Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 In the beginning was the Word, and the Word was with our Father, and the Word was God. Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.
2 He was in the beginning with our Father. Mawuwa anali ndi Mulungu pachiyambi.
3 All things were made through him, and without him not one thing was made that was made. Zinthu zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo popanda Iye sikukanakhala kanthu kalikonse kolengedwa.
4 In him was life, and the life was the light of all people. Mwa Iye munali moyo, ndipo moyowo unali kuwunika kwa anthu.
5 The light shines in the darkness, and the darkness has not overcome it. Kuwunika kunawala mu mdima, koma mdimawo sunakuzindikire.
6 There came a man sent from our Father, whose name was John. Kunabwera munthu amene anatumizidwa kuchokera kwa Mulungu; Iyeyo dzina lake linali Yohane.
7 He came as a witness, to bear witness about the light, so that all might believe through John's witness. Iye anabwera ngati mboni kudzachitira umboni kuwunikako kuti kudzera mwa iye anthu onse akhulupirire.
8 He was not the light, but came to bear witness about the light. Iyeyu sanali kuwunika; koma anabwera ngati mboni ya kuwunika.
9 The true light, which gives light to everyone, was coming into the world. Kuwunika koona kumene kuwunikira munthu aliyense kunabwera ku dziko lapansi.
10 He was in the world. The world came into being through him, yet did not know him. Iye anali mʼdziko lapansi, ndipo ngakhale kuti dziko lapansi linalengedwa ndi Iye, dziko lapansilo silinamuzindikire Iye.
11 He came to his own, and his own people did not receive him. Iye anabwera kwa iwo amene anali akeake, koma akewo sanamulandire Iye.
12 But to all who received him, believing in his name, he gave the right to become children of our Father, Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;
13 children born not of blood nor of the will of flesh nor of the will of man, but of our Father. ana wobadwa osati monga mwachilengedwe, kapena chisankho cha munthu, kapena chifuniro cha mwamuna koma wobadwa mwa Mulungu.
14 The Word became flesh and lived among us. We saw his glory, the glory of the one and only Son from the Father, full of grace and truth. Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.
15 John testified about him, crying out, "This is the one I meant: he who comes after me outranks me, since he existed before me." Yohane achitira umboni za Iye. Iye akufuwula kuti, “Uyu ndi Iye amene ndinati, ‘Iye amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa, Iyeyo analipo ine ndisanabadwe.’ ”
16 For from his fullness we have all received, grace upon grace. Kuchokera mʼkuchuluka kwa chisomo chake ife tonse talandira madalitso pamwamba pa madalitso.
17 For the law was given through Moses; grace and truth came through Jesus Christ. Pakuti lamulo linapatsidwa kudzera mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinabwera kudzera mwa Yesu Khristu.
18 No one has ever seen our Father; the one and only God, close beside the Father, has made him known. Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.
19 This is John's testimony, when the Jews sent priests and Levites from Jerusalem to ask him, "Who are you?" Tsopano uwu ndi umboni wa Yohane pamene Ayuda a ku Yerusalemu anatumiza ansembe ndi Alevi kudzamufunsa kuti iye anali yani.
20 He confessed, and did not deny, but confessed, "I am not the Christ." Iye sanalephere kuvomereza, koma iye anavomereza momasuka kuti, “Ine sindine Khristu.”
21 So they asked him, "What then? Are you Elijah?" "I am not," he said. "Are you the Prophet?" "No," he answered. Iwo anamufunsa kuti, “Nanga iwe ndiwe yani? Kodi ndiwe Eliya?” Iye anati, “Sindine.” “Kodi ndiwe Mneneri?” Iye anayankha kuti, “Ayi.”
22 So they asked, "Who are you? We need to give an answer to those who sent us. What do you say about yourself?" Pomaliza iwo anati, “Ndiwe yani? Tipatse yankho kuti tipite nalo kwa amene anatituma. Kodi iwe ukuti chiyani za iwe mwini?”
23 He said, "I'm the voice of one crying out in the wilderness, 'Make straight the way of the Lord,' as the prophet Isaiah said." Yohane anayankha ndi mawu a mneneri Yesaya kuti, “Ine ndi mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Wongolani njira ya Ambuye.’ ”
24 Now they had been sent from the Pharisees. Tsopano Afarisi ena amene anatumidwa
25 They asked him, "Why baptize, then, if you're not the Christ, nor Elijah, nor the Prophet?" anamufunsa Iye kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani, umabatiza ngati iwe si Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneri?”
26 John answered them, "I baptize with water, but among you stands one you do not know, Yohane anayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panu payima amene simukumudziwa.
27 even he who comes after me, whose sandal strap I am not worthy to untie." Iye ndi amene akubwera pambuyo panga, ine siwoyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”
28 These things took place in Bethany across the Jordan, where John was baptizing. Zonsezi zinachitika ku Betaniya kutsidya lina la mtsinje wa Yorodani, kumene Yohane ankabatizira.
29 The next day, seeing Jesus coming toward him, he said, "Look! The Lamb of our Father—Jesus—who takes away the sin of the world! Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi!
30 This is the one I meant: 'After me comes a man who ranks before me, because he was before me.' Uyu ndi amene ndimatanthauza pamene ndinanena kuti, ‘Munthu amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa analipo ine ndisanabadwe.’
