Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 9 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 As Jesus passed by, he saw a man who had been blind from birth. Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire.
2 His disciples asked him, "Rabbi, who sinned, this man or his parents, that he was born blind?" Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?”
3 "Neither this man nor his parents sinned,' Jesus answered, 'but this happened so the works of our Father might be revealed in him. Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu.
4 We must do the works of the one who sent me while it is day; night comes, when no one can work. Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito.
5 As long as I am in the world, I am the light of the world.'" Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”
6 Saying this, he spat on the ground, made mud from the saliva, and smeared it on the man's eyes. Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo.
7 He told him, "Go, wash in the pool of Siloam" (meaning Sent). So the man went, washed, and returned able to see. Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
8 Neighbors and those who'd seen him begging before said, "Isn't this the one who used to sit and beg?" Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?”
9 Some said, "That's him." Others said, "No, he just looks like him." He kept saying, "I'm the one." Ena ananena kuti anali yemweyo. Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.” Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.”
10 So they asked him, "Then how were your eyes opened?" Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”
11 He replied, "The man called Jesus made mud, smeared it on my eyes, and told me, 'Go to Siloam and wash.' So I went, washed, and could see." Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.”
12 They said to him, "Where is he?" He said, "I do not know." Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?” Iye anati, “Ine sindikudziwa.”
13 They brought the man who had been blind to the Pharisees. Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi.
14 Now it was a Sabbath day when Jesus made the mud and opened his eyes. Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu.
15 So the Pharisees also asked him again how he had gained sight. He told them, "He put mud on my eyes, and I washed, and I see." Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.”
16 Some Pharisees said, "This man isn't from God—he doesn't keep the Sabbath." Others said, "How can a sinful man do such signs?" So they were divided among them. Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.” Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.
17 Again they asked the blind man, "What do you say about him, since he opened your eyes?" He said, "He is a prophet." Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?” Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”
18 The Jews did not believe he had been blind and gained sight, until they summoned the parents of the man who had gained sight. Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake.
19 They asked them, "Is this your son you say was born blind? How then does he now see?" Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?”
20 His parents answered, "We know that this is our son and that he was born blind. Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona.
21 But how he now sees, we don't know; or who opened his eyes, we don't know. Ask him—he's an adult; he'll speak for himself." Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.”
22 His parents said this, fearing the Jews, since the Jews had already agreed that if anyone confessed Jesus as the Christ, he would be expelled from the synagogue. Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge.
23 That was why his parents said, "He is of age; ask him." Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.”
24 So they called the once-blind man again and said, "Give God the glory. We know this man is a sinner." Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”
25 He replied, "Whether he's a sinner, I don't know. I know one thing: I was blind, now I see." Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”
26 They said to him, "What did he do to you? How did he open your eyes?" Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?”
27 He answered them, "I already told you, and you didn't listen. Why do you want to hear it again? Do you also want to become his disciples?" Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?”
28 And they reviled him, saying, "You are his disciple, but we are disciples of Moses. Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose!
29 We know God spoke to Moses, but we don't know where this man is from." Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”
30 The man answered them, "Here's the amazing thing: you don't know where he's from, yet he opened my eyes. Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga.
31 We know God doesn't listen to sinners, but if anyone reveres God and does his will, God listens to him. Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake.
32 Never since the world began has anyone heard of someone opening the eyes of a person born blind. Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona.
33 If this man were not from God, he could do nothing." Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”
34 They answered him, "You were born entirely in sin, yet you teach us?" and threw him out. Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja.
35 Jesus heard they had thrown him out, and finding him, said, "Do you believe in the Son of Man?" Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”
36 He answered, "And who is he, sir, so I can believe in him?" Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?”
37 Jesus said to him, "You have seen him, and it is he who is speaking with you." Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.”
38 He said, "Lord, I believe," and he worshiped him. Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.
39 Jesus said, "I came into this world for judgment, so those who don't see may see, and those who see may become blind." Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.”
40 Some Pharisees with him heard this and said, "Are we blind too?" Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?”
41 Jesus told them, "If you were blind, you would have no sin; but since you say, 'We see,' your sin remains." Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]