, I gathered all the earth. Not one flapped a wing or opened its beak to chirp. Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame, ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse; palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake, kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”
15 Does the axe exalt itself over the one who swings it? Does the saw boast against the one who wields it? As if a rod could brandish the one who lifts it, as if a staff could lift what is not wood!" Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito, kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula, kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
16 Therefore the Sovereign Father, the Father of heaven's armies, will send a wasting disease among his sturdy warriors, and beneath his glory a fire will blaze like a burning flame. Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu; kunyada kwa mfumuyo kudzapsa ndi moto wosazima.
17 The Light of Israel will become a fire, our Holy One a flame; in a single day it will burn and consume his thorns and briers. Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto, Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto. Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
18 The glory of his forest and his fertile field our Father will destroy, both soul and body; it will be as when a sick man wastes away. Ankhondo ake adzawonongedwa ngati nkhalango yayikulu ndi ngati nthaka yachonde.
19 The remaining trees of his forest will be so few that a child could count them. Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.
20 In that day the remnant of Israel and the survivors of the house of Jacob will no longer lean on the one who struck them, but will truly lean on our Father, the Holy One of Israel. Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli, opulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzadaliranso anthu amene anawakantha, koma adzadalira Yehova, Woyerayo wa Israeli.
21 A remnant will return—a remnant of Jacob—to the Mighty God. Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.
22 Though your people Israel be like the sand of the sea, only a remnant will return. Destruction is decreed, overflowing with righteousness. Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
23 For the Sovereign Father, the Father of heaven's armies, will carry out the decreed destruction throughout the land. Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse monga momwe analamulira.
24 Therefore the Sovereign Father, the Father of heaven's armies, says: "My people who live in Zion, do not be afraid of Assyria, who strikes you with the rod and lifts the staff against you as Egypt did. Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musawaope Asiriya, amene amakukanthani ndi ndodo nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
25 For in a very little while my fury will end, and my anger will turn to their destruction." Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”
26 The Father of heaven's armies will brandish a whip against them, as when he struck Midian at the rock of Oreb; he will raise his staff over the sea as he did in Egypt. Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu, monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu; ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
27 In that day their burden will be lifted from your shoulder, their yoke from your neck; the yoke will be broken. Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu, goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu; golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa kwambiri.
28 He comes against Aiath, passes through Migron, stores his supplies at Michmash. Adani alowa mu Ayati apyola ku Migironi; asunga katundu wawo ku Mikimasi.
29 They cross the pass: "We will camp at Geba." Ramah trembles; Gibeah of Saul flees. Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti, “Tikagona ku Geba” Rama akunjenjemera; Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
30 Cry out, daughter of Gallim! Listen, Laishah! Poor Anathoth! Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu! Tchera khutu, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!
31 Madmenah is fleeing; the people of Gebim are taking cover. Anthu a ku Madimena akuthawa; anthu a ku Gebimu bisalani.
32 This very day he stops at Nob, shaking his fist at the mount of the daughter of Zion, the hill of Jerusalem. Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu; adzagwedeza mikono yawo, kuopseza anthu a ku Ziyoni, pa phiri la Yerusalemu.
33 Look, the Sovereign Father, the Father of heaven's armies, will lop off the branches with terrifying force; the tallest trees will be felled, the lofty ones brought low. Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo, mitengo yodzikweza idzadulidwa, mitengo yayitali idzagwetsedwa.
34 He will cut down the forest thickets with an axe, and Lebanon will fall before the Majestic One. Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira; Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]