31 I didn't know him, but I came baptizing with water so he would be revealed to Israel." Ine mwini sindinamudziwe Iye, koma ndinabwera kubatiza ndi madzi kuti Iye adziwike mu Israeli.”
32 John testified: "I saw the Holy Spirit descend from heaven like a dove and remain on him. Kenaka Yohane anapereka umboni uwu: “Ine ndinaona Mzimu Woyera ngati nkhunda kuchokera kumwamba nakhala pa Iye.
33 I didn't know him, but the one who sent me to baptize with water told me, 'The one you see the Holy Spirit come down and stay on—he is the one who baptizes with the Holy Spirit.' Ine sindikanamudziwa Iye, koma kuti amene anandituma ine kudzabatiza ndi madzi anati kwa ine, ‘Munthu amene udzaona Mzimu Woyera akutsika nakhazikika pa Iye ndi amene adzabatize ndi Mzimu Woyera.’
34 And I have seen and have borne witness that this is the Son of our Father." Ine ndaona ndipo ndikuchitira umboni kuti uyu ndi Mwana wa Mulungu.”
35 The next day John was standing again with two of his disciples, Pa tsiku lotsatira Yohane analinso pamenepo pamodzi ndi awiri a ophunzira ake.
36 and looking at Jesus as he walked by, he said, "Look! The Lamb of our Father!" Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”
37 The two disciples heard him say this, and they followed Jesus. Ophunzira ake awiriwo atamva iye akunena izi, iwo anamutsatira Yesu.
38 Jesus turned, saw them following, and asked, "What do you seek?" They said, "Rabbi" (meaning Teacher), "where do you stay?" Atatembenuka, Yesu anaona iwo akumutsatira ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” Iwo anati, “Rabi (kutanthauza kuti Aphunzitsi), kodi mukukhala kuti?”
39 He told them, "Come and you will see." So they went and saw where he was staying, and remained with him that day—about four in the afternoon. Iye anayankha kuti, “Bwerani mudzaone.” Choncho iwo anapita ndi kukaona kumene Iye amakhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Linali ngati pafupifupi ora la khumi.
40 One of the two who heard John speak and followed Jesus was Andrew, Simon Peter's brother. Andreya mʼbale wake wa Simoni Petro, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndiponso amene anamutsata Yesu.
41 He first found his own brother Simon and told him, "We've found the Messiah" (meaning Christ). Choncho chimene Andreya anachita ndi kukapeza mʼbale wake Simoni ndipo anamuwuza kuti, “Ife tamupeza Mesiya,” (kutanthauza kuti Khristu).
42 He brought him to Jesus. Jesus looked at him and said, "You are Simon the son of John. You will be called Cephas" (meaning Peter). Kenaka iye anabweretsa Simoni kwa Yesu, amene anamuyangʼana ndipo anati, “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Udzatchedwa Kefa” (limene litanthauza kuti Petro).
43 The next day, Jesus decided to leave for Galilee. He found Philip and said, "Follow me." Pa tsiku lotsatira Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Atamupeza Filipo, anati kwa iye, “Nditsate.”
44 Now Philip was from Bethsaida, the city of Andrew and Peter. Filipo monga Andreya ndi Petro, anali wochokera ku mzinda mudzi Betisaida.
45 Philip found Nathanael and told him, "We've found the one Moses wrote of in the Law and the prophets—Jesus, son of Joseph, from Nazareth." Filipo anakapeza Natanieli ndipo anamuwuza kuti, “Ife tapeza amene Mose analemba za Iye mʼmalamulo, ndi zimene aneneri analembanso za Iye, Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe.”
46 Nathanael said, "Can anything good come from Nazareth?" Philip said, "Come and see." Natanieli anafunsa kuti, “Nazareti! Kodi kanthu kalikonse kabwino kangachokere kumeneko?” Filipo anati, “Bwera udzaone.”
47 Jesus saw Nathanael approaching and said of him, "Look—a true Israelite, with no deceit in him!" Yesu atamuona Natanieli akuyandikira, anati kwa iye, “Uyu ndi Mwisraeli weniweni, mwa iye mulibe chinyengo.”
48 Nathanael asked him, "How do you know me?" Jesus answered, "Before Philip called you, while you were under the fig tree, I saw you." Natanieli anafunsa kuti, “Kodi mwandidziwa bwanji?” Yesu anayankha kuti, “Ine ndinakuona iwe utakhala pansi pamtengo wamkuyu Filipo asanakuyitane.”
49 Nathanael answered him, "Rabbi, you are the Son of our Father! You are the King of Israel!" Kenaka Natanieli ananena kuti, “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli.”
50 Jesus answered him, "You believe because I told you I saw you under the fig tree? You'll see greater things than these." Yesu anati, “Ukukhulupirira chifukwa chakuti ndakuwuza kuti Ine ndinakuona iwe uli pansi pamtengo wamkuyu? Iwe udzaona zinthu zazikulu kuposa izo.”
51 He told him, "Truly, truly, I say to you, you will see heaven opened, and our Father's angels ascending and descending on the Son of Man." Ndipo Iye anapitirira kuti, “Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]