Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 23 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then the whole assembly rose and brought him before Pilate. Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato.
2 They began accusing him: "We found this man misleading our nation, forbidding taxes to Caesar, and claiming to be Christ, a king." Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
3 Pilate asked him, "Are you the King of the Jews?" He answered, "You say so." Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
4 Then Pilate said to the chief priests and the crowds, "I find no guilt in this man." Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”
5 But they pressed on: "He stirs up the people, teaching all through Judea, from Galilee to here." Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”
6 When Pilate heard this, he asked whether the man was a Galilean. Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya.
7 Learning he was under Herod's authority, he sent him to Herod, who himself was also in Jerusalem in those days. Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.
8 Seeing Jesus, Herod was delighted—he'd long wanted to see him, having heard about him, and hoped to see him perform a sign. Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa.
9 He questioned him at great length, but Jesus gave him no answer. Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe.
10 The chief priests and the scribes stood by, vehemently accusing him. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri.
11 Herod and his soldiers scorned and mocked him, dressed him in bright clothing, and sent him back to Pilate. Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato.
12 That day Herod and Pilate became friends—they had been enemies before. Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.
13 Pilate then called together the chief priests, the rulers, and the people, Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu,
14 and said to them, "You brought me this man as one turning the people away. I examined him before you and found no guilt in this man on your charges. ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu.
15 Neither did Herod, for he sent him back to us. Look, he has done nothing deserving death. Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe.
16 I will therefore discipline him and release him." Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.”
17 Not in this edition (Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).
18 But they all cried out together, "Away with this man! Release Barabbas to us!" Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!”
19 a man imprisoned for a rebellion that happened in the city, and for murder. (Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).
20 Pilate addressed them once more, wanting to release Jesus, Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo.
21 but they kept shouting, "Crucify, crucify him!" Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22 A third time he said to them, "Why? What wrong has this man done? I find no ground for death in him. So I will punish and release him." Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
23 But they kept shouting loudly, demanding he be crucified, and their voices prevailed. Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira.
24 So Pilate decided that their demand should be granted. Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo.
25 He released the man they asked for, jailed for rebellion and murder, but handed Jesus over to their will. Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.
26 Leading him away, they seized a man named Simon of Cyrene, coming in from the countryside, and put the cross on him to carry behind Jesus. Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu.
27 A great crowd of the people followed him, including women who were weeping and wailing for him. Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira.
28 But Jesus turned to them and said, "Daughters of Jerusalem, don't cry for me; cry for yourselves and your children. Yesu anatembenuka nati kwa iwo, “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu.
29 For the days are coming when they will say, 'Blessed are the barren, the wombs that never bore, the breasts that never nursed.' Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’
30 Then they'll begin saying to the mountains, "Fall on us," and to the hills, "Cover us." Kenaka, “adzawuza mapiri kuti tigwereni ife; zitunda kuti tiphimbeni ife.
31 For if they do this when the wood is green, what will happen when it's dry?" Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”
32 Two others, who were criminals, were also led away to be put to death with him. Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa.
33 When they reached the place called The Skull, they crucified him there with the criminals, one on his right, one on his left. Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere.
34 Jesus said, "Father, forgive them, for they do not know what they are doing." Then they divided his garments, casting lots. Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35 The people stood watching; the rulers sneered, "He saved others—let him save himself, if he's God's Christ, the Chosen One." Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
36 The soldiers also mocked him, coming up to offer him sour wine, Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa,
37 and saying, "If you are the King of the Jews, save yourself!" ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38 There was also an inscription over him: "This is the King of the Jews." Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39 One of the hanged criminals insulted him: "Aren't you the Christ? Save yourself and us!" Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”
40 But the other rebuked him: "Don't you even fear God, since you're under the same sentence? Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi?
41 Rightly so—we're paying for what we did; but this man has done nothing wrong." Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”
42 Then he said, "Jesus, remember me when you come into your kingdom." Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”
43 And Jesus said to him, "Truly I tell you, today you will be with me in Paradise." Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”
44 It was already about noon, and darkness covered the whole land until three in the afternoon, Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi,
45 for the sun's light failed; and the curtain of the temple was torn in two. pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati.
46 Jesus called out loudly, "Father, into your hands I commit my spirit!" Then he breathed his last. Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.
47 Seeing what happened, the centurion praised our Father: "This man really was righteous." Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.”
48 All the crowds gathered for this sight, seeing what happened, went home beating their chests. Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka.
49 All his acquaintances, and the women who followed him from Galilee, stood far off watching these things. Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.
50 Now there was a man named Joseph, a member of the council, a good and righteous man, Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama.
51 who had not agreed to their plan and action. He was from Arimathea, a Jewish town, and was waiting for the kingdom of our Father. Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu.
52 This man went to Pilate and asked for the body of Jesus. Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu.
53 He took it down, wrapped it in a linen cloth, and laid him in a rock-cut tomb where no one had yet been laid. Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo.
54 It was the day of Preparation, and the Sabbath was about to begin. Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.
55 Women who came with him from Galilee followed, saw the tomb, and how his body was placed. Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira.
56 They went back and prepared spices and ointments, then rested on the Sabbath as commanded. Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]