Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 21 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Looking up, Jesus saw the rich putting their gifts into the temple treasury. Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu.
2 He also saw a poor widow putting in two small copper coins. Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri.
3 "Truly I tell you," he said, "this poor widow has put in more than all the others. Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa.
4 For all these gave gifts from their surplus, but she gave from her poverty all she had to live on." Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”
5 As some were speaking of the temple, decorated with fine stones and gifts dedicated to our Father, he said: Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati,
6 "As for what you're looking at, days are coming when not one stone will be left on another—every one will be thrown down." “Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
7 "Teacher," they asked, "when will these things happen, and what sign will show these things are about to happen?" Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”
8 "Watch out, don't be deceived," he said. "Many will come in my name, saying, 'I am he,' and, 'The time is near.' Don't follow them. Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo.
9 When you hear of wars and revolts, don't panic. These must come first, but the end won't follow at once." Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”
10 Then he said to them, "Nation will rise against nation, and kingdom against kingdom. Kenaka anawawuza kuti, “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina.
11 Great earthquakes will strike, with famines and plagues in various places, and terrors and great signs from heaven. Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.
12 But before all this, they'll grab you and persecute you, handing you over to synagogues and prisons, hauling you before kings and governors because of my name. “Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa.
13 This will be your opportunity to bear witness. Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni.
14 So settle in your hearts not to prepare your defense beforehand, Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire.
15 for I will give you words and wisdom no opponent can resist or refute. Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa.
16 You will be betrayed even by parents and brothers and relatives and friends, and they will kill some of you. Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani.
17 You will be hated by everyone for my name's sake. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine.
18 But not a hair of your head will perish. Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke.
19 By your endurance you will gain your lives." Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.
20 "When you see Jerusalem surrounded by armies, then know that its desolation has drawn near. “Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi.
21 Then let those in Judea flee to the mountains, let those in the city leave, and let those in the countryside not enter it, Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda.
22 for these are days of judgment, when all that is written will be fulfilled. Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa.
23 How terrible it will be for pregnant women and nursing mothers in those days! For great distress will fall on the land, and wrath against this people. Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira.
24 They will fall by the edge of the sword and be led captive into all nations. Jerusalem will be trampled by the nations until the times of the nations are fulfilled." Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.
25 "There will be signs in sun, moon, and stars, and on earth, nations in distress, confused by the sea's roar and surge. “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja.
26 People fainting from fear, dreading what's coming on the world, for the powers of the heavens will be shaken. Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka.
27 Then they will see the Son of Man coming in a cloud with power and great glory. Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.
28 When these things start, straighten up and lift your heads, for your redemption is near." Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”
29 Then he told them a parable: "Look at the fig tree and all the trees. Iye anawawuza fanizo ili, “Taonani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse.
30 When they sprout leaves, you see for yourselves and know summer is already near. Ikamatulutsa masamba, mumakhoza kudzionera nokha ndi kudziwa kuti dzinja lili pafupi.
31 Likewise, when you see these things happen, know the kingdom of our Father is near. Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.
32 Truly I tell you, this generation will not pass away until all these things have taken place. “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika.
33 Heaven and earth will pass away, but my words will never pass away." Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
34 "Watch yourselves, or your hearts will be weighed down by wild living, drunkenness, and life's worries, and that day will spring on you suddenly, like a trap. “Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha.
35 For it will come upon everyone living on the face of the whole earth. Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi.
36 Keep watch at all times, praying for strength to escape everything about to happen, and to stand before the Son of Man." Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”
37 By day he taught in the temple; at night he went out and stayed on the Mount of Olives. Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse.
38 All the people would come to him at dawn in the temple to hear him. Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]