Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 20 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 One of those days, as Jesus taught the people in the temple and preached good news, the chief priests and scribes came up with the elders, Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
2 and asked him, "Tell us by what authority you do these things, or who gave you this authority." Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?”
3 He answered them, "I also will ask you a question. Tell me: Iye anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe,
4 Was the baptism of John from heaven, or from man?" ‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’ ”
5 They discussed among themselves: "If we say, 'From heaven,' he'll say, 'Why didn't you believe him?' Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’
6 But if we say 'From man,' all the people will stone us, for they're convinced John was a prophet." Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.”
7 So they answered that they did not know where it came from. Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.”
8 And Jesus said to them, "Neither will I tell you by what authority I do these things." Yesu anati, “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”
9 He began telling the people this parable: A man planted a vineyard, leased it to tenants, then went abroad for a long time. Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali.
10 "At harvest he sent a servant to the tenant farmers for his share of the vineyard's fruit, but they beat him and sent him away empty-handed. Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu.
11 He sent another servant; they beat him too, humiliated him, and sent him away empty-handed. Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu.
12 And he sent yet a third, but they wounded this one too and threw him out. Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.
13 The vineyard owner said, 'What should I do? I will send my beloved son; perhaps they will respect him.' “Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’
14 But seeing him, the tenants reasoned among themselves: 'This is the heir. Let's kill him, so the inheritance becomes ours.' “Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’
15 They threw him out of the vineyard and killed him. What then will the vineyard owner do to them? Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha. “Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa?
16 "He will come, destroy those tenants, and give the vineyard to others." Hearing this, they said, "Impossible!" Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.” Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.”
17 He looked straight at them and asked, "Then what is this that's written: 'The stone the builders rejected became the cornerstone'? Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti, “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana wasanduka mwala wa pa ngodya.
18 Everyone who falls on that stone will be broken to pieces, and when it falls on anyone, it will crush him." Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’ ”
19 The scribes and chief priests wanted to arrest him then and there, knowing he'd told this parable against them—but they feared the people. Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.
20 Watching closely, they sent spies pretending to be honest, to catch him in his words, so as to hand him over to the governor's rule and authority. Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza.
21 They asked him, "Teacher, we know you speak and teach rightly, favor no one, but truly teach God's way. Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi.
22 Is it lawful for us to pay taxes to Caesar, or not?" Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?”
23 But he saw through their cunning and said, Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti,
24 "Show me a coin worth a day's wages. Whose image and inscription is on it?" They said, "Caesar's." “Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”
25 He said to them, "Then give Caesar what's Caesar's, and our Father what's our Father's." Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”
26 They could not trap him in his words before the people, and amazed at his answer, they fell silent. Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.
27 Some Sadducees, who deny there is a resurrection, came and asked him, Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso.
28 "Teacher, Moses wrote for us: if a man dies leaving a wife but no children, his brother must marry the widow and raise offspring for him. Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
29 Now there were seven brothers. The first took a wife and died childless. Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana.
30 And the second, Wachiwiri
31 and the third took her, and likewise all seven left no children and died. ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana.
32 Finally the woman also died. Pa mapeto pake mkaziyo anafanso.
33 At the resurrection, then, whose wife will she be? For all seven had married her." Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?”
34 And Jesus said to them, "The people of this age marry and are given in marriage, Yesu anayankha kuti, “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa.
35 "But those considered worthy to reach that age and the resurrection from the dead neither marry nor are given in marriage. Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.
36 For they can no longer die, because they are like angels and children of our Father, children of the resurrection. Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.
37 But even Moses showed the dead are raised, at the bush passage, calling our Father the God of Abraham and of Isaac and of Jacob. Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’
38 He isn't God of the dead but of the living, for all are alive to him." Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”
39 Then some of the scribes answered, "Teacher, you have spoken well." Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!”
40 For they no longer dared to ask him anything. Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena.
41 But he said to them, "How can they say that the Christ is the son of David? Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide?
42 For David himself says in the Psalms, 'Our Father said to my Lord, "Sit at my right hand, Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti, “Ambuye anati kwa Ambuye anga: ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,
43 until I make your enemies a footstool for your feet."' mpaka Ine nditasandutsa adani anu chopondapo mapazi anu?’
44 David then calls him Lord—how is he his son?" Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”
45 While all the people were listening, he said to his disciples, Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake,
46 "Watch out for the scribes, who want to walk in long robes, and love greetings in the marketplaces, the best seats in synagogues, and places of honor at feasts, “Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando.
47 who devour widows' houses and pray long prayers for show. They will receive greater condemnation." Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]