Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Numbers 13 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Our Father said to Moses, Yehova anawuza Mose kuti,
2 "send men to scout the land of Canaan, which I'm giving Israel's people. Send one man per ancestral tribe, each a leader among them." “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.”
3 So Moses sent them from the wilderness of Paran at our Father's command; all were leaders of Israel's people. Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli.
4 These were their names: from the tribe of Reuben, Shammua the son of Zaccur; Mayina awo ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri;
5 from the tribe of Simeon, Shaphat the son of Hori; kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori;
6 from the tribe of Judah, Caleb the son of Jephunneh; kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune;
7 from the tribe of Issachar, Igal the son of Joseph; kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe;
8 from the tribe of Ephraim, Hoshea the son of Nun; kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni;
9 from the tribe of Benjamin, Palti the son of Raphu; kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu;
10 from the tribe of Zebulun, Gaddiel the son of Sodi; kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi;
11 from the tribe of Joseph (that is, from the tribe of Manasseh), Gaddi the son of Susi; kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi;
12 from the tribe of Dan, Ammiel the son of Gemalli; kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali;
13 from the tribe of Asher, Sethur the son of Michael; kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli;
14 from the tribe of Naphtali, Nahbi the son of Vophsi; kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi;
15 from the tribe of Gad, Geuel the son of Machi. kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki.
16 These are the names of the men Moses sent to scout the land. Moses named Hoshea son of Nun, Joshua. Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa).
17 Moses sent them to scout the land of Canaan and said to them, "Go up this way into the Negev, go up into the hill country, Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri.
18 and see what the land is like, and whether the people living there are strong or weak, few or many, Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri.
19 and whether the towns they live in are open camps or fortified, and whether the land is good or bad, Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga?
20 and whether the land is rich or poor, and whether it has trees or not. Be brave, and bring back fruit from the land." It was the season of the first ripe grapes. Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa).
21 So they went up and explored the land from the wilderness of Zin to Rehob, near Lebo-hamath. Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati.
22 They went up through the Negev to Hebron, where Ahiman, Sheshai, and Talmai, Anak's descendants, lived. Hebron was built seven years before Zoan in Egypt. Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto).
23 They reached the Valley of Eshcol and cut a branch with one cluster of grapes, carried on a pole between two men; they also brought pomegranates and figs. Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu.
24 That place was named Valley of Eshcol, since the Israelites cut a cluster of grapes there. Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko.
25 At the end of forty days they returned from exploring the land. Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija.
26 They came to Moses, Aaron, and the whole community of Israel in the wilderness of Paran, at Kadesh, reported back to them and the whole community, and showed them the land's fruit. Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo.
27 They told him, "We went to the land you sent us to. It truly flows with milk and honey; here is its fruit. Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi.
28 Yet the people in the land are strong, the cities fortified and very large—we even saw Anak's descendants there. Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko.
29 Amalekites live in the Negev. Hittites, Jebusites, and Amorites live in the hills. Canaanites live along the sea and beside the Jordan." Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.”
30 Caleb silenced the people before Moses and said, "Let's go up now and possess it—we can certainly overcome it." Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.”
31 But the men who went up with him said, "We can't go up against the people, for they are stronger than we are." Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.”
32 So they gave Israel a bad report of the land they had explored, saying, "The land we crossed to explore devours its inhabitants, and everyone we saw there is of great size. Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali.
33 There we saw the Nephilim—Anak's descendants come from the Nephilim. We seemed like grasshoppers to ourselves, and so we seemed to them." Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]