Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 24 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 On the first day of the week, at dawn, they came to the tomb, carrying the spices they had prepared. Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda.
2 They found the stone rolled away from the tomb, Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika
3 but when they went in they did not find the body of the Lord Jesus. ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu.
4 While they were perplexed about this, suddenly two men stood beside them in dazzling clothes. Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo.
5 Frightened, they bowed their faces to the ground. The men asked, "Why seek the living among the dead? Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa?
6 He's not here—he's risen. Remember what he told you while still in Galilee, Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya:
7 that the Son of Man must be handed over to sinful men, be crucified, and rise on the third day." ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ”
8 And they remembered his words, Ndipo anakumbukira mawu ake.
9 returning from the tomb, they told all this to the eleven and all the rest. Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse.
10 Mary Magdalene, Joanna, Mary the mother of James, and the other women with them told these things to the apostles. Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi.
11 But these words seemed like nonsense to them, and they did not believe them. Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru.
12 Peter got up and ran to the tomb; bending down, he saw only the linen cloths, then went home amazed at what had happened. Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
13 That same day two of them traveled to a village called Emmaus, about seven miles from Jerusalem, Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu.
14 and they were talking with each other about all these things that had happened. Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo.
15 While they were talking and discussing together, Jesus himself drew near and went with them. Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi;
16 But their eyes were kept from recognizing him. koma iwo sanamuzindikire.
17 He asked them, "What are you discussing with each other as you walk?" They stopped, looking sad. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?” Iwo anayima ndi nkhope zakugwa.
18 One of them, Cleopas, replied, "Are you the only visitor to Jerusalem who does not know what has happened there these days?" Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?”
19 He asked, "What things?" They said, "About Jesus of Nazareth—a prophet powerful in deed and word before our Father and all the people, Iye anafunsa kuti, “Zinthu zotani?” Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
20 and how our chief priests and rulers handed him over to a death sentence, and crucified him. Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye;
21 We'd hoped he was the one to redeem Israel. Yet on top of all this, it's the third day since these things happened. koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi.
22 Some women of ours also amazed us—early at the tomb, Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa
23 and not finding his body, they came back saying they'd even seen a vision of angels, who said he was alive. koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo.
24 Some of our companions went to the tomb and found it just as the women said, but they did not see him." Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.”
25 He said to them, "How foolish you are, and slow to believe all the prophets said! Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena!
26 Was it not necessary that the Christ should suffer these things and enter into his glory?" Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?”
27 And beginning with Moses and all the Prophets, he explained to them from all the Scriptures everything about himself. Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
28 And they approached the village they were heading to, and he pretended to go farther. Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira.
29 But they insisted, "Stay with us—evening is near, the day nearly done." So he went in to stay with them. Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
30 As he reclined with them, he took the bread, blessed it, broke it, and gave it to them. Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira.
31 And their eyes were opened, and they recognized him. And he vanished from their sight. Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo.
32 They said to each other, "Weren't our hearts burning within us as he spoke to us on the road, as he opened the Scriptures to us?" Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”
33 That same hour they got up, returned to Jerusalem, and found the eleven and those with them gathered together, Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi
34 saying, "The Lord has risen indeed, and has appeared to Simon!" ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.”
35 And they told what happened on the road, and how he was recognized in the breaking of the bread. Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.
36 As they spoke these things, Jesus himself stood among them and said to them, "Peace to you!" Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.”
37 But they were startled and frightened and thought they saw a spirit. Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa.
38 And he said to them, "Why are you troubled, and why do doubts arise in your hearts? Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu?
39 Look at my hands and my feet—it's really me. Touch me and see: a spirit has no flesh and bones, as you see I have." Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”
40 And when he had said this, he showed them his hands and his feet. Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake.
41 And while they still disbelieved for joy and were marveling, he said to them, "Do you have anything here to eat?" Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”
42 They gave him a piece of broiled fish, Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika.
43 and he took it and ate before them. Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.
44 He said to them, "This is what I told you while still with you: everything written about me in the Law of Moses, the Prophets, and the Psalms had to be fulfilled." Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”
45 Then he opened their minds to understand the Scriptures, Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba.
46 and told them, "This is written: the Christ must suffer and rise from the dead on the third day, Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu.
47 and that repentance for the forgiveness of sins should be proclaimed in his name to all nations, beginning from Jerusalem. Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.
48 You are witnesses of these things. Inu ndinu mboni za zimenezi.
49 I am sending the promise of my Father on you. Stay in the city until you are dressed with power from on high." Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”
50 And he led them out as far as Bethany, and lifting up his hands he blessed them. Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa.
51 While he blessed them, he parted from them and was carried up into heaven. Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba.
52 And they worshiped him and returned to Jerusalem with great joy, Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.
53 and were continually in the temple blessing our Father. Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]