Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 19 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Jesus entered Jericho and was passing through. Yesu analowa mu Yeriko napitirira.
2 And there was a man named Zacchaeus; he was a chief tax collector, and he was rich. Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera.
3 He wanted to see who Jesus was, but couldn't for the crowd—he was short. Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu.
4 He ran ahead and climbed a sycamore tree to see him, since Jesus was about to pass that way. Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.
5 When Jesus reached the spot, looked up, and said to him, "Zacchaeus, hurry down, for I must stay at your house today." Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.”
6 So he hurried down and welcomed him joyfully. Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.
7 Seeing this, everyone grumbled, "He's gone to stay with a sinful man." Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”
8 Zacchaeus stood and said to the Lord, "Look, Lord, I give half my possessions to the poor, and if I've cheated anyone, I'll repay four times as much." Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”
9 Jesus told him, "Today salvation has come to this house, since he too is a son of Abraham. Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu.
10 For the Son of Man came to seek and to save the lost." Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”
11 While they listened, he added a parable, since he was near Jerusalem and they thought our Father's kingdom would appear immediately. Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo.
12 So he said, "A nobleman went to a distant land to receive a kingdom for himself and return. Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo.
13 Calling ten of his servants, he gave each about three months' wages, saying, "Trade with this until I return." Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’
14 His citizens hated him and sent envoys after him, saying, "We don't want this man ruling over us." “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’
15 "Returning after receiving the kingdom, he called the servants he had given money to, to learn what they had earned. “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.
16 The first came, saying, 'Lord, your money has earned ten times as much.'" “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’
17 "He replied, 'Well done, good servant! Since you were faithful in a small matter, take charge of ten cities.'" “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’
18 "And the second came, saying, 'Lord, the money you gave me has earned five times as much.'" “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’
19 "And he said to him, 'And you will be in charge of five cities.'" “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’
20 "Then another came, saying, 'Lord, here is your money back, which I kept wrapped in a cloth;' “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu.
21 for I was afraid of you, because you're a harsh man: you take what you didn't deposit and reap what you didn't sow." Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’
22 He answered, "By your own mouth I judge you, wicked servant! You knew I'm a harsh man, taking what I didn't deposit and reaping what I didn't sow? “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale?
23 Why then didn't you put my money in the bank? I'd have collected it with interest when I returned. Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’
24 He said to those standing by, 'Take the money from him and give it to the one with ten times as much.'" “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”
25 "And they said to him, 'Lord, he has ten times as much! Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”
26 I tell you: everyone who has will be given more; but from the one who has none, even what he has will be taken. Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.
27 But bring here these enemies of mine who refused my rule, and slaughter them before me.'" Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”
28 And when he had said these things, he went on ahead, going up to Jerusalem. Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu.
29 Nearing Bethphage and Bethany, at the Mount of Olives, he sent two of the disciples, Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo,
30 saying, "Go into the village ahead. As you enter, you will find a colt tied there, never sat on. Untie it and bring it here. “Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno.
31 If anyone asks you, 'Why are you untying it?' say, 'The Lord needs it.'" Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ ”
32 So those who were sent went away and found it just as he had told them. Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira.
33 As they were untying the colt, its owners said to them, "Why are you untying the colt?" Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?”
34 And they said, "The Lord needs it." Iwo anayankha kuti, “Ambuye akumufuna.”
35 They brought it to Jesus, threw their cloaks on the colt, and set Jesus on it. Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu.
36 And as he rode along, they spread their cloaks on the road. Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu.
37 As he neared the descent of the Mount of Olives, the whole crowd of disciples began rejoicing, praising our Father loudly for all the mighty works they had seen, Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.
38 saying, "Blessed is the King who comes in the name of our Father! Peace in heaven and glory in the highest!" “Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!” “Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!”
39 And some of the Pharisees in the crowd said to him, "Teacher, rebuke your disciples." Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!”
40 He answered, "I tell you, if these were silent, the very stones would cry out." Iye anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula.”
41 And when he drew near and saw the city, he wept over it, Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira
42 saying, "If only you had known today what brings you peace! But now it is hidden from your eyes. nati, “Iwe ukanadziwa lero lino zinthu zokubweretsera mtendere, koma tsopano zabisikira maso ako.
43 Days are coming when your enemies will build a barricade around you, surround you, and hem you in on every side, Pakuti masiku adzabwera pamene adani ako adzamanga mitumbira yankhondo nakuzungulira, nadzakutsekereza mbali zonse.
44 and they will level you and your children within your walls, leaving no stone on another, because you did not recognize the time of your visitation." Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”
45 And he entered the temple and began to drive out those who were selling, Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda.
46 he told them, "Scripture says, 'My house will be a house of prayer,' but you've made it a den of robbers." Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”
47 He taught daily in the temple, while the chief priests, scribes, and leaders of the people looked for a way to kill him, Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe.
48 but they found nothing they could do, since all the people hung on his words. Komabe iwo sanathe kupeza njira ina iliyonse kuti achite izi, chifukwa anthu onse anakhulupirira mawu ake.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]