Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 10 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 "Truly, truly, I tell you: whoever doesn't enter the sheepfold through the gate, but climbs in another way, is a thief and a robber. “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba.
2 But the one who enters by the gate is the shepherd of the sheep. Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo.
3 The gatekeeper opens for him, and the sheep hear his voice. He calls his own sheep by name and leads them out. Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa.
4 After bringing all his own out, he goes ahead of them, and the sheep follow him because they know his voice. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake.
5 They will never follow a stranger—they'll run from him, since they don't know the voice of strangers." Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.”
6 Jesus told them this figure of speech, but they didn't grasp what he meant. Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
7 So Jesus said again, "Truly, truly, I tell you, I am the gate for the sheep. Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa.
8 "All who came before me are thieves and robbers, but the sheep did not listen to them. Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere.
9 I am the gate; whoever enters through me will be saved, going in and out, finding pasture. Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.
10 The thief comes only to steal, kill, and destroy. I came so they may have life, and have it in abundance. Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
11 "I am the good shepherd. The good shepherd lays down his life for the sheep. “Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
12 The hired hand, not a shepherd, doesn't own the sheep. Seeing the wolf coming, he leaves the sheep and flees—the wolf snatches and scatters them. Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa.
13 The man runs away because he is a hired hand and cares nothing for the sheep. Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.
14 "I am the good shepherd. I know my own and my own know me, “Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa,
15 as the Father knows me and I know the Father, and I lay down my life for the sheep. monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
16 I have other sheep not of this fold; I must lead them too, and they will hear my voice. They will become one flock, one shepherd. Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi.
17 This is why the Father loves me: I lay down my life only to take it up again. Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso.
18 No one takes it from me, but I lay it down on my own. I have authority to lay it down, and authority to take it up again. This charge I received from my Father." Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
19 These words brought division among the Jews once again. Pa mawu awa Ayuda anagawikananso.
20 Many of them said, "He is demon-possessed and out of his mind. Why listen to him?" Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”
21 But others said, "These aren't a demon-possessed man's words. Can a demon open blind eyes?" Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”
22 Then came the Feast of Dedication at Jerusalem. It was winter, Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira,
23 and Jesus was walking in the temple, in Solomon's Colonnade. ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni.
24 The Jews surrounded him and said, "How long will you hold us in suspense? If you are the Christ, tell us plainly." Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”
25 Jesus answered, "I told you, and you don't believe. The works I do in my Father's name testify about me, Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni,
26 but you do not believe, because you are not my sheep. koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga.
27 My sheep listen to my voice; I know them, and they follow me. Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.
28 I give them eternal life, and they will never perish, and no one will snatch them from my hand. Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.
29 My Father, who gave them to me, is greater than all; no one can snatch them out of the Father's hand. Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga.
30 I and the Father are one." Ine ndi Atate ndife amodzi.”
31 Again the Jews picked up stones to stone him. Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye,
32 Jesus replied, "I have shown you many good works from the Father. For which of these are you going to stone me?" koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”
33 "We're stoning you not for good work," they said, "but for blasphemy, because you, a mere man, claim to be God." Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
34 Jesus answered them, "Is it not written in your Law: 'I have said you are gods'? Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’
35 If he called them 'gods,' to whom the word of my Father came—and Scripture cannot be broken, Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,
36 what about the one the Father set apart and sent into the world? Why accuse me of blasphemy for saying, 'I am the Son of our Father'? nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’
37 "If I am not doing the works of my Father, then do not believe me. Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga.
38 But if I do them, even if you won't believe me, believe the works, so you'll know and keep knowing the Father is in me, and I in the Father." Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.”
39 Again they tried to seize him, but he escaped their grasp. Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.
40 Jesus then went back across the Jordan, to the place where John had first been baptizing, and stayed there. Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko
41 Many came to him, saying, "John performed no sign, but all John said about this man was true." ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.”
42 And in that place many believed in him. Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]