Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Micah 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 The word of our Father to Micah of Moresheth in the days of Jotham, Ahaz, and Hezekiah, kings of Judah—what he saw about Samaria and Jerusalem. Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.
2 Hear, all you peoples; listen, earth, and all that fills it—let the Sovereign Father be a witness against you, the Sovereign Father from his holy temple. Tamverani, inu anthu a mitundu yonse, mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo, pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani, Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.
3 For look—our Father is coming out from his place; he will come down and tread on the high places of the earth. Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake; Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.
4 The mountains will melt beneath him, and the valleys will split apart, like wax before the fire, like waters poured down a steep slope. Mapiri akusungunuka pansi pake, ndipo zigwa zikugawikana ngati phula pa moto, ngati madzi ochokera mʼphiri.
5 All this is because Jacob rebelled and the house of Israel sinned. What is Jacob's rebellion? Isn't it Samaria? And what is Judah's high place? Isn't it Jerusalem? Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo, chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli. Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani? Kodi si Samariya? Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati? Kodi si Yerusalemu?
6 So I will make Samaria a heap of ruins in the open field, a place for planting vineyards. I will pour her stones down into the valley and lay bare her foundations. “Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja, malo odzalamo mphesa. Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa ndipo ndidzafukula maziko ake.
7 All her carved images will be shattered, all her wages burned in the fire; all her idols I will lay waste. For from a prostitute's wages she gathered them, and to a prostitute's wages they will return. Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya; mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto; ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake. Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere, mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”
8 Because of this I will lament and wail; I will go stripped and naked. I will howl like jackals and moan like ostriches. Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni; ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche. Ndidzafuwula ngati nkhandwe ndi kulira ngati kadzidzi.
9 For her wound is incurable; it has come all the way to Judah. It has reached the gate of my people, all the way to Jerusalem. Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika; chafika ku Yuda. Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga, mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.
10 Do not tell it in Gath; do not weep at all. In Beth-le-aphrah roll yourselves in the dust. Musanene zimenezi ku Gati; musalire nʼkomwe. Mugubuduzike mu fumbi ku Beti-Leafura.
11 Pass on your way, you who live in Shaphir, in nakedness and shame. Those who live in Zaanan do not come out; the wailing of Beth-ezel leaves you with no place to stand. Inu anthu okhala ku Safiro, muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi. Iwo amene akukhala ku Zanaani sadzatuluka. Beti-Ezeli akulira mwachisoni; chitetezo chake chakuchokerani.
12 For those who live in Maroth wait anxiously for good, because disaster has come down from our Father to the gate of Jerusalem. Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu, akuyembekezera thandizo, chifukwa Yehova wabweretsa tsoka, lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
13 Harness the horses to the chariot, you who live in Lachish. She was the beginning of sin to the daughter of Zion, for in you the rebellions of Israel were found. Inu anthu okhala ku Lakisi mangani akavalo ku magaleta. Inu amene munayamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti zolakwa za Israeli zinapezeka pakati panu.
14 Therefore you will give parting gifts to Moresheth-gath; the houses of Achzib will be a deception to the kings of Israel. Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana ndi a ku Moreseti Gati. Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama kwa mafumu a Israeli.
15 Once more I will bring a conqueror against you, you who live in Mareshah; the glory of Israel will come to Adullam. Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu okhala mu Maresa. Ulemerero wa Israeli udzafika ku Adulamu.
16 Shave your head and cut off your hair for the children you love; make yourself as bald as the eagle, for they will go from you into exile. Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira ana anu amene mumawakonda; mudzichititse dazi ngati dembo, pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]