Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Luke 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 In Tiberius Caesar's fifteenth year, when Pontius Pilate was governor of Judea, Herod was tetrarch of Galilee, his brother Philip of the region of Ituraea and Trachonitis, and Lysanias of Abilene, Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene.
2 under high priests Annas and Caiaphas, our Father's word came to John son of Zechariah in the wilderness. Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu.
3 He went through the whole Jordan region, preaching a baptism of repentance for the forgiveness of sins, Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo.
4 as it is written in the book of the words of Isaiah the prophet: "A voice of one calling in the wilderness: Prepare the way for the Lord, make his paths straight. Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti: “Mawu a wofuwula mʼchipululu, konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.
5 Every valley will be filled in, and every mountain and hill made low. The crooked roads will become straight, and the rough ways smooth, Chigwa chilichonse chidzadzazidwa ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, misewu yokhotakhota idzawongoledwa, ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.
6 and all flesh will see the salvation of our Father." Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”
7 John said then to the crowds coming to be baptized by him: "You brood of vipers! Who warned you to flee the coming wrath? Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera?
8 So produce fruit worthy of repentance. Don't start telling yourselves, 'We have Abraham as our father.' For I tell you, our Father can raise up children for Abraham from these stones. Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana.
9 Already the axe lies at the root of the trees; every tree not bearing good fruit is cut down and thrown into the fire." Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”
10 And the crowds asked him, "What then should we do?" Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”
11 He replied, "Whoever has two shirts, share with the one who has none; whoever has food, do the same." Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”
12 Tax collectors also came to be baptized, and they said to him, "Teacher, what should we do?" Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”
13 "Collect no more than you are required to," he told them. Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.”
14 Soldiers also asked him, "And us—what should we do?" He said to them, "Don't extort anyone by force or false charges; be satisfied with your wages." Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”
15 The people were expectant, all wondering in their hearts whether John himself might be the Christ. Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu.
16 John answered them all, "I baptize you with water. But one stronger than I is coming—I'm not worthy to untie his sandal strap. He will baptize you with the Holy Spirit and fire. Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto.
17 Winnowing fork in hand, he will clear his threshing floor, gather the wheat into his barn, but burn the chaff with fire that can't be put out." Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.”
18 And with many other words of exhortation, John proclaimed the good news to the people. Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.
19 But John confronted Herod the tetrarch about Herodias, his brother's wife, and about all the evil Herod had done, Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita,
20 Herod added this to all the rest: he locked John up in prison. Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.
21 When all the people were baptized, Jesus was baptized too. As he prayed, heaven opened, Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka.
22 and the Holy Spirit descended on him in bodily form like a dove. And a voice came from heaven: "You are my beloved Son; in you I delight." Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”
23 Jesus was about thirty when he began his ministry, the son—so it was thought—of Joseph, son of Heli, Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,
24 the son of Matthat, the son of Levi, the son of Melchi, the son of Jannai, the son of Joseph, mwana wa Matate, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe
25 the son of Mattathias, the son of Amos, the son of Nahum, the son of Esli, the son of Naggai, mwana wa Matati, mwana wa Amosi, mwana wa Naomi, mwana wa Esli, mwana wa Nagai,
26 the son of Maath, the son of Mattathias, the son of Semein, the son of Josech, the son of Joda, mwana wa Maati, mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda
27 the son of Joanan, the son of Rhesa, the son of Zerubbabel, the son of Shealtiel, the son of Neri, mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, mwana wa Neri,
28 the son of Melchi, the son of Addi, the son of Cosam, the son of Elmadam, the son of Er, mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,
29 the son of Joshua, the son of Eliezer, the son of Jorim, the son of Matthat, the son of Levi, mwana wa Jose, mwana wa Eliezara, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,
30 the son of Simeon, the son of Judah, the son of Joseph, the son of Jonam, the son of Eliakim, mwana wa Simeoni, mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,
31 the son of Melea, the son of Menna, the son of Mattatha, the son of Nathan, the son of David, mwana wa Meleya, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natani, mwana wa Davide,
32 the son of Jesse, the son of Obed, the son of Boaz, the son of Salmon, the son of Nahshon, mwana wa Yese, mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,
33 the son of Amminadab, the son of Admin, the son of Arni, the son of Hezron, the son of Perez, the son of Judah, mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni, mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,
34 the son of Jacob, the son of Isaac, the son of Abraham, the son of Terah, the son of Nahor, mwana wa Yakobo, mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,
35 the son of Serug, the son of Reu, the son of Peleg, the son of Eber, the son of Shelah, mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, mwana wa Sela,
36 the son of Cainan, the son of Arphaxad, the son of Shem, the son of Noah, the son of Lamech, mwana wa Kainane, mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,
37 the son of Methuselah, the son of Enoch, the son of Jared, the son of Mahalalel, the son of Cainan, mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli, mwana wa Kainane,
38 the son of Enosh, the son of Seth, the son of Adam, the son of our Father. mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]