Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Since many have undertaken to compile an ordered account of what has been accomplished among us. Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu,
2 Just as eyewitnesses from the beginning and servants of the word handed these accounts to us, monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu.
3 I too, having traced everything accurately from the start, decided to write it in order for you, most excellent Theophilus, Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo,
4 so that you may know the certainty of the things you have been taught. kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa.
5 In the days of Herod, king of Judea, a priest named Zechariah was in Abijah's priestly division. His wife Elizabeth descended from Aaron. Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni.
6 They were both righteous before our Father, walking blamelessly in all his commandments and ordinances. Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse.
7 But they had no child, because Elizabeth was barren, and both were very old. Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba.
8 Now while he was serving as priest before our Father when his division was on duty, Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu,
9 by priestly custom, lot chose him to enter his sanctuary and burn incense. Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani.
10 And the whole crowd of the people were praying outside at the hour of incense. Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja.
11 Then an angel of our Father appeared to him, standing at the right of the altar of incense. Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira.
12 Zechariah was shaken when he saw him, and fear came over him. Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha.
13 The angel said to him, "Don't be afraid, Zechariah—your prayer has been heard. Your wife Elizabeth will bear you a son; name him John. Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane.
14 You will have joy and gladness; many will rejoice at his birth. Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake,
15 He will be great before our Father, must never drink wine or other alcoholic drinks, and he will be filled with the Holy Spirit even from his mother's womb. chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa.
16 And he will turn many of the children of Israel back to their Father. Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo.
17 He will go before our Father in Elijah's spirit and power, turning fathers' hearts to their children, and the disobedient to the wisdom of the righteous, to prepare a people ready for our Father." Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”
18 Zechariah said to the angel, "How will I know this? I'm old, and my wife is well along in years." Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.”
19 The angel answered him, "I am Gabriel, who stands in our Father's presence, sent to speak to you and bring you this good news. Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu.
20 And now you will be silent, unable to speak, until the day these things happen, because you did not believe my words, which will come true in their time." Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”
21 Meanwhile the people waited for Zechariah, wondering why he stayed so long in the sanctuary. Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu.
22 When he came out, he could not speak to them, and they knew he had seen a vision in the sanctuary. He kept motioning to them and stayed mute. Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula.
23 And when his days of service were ended, he went home. Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo.
24 After these days his wife Elizabeth became pregnant, and for five months she kept herself hidden, saying, Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu.
25 "This is what our Father did for me, in the days he looked on me, to remove my disgrace among people." Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.”
26 In month six our Father sent the angel Gabriel to a Galilee town called Nazareth, Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya,
27 to a virgin engaged to a man named Joseph, of the house of David; the virgin's name was Mary. kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya.
28 And he came to her and said, "Greetings, favored one! Our Father is with you." Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”
29 But she was greatly troubled by his words, and wondered what kind of greeting this might be. Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere.
30 The angel said to her, "Don't be afraid, Mary, for you have found favor with our Father. Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu.
31 You will conceive in your womb and bear a son, and you will call his name Jesus. Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu.
32 He will be great and called Son of the Most High, and our Father will give him the throne of his father David, Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide,
33 and he will reign over Jacob's house forever; his kingdom will never end." ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”
34 And Mary said to the angel, "How will this be, since I am a virgin?" Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”
35 The angel answered her, "The Holy Spirit will come over you, and the Most High's power will shadow you; so the holy child born will be called the Son of our Father. Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu.
36 Look, your relative Elizabeth has also conceived a son in her old age—this is the sixth month for her called barren. Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.
37 For nothing will be impossible with our Father." Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”
38 Mary said, "I am the servant of our Father; let it happen to me as you said." Then the angel left her. Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”
39 In those days Mary got up and hurried to the hill country, to a town in Judah, Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya,
40 and she entered the house of Zechariah and greeted Elizabeth. kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti.
41 When Elizabeth heard Mary's greeting, her baby leaped in her womb, and she was filled with the Holy Spirit. Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera.
42 She cried out with a loud voice, "Blessed are you among women, blessed is the fruit of your womb! Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke!
43 And why is this granted to me, that the mother of my Lord should come to me? Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine?
44 For the moment I heard your greeting, the baby in my womb leaped for joy. Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe.
45 Blessed is she who believed that there would be a fulfillment of what our Father spoke to her." Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!”
46 And Mary said, "My soul magnifies our Father, Ndipo Mariya anati: “Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47 and my spirit rejoices in our Father, my Savior, Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 for he has looked on the humble estate of his servant. For from now on all generations will call me blessed; pakuti wakumbukira kudzichepetsa kwa mtumiki wake. Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49 for the Mighty One has done great things for me, and holy is his name. pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu, dzina lake ndi loyera.
50 And his mercy is for those who fear him from generation to generation. Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye kufikira mibadomibado.
51 He has shown strength with his arm; he has scattered the proud in the thoughts of their hearts; Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake; Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 he has brought down the mighty from their thrones and lifted up the humble; Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu, koma wakweza odzichepetsa.
53 he has filled the hungry with good things, and the rich he has sent away empty. Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 He has helped his servant Israel, in remembrance of his mercy, Iye anathandiza mtumiki wake Israeli, pokumbukira chifundo chake.
55 just as he spoke to our fathers, to Abraham and to his offspring forever." Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse monga ananena kwa makolo athu.”
56 And Mary remained with her about three months and then returned to her home. Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo.
57 Now the time came for Elizabeth to give birth, and she bore a son. Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna.
58 Her neighbors and relatives heard our Father had shown her great mercy, and rejoiced with her. Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi.
59 On the eighth day they came to circumcise the child, and were going to call him Zechariah after his father, Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya,
60 but his mother answered, "No; he will be called John." koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.”
61 And they said to her, "None of your relatives is called by this name." Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.”
62 And they made signs to his father, asking what Zechariah wanted the child to be called. Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo.
63 He asked for a tablet and wrote, "His name is John." And everyone was amazed. Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.”
64 And immediately his mouth was opened and his tongue loosed, and he spoke, blessing our Father. Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu.
65 Fear fell on all their neighbors, and all these things were talked about throughout Judea's hill country. Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi.
66 And all who heard kept these things in their hearts, saying, "What then will this child become?" For our Father's hand was with him. Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye.
67 And his father Zechariah was filled with the Holy Spirit and prophesied, saying, Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,
68 "Blessed be our Father of Israel, for he has visited and redeemed his people, “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
69 and has raised up a mighty Savior for us in the house of his servant David, Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife mu nyumba ya mtumiki wake Davide.
70 as he spoke through the mouth of his holy prophets long ago, (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),
71 that we should be saved from our enemies and from the hand of all who hate us; chipulumutso kuchoka kwa adani athu ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,
72 to show the mercy promised to our fathers and to remember his holy covenant, kuonetsa chifundo kwa makolo athu ndi kukumbukira pangano lake loyera,
73 the oath that he swore to our father Abraham, to grant us, lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:
74 that we, being delivered from the hand of our enemies, might serve him without fear, kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu, ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,
75 in holiness and righteousness before him all our days. mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.
76 And you, child, will be called the prophet of the Most High; for you will go before the Lord to prepare his ways, “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba; pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,
77 to give his people the knowledge of salvation through the forgiveness of their sins, kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,
78 because of the tender mercy of our Father, by which the sunrise from on high will visit us, chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,
79 to give light to those who sit in darkness and in the shadow of death, to guide our feet into the way of peace." kuwalira iwo okhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa, kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”
80 The child grew, became strong in spirit, and lived in the wilderness until the day he appeared publicly to Israel. Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]