Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Amos 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 This is what our Father says: For three sins of Moab, and for four, I will not revoke it—he burned the bones of Edom's king to lime. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu, mpaka kuwasandutsa phulusa,
2 So I will send fire on Moab, and it will devour the strongholds of Kerioth; Moab will die amid the uproar, with shouting and the sound of the shofar. Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti. Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa, mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.
3 I will cut off the ruler from her midst and kill all her officials with him, says our Father. Ndidzawononga wolamulira wake ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,” akutero Yehova.
4 This is what our Father says: For three sins of Judah, and for four, I will not revoke it—they rejected our Father's instruction and did not keep his rules, and their lies led them astray, the same lies their ancestors followed. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo akana lamulo la Yehova ndipo sanasunge malangizo ake, popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza, milungu imene makolo awo ankayitsatira,
5 So I will send fire on Judah, and it will devour the strongholds of Jerusalem. Ine ndidzatumiza moto pa Yuda, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”
6 This is what our Father says: For three sins of Israel, and four, I won't relent—they sell the righteous for silver, the needy for a pair of sandals. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva, ndi osauka ndi nsapato.
7 They trample the heads of the poor into the dust of the earth and push the afflicted off the road. A man and his father go to the same girl, profaning my holy name. Amapondereza anthu osauka ngati akuponda fumbi, ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa. Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo, ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
8 They stretch out beside every altar on garments taken as collateral, and in the house of their God they drink the wine of those they have fined. Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe pa zovala zimene anatenga ngati chikole. Mʼnyumba ya mulungu wawo amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.
9 Yet it was I who destroyed the Amorite before them, as tall as the cedars and as strong as the oaks; I destroyed his fruit above and his roots below. “Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo, ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu. Ndinawononga zipatso zawo ndiponso mizu yawo.
10 And it was I who brought you up out of the land of Egypt and led you forty years in the wilderness, to take possession of the land of the Amorite. “Ine ndinakutulutsani ku Igupto, ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kudzakupatsani dziko la Aamori.
11 I raised up some of your sons as prophets and some of your young men as Nazirites. Is this not so, people of Israel? declares our Father. Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri, ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri. Kodi si choncho, inu Aisraeli?” akutero Yehova.
12 But you made the Nazirites drink wine, and you commanded the prophets, saying, "Do not prophesy." “Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja, ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.
13 Look, I will crush you in your place, as a cart full of sheaves crushes the ground beneath it. “Tsono Ine ndidzakupsinjani monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.
14 Even the swift will find no escape, the strong will not hold on to his strength, and the warrior will not save his life. Munthu waliwiro sadzatha kuthawa, munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga, wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15 The archer will not stand his ground, the fleet-footed will not escape, and the horseman will not save his life. Munthu wa uta sadzalimbika, msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka, ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16 Even the bravest of the warriors will flee away naked on that day, declares our Father. Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri adzathawa ali maliseche pa tsikulo,” akutero Yehova.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]