Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 8 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 But Jesus went to the Mount of Olives. Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi.
2 At dawn he came again to the temple; all the people came to him, and he sat down and taught them. Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa.
3 The scribes and Pharisees brought a woman caught in adultery and stood her in the middle. Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo
4 They said to him, "Teacher, this woman was caught in the act of adultery. anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo.
5 Now in the Law, Moses commanded us to stone such women. So what do you say? Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?”
6 They said this to test him, seeking grounds to accuse him. But Jesus bent down and wrote on the ground with his finger." Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye. Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake.
7 When they kept questioning him, he stood up and said to them, "Whichever of you has no sin, cast the first stone at her." Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.”
8 And once more he bent down and wrote on the ground. Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.
9 Hearing this, they left one by one, starting with the oldest, until Jesus was left alone with the woman standing there. Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo.
10 Jesus stood up and said to her, "Woman, where are they? Has no one condemned you?" Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”
11 She said, "No one, Lord." Jesus said, "I don't condemn you either. Go, and from now on, don't sin anymore." Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.” “Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”
12 Jesus spoke to them again: "I am the world's light. Whoever follows me will never walk in darkness but will have the light of life." Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
13 So the Pharisees said to him, "You are bearing witness about yourself; your testimony is not true." Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”
14 Jesus replied, "Even if I testify about myself, my testimony is true, because I know where I came from and where I'm going; but you don't know where I come from or where I'm going. Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita.
15 You judge according to the flesh; I judge no one. Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense.
16 Even if I judge, my judgment is true, since I do not judge alone, but I and the Father who sent me. Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma.
17 In your Law it is written that the testimony of two people is true. Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka.
18 I testify about myself, and the Father who sent me testifies about me." Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”
19 They asked, "Where is your Father?" Jesus answered, "You know neither me nor my Father. If you knew me, you would know my Father also." Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?” Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.”
20 He said this while teaching in the temple, in the treasury; no one seized him—his hour had not yet come. Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.
21 So he told them again, "I am going away. You will look for me and die in your sin. Where I am going, you cannot come." Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”
22 So the Jews said, "Will he kill himself, since he says, "You can't come where I'm going"?" Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”
23 He said to them, "You're from below; I'm from above. You're of this world; I'm not of this world. Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino.
24 I told you that you'll die in your sins; if you don't believe I AM, you'll die in your sins." Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”
25 So they said to him, "Just who are you?" Jesus said to them, "Exactly what I've said from the start. Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?” Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi,
26 I have much to say and judge about you, but the One who sent me is true; what I heard from him, I tell the world." ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”
27 They did not understand that he had been speaking to them about the Father. Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake.
28 So Jesus told them, "When you lift up the Son of Man, then you'll know that I AM, and that I do nothing on my own, but say these things as the Father taught me. Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa.
29 The one who sent me is with me; he hasn't left me alone, because I always do what pleases him." Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.”
30 As he was saying these things, many believed in him. Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.
31 Jesus then told the Jews who had believed him, "If you remain in my word, you are truly my disciples, Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga.
32 and you will know the truth, and the truth will set you free." Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
33 They answered him, "We are Abraham's descendants, never enslaved to anyone. How can you say, 'You will become free'?" Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”
34 Jesus answered them, "Truly, truly, I tell you: everyone who keeps sinning is sin's slave. Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.
35 The slave does not remain in the house forever; the son remains forever. Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse.
36 So if the Son sets you free, you will be free indeed. Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu.
37 I know you are Abraham's descendants; yet you seek to kill me because my word has no space in you. Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu.
38 I speak what I've seen with my Father, and you do what you heard from your father." Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”
39 They answered, "Abraham is our father." Jesus said, "If you were Abraham's children, you'd do the works Abraham did, Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.” Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita.
40 but now you want to kill me—a man who told you the truth I heard from my Father. Abraham didn't do this. Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi.
41 You do your father's works." They said to him, "We weren't born of sexual sin. We have one Father—God himself." Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.” Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”
42 Jesus said to them, "If God were your Father, you'd love me, for I came from God and am here. I didn't come on my own—he sent me. Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha.
43 Why don't you understand my speech? Because you cannot bear to hear my word. Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga.
44 You belong to your father, the devil, and want to carry out his desires. He was a murderer from the beginning, not standing in truth, since no truth is in him. When he lies, he speaks from his own nature, since he's a liar and the lie's father. Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.
45 But because I tell the truth, you do not believe me. Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine!
46 Who among you convicts me of sin? If I speak truth, why don't you believe me? Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira?
47 Whoever is from our Father hears his words; you don't hear because you're not from our Father." Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”
48 The Jews replied, "Aren't we right in saying that you are a Samaritan and have a demon?" Ayuda anamuyankha Iye kuti, “Kodi ife sitikulondola ponena kuti Inu ndi Msamariya ndi wogwidwa ndi chiwanda?”
49 Jesus answered, "I do not have a demon, but I honor my Father, and you dishonor me. Yesu anati, “Ine sindinagwidwe ndi chiwanda, koma ndimalemekeza Atate anga, koma inu mukundinyoza.
50 But I'm not seeking my own glory; our Father seeks it, and he judges. Ine sindidzifunira ndekha ulemu; koma alipo wina amene amandifunira, ndipo Iyeyo ndiye woweruza.
51 Truly, truly, I say to you, if anyone keeps my word, he will never see death." Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”
52 The Jews said to him, "Now we know you have a demon. Abraham died, as did the prophets, yet you say, 'Whoever keeps my word will never taste death.' Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’
53 Are you greater than our father Abraham, who died? The prophets died too! Who do you claim to be?" Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?”
54 Jesus answered, "If I glorify myself, my glory is nothing. It is my Father who glorifies me, of whom you say, 'He is our God.' Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine.
55 You don't know him, but I know him. If I said I didn't know him, I'd be a liar like you. But I know him and keep his word. Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake.
56 Your father Abraham rejoiced that he would see my day. He saw it and was glad." Abambo anu Abrahamu anakondwera poyembekezera kubwera kwanga. Iwo anandiona ndipo anasangalala.”
57 So the Jews said to him, "You're not yet fifty years old, and you've seen Abraham?" Ayuda anati kwa Iye, “Inu sumunafike nʼkomwe zaka makumi asanu, ndipo mukuti munamuona Abrahamu!”
58 Jesus said to them, "Truly, truly, I say to you, before Abraham was, I AM." Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!”
59 So they grabbed stones to throw at him, but Jesus hid himself and slipped out of the temple. Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]