Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 After this there was a feast of the Jews, and Jesus went up to Jerusalem. Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda.
2 By the Sheep Gate in Jerusalem is a pool with five covered porches, called Bethesda in Aramaic. Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu.
3 In these lay a multitude of the sick—blind, lame, and paralyzed. Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo.
4 Not in this edition Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.
5 One man was there who had been sick for thirty-eight years. Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38.
6 Seeing him lying there and knowing he had already been there a long time, Jesus asked, "Do you want to be healed?" Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
7 The sick man answered him, "Sir, I have no one to put me in the pool once the water stirs—while I'm on my way, someone else gets in first." Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
8 Jesus said to him, "Get up, take up your mat, and walk." Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.”
9 At once the man became well, picked up his mat, and walked. That day was the Sabbath. Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda. Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.
10 So the Jews told the healed man, "It's the Sabbath—you're not allowed to carry your mat." Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
11 He answered them, "The man who healed me told me, 'Take up your mat and walk.'" Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine, ‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’ ”
12 They asked him, "Who is the man who told you, 'Take it up and walk'?" Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’ ”
13 But the healed man didn't know who it was, since Jesus had slipped away into the crowd there. Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
14 Later Jesus found him in the temple and said, "You are healed now. Stop sinning, or something worse may happen to you." Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.”
15 The man went away and told the Jews that it was Jesus who had made him well. Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
16 And so the Jews began persecuting Jesus, because he was doing these things on the Sabbath. Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda.
17 But Jesus answered them, "My Father is working until now, and I too am working." Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.”
18 So the Jews sought even more to kill him: he not only broke the Sabbath but called our Father his own Father, making himself equal to him. Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
19 So Jesus said to them, "Truly, truly, I tell you: the Son can do nothing on his own, but only what he sees the Father doing. Whatever the Father does, the Son does the same. Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso.
20 "For the Father loves the Son and shows him everything he does; he will show him greater works than these, so you will be amazed. Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa.
21 For as the Father raises the dead and gives life, so the Son too gives life to anyone he wants. Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna.
22 For the Father judges no one, but has entrusted all judgment to the Son, Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo,
23 so everyone honors the Son as they honor the Father; whoever doesn't honor the Son doesn't honor the Father who sent him. kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
24 Truly, truly, I tell you: whoever hears my word and believes the one who sent me has eternal life and won't face judgment—they have passed from death to life. “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.
25 Truly, truly, I tell you, an hour comes, and is now here, when the dead will hear the voice of the Son of our Father, and those hearing will live. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.
26 For as the Father has life in himself, he gave the Son to also have life in himself. Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana.
27 And he has given him authority to execute judgment, because he is the Son of Man. Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
28 Don't be astonished at this—an hour is coming when everyone in the tombs will hear his voice, “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake
29 and come out—those who did good, to the resurrection of life; those who did evil, to the resurrection of judgment. ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.
30 By myself I can do nothing. I judge as I hear; my judgment is fair, because I seek not my own will but the will of the One who sent me. Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
31 "If I testify about myself, my testimony is not valid. “Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona.
32 There is another who testifies about me, and I know his testimony about me is true. Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
33 You sent messengers to John, and he has testified to the truth. “Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona.
34 Not that I accept human testimony, but I say these things so that you may be saved. Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe.
35 John was a burning, shining lamp, and you were willing to rejoice briefly in his light. Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
36 But I have testimony greater than John's: the works my Father gave me to finish—the very works I'm doing—testify that my Father sent me. “Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine.
37 And my Father who sent me has himself testified about me. You've never heard his voice or seen his form, Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake,
38 and you don't have his word remaining in you, since you don't believe the one he sent. kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma.
39 You search the Scriptures, thinking they hold eternal life—yet they themselves testify about me, Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.
40 yet you refuse to come to me so that you may have life. Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
41 I do not accept glory from people, “Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu
42 but I know you—that you do not have the love of our Father within you. koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu.
43 I have come in my Father's name, and you don't receive me; if another comes in his own name, you'll receive him. Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira.
44 How can you believe, when you accept glory from one another and don't seek the glory from the only God? Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
45 Don't think I will accuse you before my Father. Moses, in whom you've hoped, accuses you. “Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu.
46 For if you believed Moses, you would believe me, because he wrote about me. Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine.
47 But if you do not believe his writings, how will you believe my words?" Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]