Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 18 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then Jesus told them a parable about the need to always pray and never lose heart. Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke.
2 "In a certain town there was a judge who neither feared God nor respected people. Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu.
3 A widow in that town kept coming to him, saying, 'Grant me justice against my opponent.' Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’
4 For a while he refused, but then said to himself, 'Though I don't fear God nor respect people, “Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu,
5 since this widow keeps troubling me, I'll grant her justice, so she doesn't wear me out with her endless visits.'" koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ”
6 And the Lord said, "Listen to what the unjust judge says. Ndipo Ambuye anati, “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena.
7 Won't our Father bring justice for his chosen ones who cry to him day and night? Will he keep delaying? Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira?
8 I tell you, he will grant them justice quickly. But when the Son of Man comes, will he find faith on earth?" Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”
9 He also told this parable to some who trusted in themselves as righteous and despised everyone else: Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse.
10 "Two men went up to the temple to pray, one a Pharisee and the other a tax collector. “Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho.
11 The Pharisee stood and prayed about himself: 'God, I thank you I'm not like other people—robbers, wrongdoers, adulterers—or even like this tax collector.' Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu.
12 'I fast twice a week; I give a tenth of all I get.' Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’
13 But the tax collector, standing far off, would not even raise his eyes to heaven, but beat his chest, saying, 'our Father, have mercy on me, a sinner.' “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’
14 I tell you, this man went to his home justified, not the other. Everyone who lifts himself up will be humbled; the one who humbles himself will be lifted up." “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”
15 People were even bringing their infants to him to touch them, but the disciples saw this and warned them off. Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula.
16 But Jesus called the children to him and said, "Let the children come to me; don't stop them—the kingdom of our Father belongs to ones like these. Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere.
17 Truly I tell you: whoever doesn't accept the kingdom of our Father like a little child will never enter it." Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”
18 A certain ruler asked him, "Good Teacher, what must I do to inherit eternal life?" Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
19 Jesus said to him, "Why call me good? No one is good except our Father alone. Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha.
20 You know the commandments: 'Do not commit adultery, Do not murder, Do not steal, Do not testify falsely, Honor your father and mother.'" Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”
21 "All these I have kept since my youth," he said. Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”
22 Hearing this, Jesus said, "One thing you still lack: sell all you own, give to the poor, and you'll have treasure in heaven; then come, follow me." Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”
23 But when he heard this, he became very sad, for he was extremely rich. Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri.
24 Jesus looked at him and said, "How hard it is for the wealthy to enter our Father's kingdom! Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!
25 For it's easier for a camel to pass through a needle's eye than for a rich person to enter our Father's kingdom." Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”
26 Those who heard it asked, "Then who can be saved?" Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 But he said, "What is impossible for people is possible for our Father." Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
28 Then Peter said, "Look, we have left our own homes and followed you." Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”
29 He said to them, "Truly I tell you: no one has left house, wife, brothers, parents, or children for the sake of our Father's kingdom, Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu
30 who will not receive many times more now, and eternal life in the age to come." adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”
31 He took the Twelve aside and said, "Look, we're going up to Jerusalem, and all the prophets wrote about the Son of Man will be fulfilled. Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa.
32 For he will be handed over to the Gentiles, mocked, insulted, and spit on. Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira,
33 They will flog him and kill him, and on the third day he will rise." adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”
34 But they understood none of this; this saying was hidden from them, and they did not grasp what was said. Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.
35 As Jesus drew near to Jericho, a blind man was sitting by the roadside begging. Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha,
36 Hearing a crowd going by, he asked what was happening. anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika.
37 They told him, "Jesus of Nazareth is passing by." Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”
38 So he called out, "Jesus, Son of David, have mercy on me!" Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
39 Those who were in front rebuked him and told him to be quiet, but he cried out all the more, "Son of David, have mercy on me!" Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
40 Jesus stopped and ordered him brought to him. When he came near, Jesus asked, Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti,
41 "What do you want me to do for you?" He said, "Lord, let me see again." “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”
42 And Jesus said to him, "Receive your sight; your faith has saved you." Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.”
43 At once he could see and followed Jesus, glorifying our Father. All the people who saw it praised our Father too. Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]