Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 On the third day, a wedding took place in Cana of Galilee; Jesus's mother was there. Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko,
2 Jesus and his disciples were also invited to the wedding. ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo.
3 When the wine ran out, the mother of Jesus said to him, "They have no wine." Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
4 "Woman, why are you bringing me into this?" Jesus replied. "My hour has not yet come." Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
5 His mother said to the servants, "Do whatever he tells you." Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
6 Six stone water jars stood there, used for Jewish purification, each holding twenty to thirty gallons. Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
7 Jesus said to them, "Fill the jars with water," so they filled them to the brim. Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
8 He told them, "Draw some out now, and take it to the head steward." So they did. Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.” Iwo anachita momwemo.
9 The master of the banquet tasted the water now wine, not knowing its source—though the servants who drew it knew. So he called the bridegroom aside, Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali
10 and said, "Everyone serves the good wine first, then the lesser once guests are drunk. But you've kept the good wine till now." ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
11 Jesus performed this first sign at Cana in Galilee. He revealed his glory, and his disciples believed in him. Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
12 After this he went down to Capernaum with his mother, brothers, and disciples, and stayed there a few days. Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.
13 When the Jewish Passover was near, Jesus went up to Jerusalem. Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu.
14 In the temple courts he found sellers of cattle, sheep, and doves, and others sitting at tables exchanging money. Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo.
15 He made a whip of cords and drove them all out of the temple courts, sheep and cattle alike, poured out the money-changers' coins, and overturned their tables. Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo.
16 To the dove sellers he said, "Take these out of here! Don't make my Father's house a marketplace." Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”
17 His disciples remembered that it is written: "Zeal for your house will consume me." Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”
18 So the Jews asked, "What sign will you show us for doing these things?" Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”
19 Jesus answered them, "Destroy this temple, and in three days I will raise it up." Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”
20 They replied, "This temple took forty-six years to build, and will you raise it in three days?" Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?”
21 But the temple he had spoken of was his body. Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.
22 After he rose from the dead, his disciples remembered he had said this, and believed the Scripture and the word Jesus had spoken. Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.
23 While he was in Jerusalem at the Passover, many saw the signs he did and trusted in his name. Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake.
24 But Jesus would not entrust himself to them, for he knew all people. Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse.
25 He didn't need anyone's testimony about people—he knew what was in each one. Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]