Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 4 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 So when Jesus knew the Pharisees heard he was making and baptizing more disciples than John. Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane,
2 (though Jesus himself was not baptizing, but his disciples were), (ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake).
3 he left Judea and went back to Galilee. Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya.
4 And he had to pass through Samaria. Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya.
5 So he came to a town of Samaria called Sychar, near the field Jacob gave his son Joseph. Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.
6 Jacob's well was there. Jesus, tired from the trip, sat down at the well—about noon. Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana.
7 A woman of Samaria came to draw water. Jesus said to her, "Give me a drink." Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye, “Kodi ungandipatse madzi akumwa.”
8 (For his disciples had gone into the town to buy food.). (Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).
9 The Samaritan woman said, "You're a Jew; why ask me, a Samaritan woman, for a drink?" (Jews don't associate with Samaritans.). Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).
10 Jesus answered her, "If you knew our Father's gift, and who asks you, 'Give me a drink,' you'd have asked him, and he'd have given you living water." Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”
11 The woman said to him, "Sir, you have nothing to draw with, and the well is deep. Where then do you get this living water? Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti?
12 Are you greater than our father Jacob, who gave us the well, drank from it himself, with his sons and livestock?" Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”
13 Jesus said to her, "Everyone who drinks of this water will be thirsty again, Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu,
14 but whoever drinks the water I give him will never thirst again; that water will become in him a spring of water welling up to eternal life." koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”
15 The woman said to him, "Sir, give me this water, so I won't get thirsty or come here to draw water." Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.”
16 Jesus said to her, "Go, call your husband, and come back here." Iye anamuwuza kuti, “Pita kayitane mwamuna wako ndipo ubwere naye.”
17 The woman answered, "I have no husband." Jesus told her, "You're right to say you have no husband. Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.” Yesu anati kwa iye, “Wakhoza ponena kuti ulibe mwamuna.
18 For you've had five husbands, and the man you have now isn't your husband. You've spoken the truth." Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.”
19 The woman said to him, "Sir, I see that you are a prophet. Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri.
20 Our fathers worshiped on this mountain, but you say Jerusalem is where people must worship." Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”
21 Jesus told her, "Woman, believe me: an hour is coming when you'll worship the Father neither on this mountain nor in Jerusalem. Yesu anati, “Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu.
22 You worship what you don't know; we worship what we know—salvation comes from the Jews. Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda.
23 But a time is coming, and now is, when true worshipers worship the Father in spirit and truth—for the Father seeks such worshipers. Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna.
24 The Father is spirit, and those who worship him must worship in spirit and truth." Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”
25 The woman said to him, "I know Messiah—the one called Christ—is coming. When he comes, he will tell us everything." Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.”
26 Jesus said to her, "I am he—the one speaking to you." Ndipo Yesu anamuwuza kuti, “Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.”
27 Just then his disciples returned, amazed he was talking with a woman. Yet no one said, "What do you want?" or, "Why talk with her?" Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?”
28 So the woman left her water jar and went back to town and said to the people, Kenaka mayiyo anasiya mtsuko wamadzi, nabwerera ku mzinda ndipo anati kwa anthu,
29 "Come, see a man who told me everything I ever did. Could this be the Christ?" “Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?”
30 They left the town and were coming to him. Iwo anatuluka mʼmudziwo ndi kupita kumene kunali Iye.
31 Meanwhile the disciples were urging him, "Rabbi, eat." Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.”
32 But he said to them, "I have food to eat that you know nothing about." Koma Iye anawawuza kuti, “Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa.”
33 So the disciples said to one another, "Has anyone brought him something to eat?" Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?”
34 Jesus said to them, "My food is doing the will of the one who sent me and finishing his work. Yesu anati, “Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake.
35 Don't you say, 'Four months more, then harvest comes'? Look, I tell you: raise your eyes, see the fields—white for harvest. Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe.
36 Already the harvester earns wages, gathering fruit for eternal life, so that planter and harvester may rejoice together. Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi.
37 For here the saying holds true: 'One plants and another harvests.' Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona.
38 I sent you to reap what you didn't work for. Others worked, and you have entered into their labor." Ine ndinakutumani kukakolola zimene simunagwirire ntchito. Ena anagwira ntchito yolemetsa ndipo inu mwatuta phindu la ntchito yawo.”
39 Many Samaritans from that town believed in him because of the woman's testimony: "He told me everything I ever did." Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.”
40 When the Samaritans came to him, they asked him to stay with them; he stayed two days. Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri.
41 And many more believed because of his word. Ndipo chifukwa cha mawu ake, ena ambiri anakhulupirira.
42 They told the woman, "It is no longer because of what you said that we believe—we've heard for ourselves, and we know this man truly is the Savior of the world." Iwo anati kwa mayiyo, “Ife sitikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha, koma tsopano ife tadzimvera tokha, ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndithu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.”
43 After the two days he departed from there for Galilee. Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya.
44 (For Jesus himself had testified that a prophet has no honor in his own hometown.). (Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake).
45 When he arrived in Galilee, the Galileans welcomed him, having seen all he did in Jerusalem at the feast—they too had gone to the feast. Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.
46 He went again to Cana in Galilee, where he had turned water to wine. A royal official's son was sick at Capernaum. Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo.
47 Hearing that Jesus had come from Judea to Galilee, he went to him and begged him to come down and heal his son, who was about to die. Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.
48 So Jesus said to him, "Unless you people see signs and wonders, you will never believe." Yesu anawawuza iwo kuti, “Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira.”
49 The royal official said to him, "Sir, come down before my child dies." Nduna ya mfumuyo inati, “Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe.”
50 Jesus said to him, "Go; your son will live." The man believed what Jesus told him and left. Yesu anayankha kuti, “Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka.
51 As he was going down, his servants met him and told him that his boy was living. Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira.
52 So he asked them the hour he improved, and they said, "Yesterday at the seventh hour, the fever left him." Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, “Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri.”
53 So the father knew this was the hour when Jesus told him, "Your son will live." He and his whole household believed. Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, “Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.
54 This was now the second sign that Jesus did when he had come from Judea to Galilee. Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]