Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 22 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Now the Feast of Bread Without Yeast, called Passover, was approaching. Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira,
2 The chief priests and the scribes were looking for a way to kill him, because they feared the people. akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu.
3 Then Satan entered into Judas, the one called Iscariot, who was one of the twelve. Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo.
4 He went and conferred with the chief priests and temple officers how he might betray him to them. Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu.
5 They were glad and agreed to give him money. Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama.
6 He agreed and began looking for an opportunity to betray him to them away from the crowd. Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.
7 Then the day of Unleavened Bread arrived, when the Passover lamb had to be sacrificed. Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe.
8 Jesus sent Peter and John, saying, "Go prepare the Passover for us to eat." Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”
9 They said to him, "Where do you want us to prepare it?" Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?”
10 He said, "Once you enter the city, a man carrying a jar of water will meet you. Follow him into the house he enters, Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe,
11 "and tell the owner of the house, 'The Teacher says to you: Where is the guest room where I may eat the Passover with my disciples?' ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’
12 And he will show you a large upper room, furnished; prepare it there." Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”
13 They went and found it just as he had told them, and they prepared the Passover. Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska.
14 When the hour came, he reclined at table, and the apostles with him. Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo.
15 He told them, "I have deeply longed to eat this Passover with you before I suffer. Ndipo Iye anawawuza kuti, “Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa.
16 For I tell you, I won't eat it until it's fulfilled in the kingdom of our Father." Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”
17 Taking a cup and giving thanks, he said, "Take this and divide it among yourselves. Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati, “Tengani ndipo patsiranani pakati panu.
18 For I tell you, from now on I will not drink the vine's fruit until our Father's kingdom comes." Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”
19 He took bread, gave thanks, broke it, and gave it to them, saying, "This is my body, given for you. Do this in memory of me." Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
20 He did the same with the cup after supper: "This cup is the new covenant in my blood, poured out for you. Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu.
21 But look—the hand of the one who betrays me is with me on the table. Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano.
22 The Son of Man goes as determined, but woe to that man through whom he is handed over!" Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.”
23 They began asking each other which of them would do this. Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi.
24 A dispute also arose among them about which of them was the greatest. Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu.
25 He said to them, "Kings of nations dominate them, and rulers over them are called benefactors. Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’
26 Not so with you: let the greatest among you become like the youngest, the leader like the one serving. Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira.
27 Who is greater—the guest at the table or the one serving? The guest, isn't it? Yet I am among you as one who serves. Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.
28 "You are those who have stayed with me in my trials, Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero.
29 and I confer on you a kingdom, just as my Father conferred one on me, Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine,
30 so you'll eat and drink at my table in my kingdom, and sit on thrones judging the twelve tribes of Israel." kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”
31 "Simon, Simon, listen—Satan has demanded to sift all of you like wheat, “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu.
32 but I prayed for you, that your faith not fail. Once you have turned back, strengthen your brothers." Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”
33 Peter said, "Lord, I'm ready to go with you to prison and death." Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”
34 Jesus said, "I tell you, Peter: the rooster won't crow today before you deny three times that you know me." Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”
35 He asked, "When I sent you without money bag, knapsack, or sandals, did you lack anything?" "Nothing," they said. Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?” Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.”
36 He said to them, "But now, let the one with a money bag take it, and a knapsack too. Let the one without a sword sell his cloak and buy one. Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula.
37 For I tell you this Scripture must be fulfilled in me: 'He was counted among sinners.' For what is written about me is coming true." Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”
38 They said, "Lord, look, here are two swords." He said to them, "It is enough." Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.” Iye anayankha kuti, “Amenewa akwanira.”
39 And he went out, as usual, to the Mount of Olives, and the disciples followed him. Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye.
40 When he reached the place, he told them, "Pray you don't give in to temptation." Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.”
41 And he withdrew from them about a stone's throw, and knelt down and prayed, Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti,
42 saying, "Father, if you are willing, take this cup from me. Yet not my will, but yours, be done." “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.”
43 And an angel from heaven appeared to him, strengthening him. Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa.
44 In agony he prayed more intensely; his sweat became like great drops of blood falling down to the ground. Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi.
45 When he rose from prayer, he came to the disciples and found them asleep from grief, Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni.
46 he said to them, "Why are you sleeping? Get up and pray, so you don't yield to temptation." Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”
47 While he was still speaking, a crowd came, led by the one called Judas, one of the twelve. He came up to Jesus to kiss him, Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone.
48 but Jesus said to him, "Judas, would you betray the Son of Man with a kiss?" Koma Yesu anamufunsa kuti, “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”
49 Seeing what was about to happen, those with him said, "Lord, should we strike with the sword?" Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?”
50 And one of them struck the servant of the high priest and cut off his right ear. Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.
51 But Jesus answered, "No more of this!" And he touched the ear and healed him. Koma Yesu anayankha kuti, “Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.
52 Then Jesus said to the chief priests, temple officers, and elders who had come out against him, "Have you come out with swords and clubs, as against a robber? Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga?
53 Every day I was with you in the temple, and you didn't lay hands on me. But this is your hour, and the authority of darkness." Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”
54 Seizing him, they led him and brought him into the high priest's house; Peter followed at a distance. Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali.
55 They lit a fire in the middle of the courtyard and sat together; Peter sat among them. Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi.
56 But a servant girl, seeing him sitting facing the light, stared at him and said, "This one too was with him." Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
57 But he denied it, saying, "Woman, I do not know him." Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”
58 Shortly after, another saw him and said, "You too are one of them." But Peter said, "Man, I'm not." Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.” Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”
59 About an hour later, another insisted, "This man was certainly with him, for he's a Galilean too." Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”
60 But Peter said, "Man, I don't know what you're saying." Immediately, while he was still speaking, the rooster crowed. Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira.
61 The Lord turned and looked at Peter. Peter remembered what the Lord had told him: "Before the rooster crows today, you will deny me three times." Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.”
62 And he went out and wept bitterly. Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.
63 Now the men who were holding Jesus mocked him as they beat him. Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya.
64 They blindfolded him and kept asking, "Prophesy! Who is it that struck you?" Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?”
65 And they said many other things against him, insulting him. Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri.
66 At daybreak, the people's council of elders convened—chief priests and scribes—and led him away to their council, saying, Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo.
67 "If you are the Christ, tell us." He said to them, "If I tell you, you will not believe, Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.” Yesu anayankha kuti, “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire.
68 "and if I ask you, you will not answer. Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe.
69 "But from now on the Son of Man will sit at the right hand of the power of our Father." Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”
70 They all said, "So you are the Son of God?" He said to them, "You say that I am." Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.”
71 They said, "What more testimony do we need? For we heard it ourselves from his mouth." Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]