Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 In those days Caesar Augustus issued a decree to register the whole inhabited world. Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma.
2 This was the first registration, when Quirinius was governor of Syria. (Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya).
3 Everyone went to be registered, each to his own town. Ndipo aliyense anapita ku mzinda wa kwawo kukalembetsa.
4 Joseph too went up from Galilee, from the town of Nazareth, to Judea, to the city of David called Bethlehem, since he belonged to David's house and family, Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide.
5 to be registered with Mary, his fiancée, who was expecting a child. Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera.
6 While they were there, the time came for her to give birth. Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe,
7 She gave birth to her firstborn son, wrapped him in cloths, and laid him in a manger, because the inn had no place for them. ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.
8 Shepherds were in that same region, staying out in the fields, keeping watch over their flock by night. Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku.
9 An angel of our Father stood before them; the glory of our Father shone around them, and great fear seized them. Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha.
10 The angel told them, "Don't be afraid—I bring good news of great joy for everyone: Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse.
11 Today in the city of David, a Savior was born to you—Christ the Lord. Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye.
12 This is your sign: you'll find a baby wrapped in cloths, lying in a manger." Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.”
13 Suddenly there was with the angel a multitude of the heavenly host, praising our Father and saying, Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,
14 "Glory to our Father in the highest, and on earth peace among those with whom he is pleased!" “Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba, ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”
15 When the angels left them for heaven, the shepherds said to each other, "Let's go straight to Bethlehem and see this thing that has happened, which our Father has made known to us." Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”
16 They hurried off and found Mary and Joseph, and the baby lying in the manger. Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe.
17 When they saw him, they made known what had been told them about this child. Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo,
18 All who heard were amazed at what the shepherds told them. ndipo onse amene anamva zimene abusawa ananena anadabwa.
19 But Mary treasured up all these things, pondering them in her heart. Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira.
20 The shepherds returned, glorifying and praising our Father for all they'd heard and seen, just as they were told. Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.
21 When eight days for his circumcision were complete, he was named Jesus, the name the angel gave before he was conceived in the womb. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.
22 When their days of purification under the Law of Moses ended, they brought him up to Jerusalem to present him to our Father, Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye.
23 (as it is written in our Father's Law, "Every firstborn male will be called holy to our Father"), (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”),
24 and to offer a sacrifice as the Law of our Father says: a pair of turtledoves or two young pigeons. ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.”
25 In Jerusalem lived a man named Simeon, righteous and devout, waiting for Israel's comfort, with the Holy Spirit on him. Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.
26 The Holy Spirit had revealed to him he wouldn't die before seeing our Father's Christ. Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye.
27 Prompted by the Spirit, he entered the temple. As the parents brought in the child Jesus to do for him what the Law required, Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo,
28 Simeon took him up in his arms and blessed our Father, saying, Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:
29 "Sovereign Father, now you are letting your servant depart in peace, according to your word. “Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza, tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere.
30 For my eyes have seen your salvation, Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,
31 which you have prepared in the presence of all peoples: chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse,
32 a light for revelation to the Gentiles, and for glory to your people Israel." kuwala kowunikira anthu a mitundu ina ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli.”
33 His father and mother were amazed at what was said about him. Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye.
34 And Simeon blessed them and told Mary, his mother, "This child is appointed for the fall and rising of many in Israel, and to be a sign that is opposed, Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho,
35 and a sword will pierce through your own soul also—so that thoughts from many hearts may be revealed." kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.”
36 Also there was Anna, a woman prophet, daughter of Phanuel of Asher's tribe, very old, having lived with her husband seven years after her virginity, Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa,
37 and a widow until eighty-four, never leaving the temple, worshiping with fasting and prayer night and day. ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera.
38 Coming up at that same hour, she gave thanks to our Father and spoke of the child to all awaiting Jerusalem's redemption. Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.
39 When they finished everything required by our Father's Law, they returned to Galilee, to their own town of Nazareth. Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti.
40 The child grew, becoming strong, filled with wisdom, and our Father's favor was on him. Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
41 Now his parents went to Jerusalem every year at the Feast of Passover. Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska.
42 When he was twelve years old, they went up according to the custom of the feast. Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo.
43 When the festival ended and they left for home, the boy Jesus stayed behind in Jerusalem, unknown to his parents. Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi.
44 Thinking he was in the group, they traveled a day's journey, then searched for him among relatives and acquaintances. Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo.
45 When they did not find him, they returned to Jerusalem, searching for him. Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna.
46 After three days they found him in the temple, sitting among the teachers, listening to them and asking them questions. Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso.
47 All who heard him were amazed at his understanding and his answers. Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake.
48 When his parents saw him, they were astonished. His mother said, "Child, why have you done this to us? Look, your father and I have been anguished, searching for you." Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.”
49 He said to them, "Why were you searching for me? Didn't you know I must be in my Father's house?" Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?”
50 But they did not understand the saying that he spoke to them. Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.
51 Then he went down with them and came to Nazareth, remaining obedient to them. His mother kept all these things in her heart. Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.
52 Jesus increased in wisdom and stature and in favor with our Father and with people. Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]