Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

John 6 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 After this, Jesus crossed the Sea of Galilee, also called the Sea of Tiberias. Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya),
2 A large crowd followed him, because they saw the signs he performed on the sick. ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala.
3 Jesus went up on the mountainside and sat down there with his disciples. Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake.
4 Now the Passover, the feast of the Jews, was near. Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi.
5 Looking up, Jesus saw a large crowd approaching and asked Philip, "Where can we buy bread for these people to eat?" Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?”
6 He said this to test Philip, for he himself already knew what he was going to do. Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
7 Philip answered him, "200 days' wages of bread isn't enough for each of them to get a little." Filipo anamuyankha Iye kuti, “Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!”
8 One of his disciples, Andrew, Simon Peter's brother, said to him, Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati,
9 "A boy here has five barley loaves and two fish—but what's that for so many?" “Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?”
10 Jesus said, "Have the people sit down." Much grass grew there, so about 5,000 men sat down. Yesu anati, “Awuzeni anthuwa akhale pansi.” Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000.
11 Jesus then took the loaves, gave thanks, and distributed them to those seated; likewise with the fish, as much as they wanted. Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
12 When they were full, he told his disciples, "Gather the leftover pieces, so nothing is lost." Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.”
13 So they gathered the fragments left over from the five barley loaves after the people ate, filling twelve baskets. Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.
14 So when the people saw the sign he did, they said, "This really is the Prophet coming into the world!" Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.”
15 Knowing they meant to come and seize him to make him king, Jesus withdrew again to the mountain alone. Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha.
16 When evening came, his disciples went down to the sea, Pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira ku nyanja,
17 got in a boat and headed across the sea to Capernaum. It was already dark, and Jesus had not yet reached them. kumene iwo analowa mʼbwato ndi kuyamba kuwoloka nyanja kupita ku Kaperenawo. Tsopano kunali kutada ndipo Yesu anali asanabwerere kwa iwo.
18 A strong wind was blowing, and the sea grew rough. Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa.
19 After rowing three or four miles, they saw Jesus walking on the water, approaching the boat, and were afraid. Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha.
20 But he said to them, "It is I; do not be afraid." Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.”
21 So they were glad to take him into the boat, and instantly it reached the shore they were heading toward. Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita.
22 The next day, the crowd remaining on the far shore saw that only one boat had been there, that Jesus had not boarded it with his disciples, but that his disciples had gone off alone. Pa tsiku lotsatira gulu la anthu limene linatsala kumbali ina yanyanjayo linaona kuti panali bwato limodzi lokha, ndipo kuti Yesu sanalowe mʼbwatomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzirawo anapita okha.
23 Other boats came from Tiberias near the place where they ate bread after the Lord gave thanks. Kenaka mabwato ena ochokera ku Tiberiya anafika pafupi ndi pamalo pamene anthu anadya buledi Ambuye atayamika.
24 So when the crowd saw Jesus and his disciples weren't there, they got in boats and went to Capernaum to look for Jesus. Nthawi yomwe gulu la anthu linaona kuti Yesu kapena ophunzira ake sanali pamenepo, ilo linalowanso mʼmabwatowo ndi kupita ku Kaperenawo kukamufunafuna Yesu.
25 Finding him across the sea, they asked, "Rabbi, when did you get here?" Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?”
26 Jesus answered them, "Truly, truly, I tell you: you seek me not because you saw signs, but because you ate the loaves and were filled. Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta.
27 Don't work for food that spoils, but for food that lasts to eternal life, which the Son of Man will give you. For on him our Father has set his seal." Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”
28 Then they said to him, "What must we do to be doing the works of our Father?" Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”
29 Jesus answered them, "This is our Father's work: that you believe in the one he sent." Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”
30 So they asked him, "What sign will you give, so we may see and believe you? What work will you do? Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani?
31 Our ancestors ate manna in the wilderness, as it is written: 'He gave them bread from heaven to eat.'" Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ”
32 Jesus told them, "Truly, truly, I tell you: Moses didn't give you the bread from heaven—my Father gives you the true bread from heaven. Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.
33 For the bread of our Father is he who comes down from heaven and gives the world life." Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”
34 So they said to him, "Lord, give us this bread always." Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.”
35 Jesus told them, "I am the bread of life. Whoever comes to me will never hunger; whoever believes in me will never thirst. Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
36 But as I told you, you have seen me and still do not believe. Monga ndakuwuzani kale, ngakhale kuti mwandiona simukukhulupirirabe.
37 All the Father gives me will come to me, and the one who comes to me I will never drive away. Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja.
38 For I came down from heaven not to do my own will, but the will of him who sent me. Pakuti Ine ndinatsika kuchokera kumwamba osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine.
39 This is the will of him who sent me: that I lose none of all he has given me, but raise them up on the last day. Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza.
40 For this is the will of my Father: that everyone who looks to the Son and believes in him should have eternal life, and I will raise them up on the last day." Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
41 So the Jews grumbled about him because he said, "I am the bread that came down from heaven." Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.”
42 They said, "Isn't this Jesus, Joseph's son, whose father and mother we know? How can he now say, 'I have come down from heaven'?" Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’ ”
43 Jesus answered them, "Stop grumbling among yourselves. Yesu anayankha kuti, “Musangʼungʼudze pakati panu.”
44 "No one can come to me unless the Father who sent me draws him, and I will raise him on the last day. Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
45 It is written in the Prophets: 'And they will all be taught by our Father.' Everyone who has heard and learned from the Father comes to me. Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine.
46 Not that anyone has seen the Father except the one from him; he has seen the Father. Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate.
47 Truly, truly, I tell you, whoever believes has eternal life. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha.
48 I am the bread of life. Ine ndine chakudya chamoyo.
49 Your ancestors ate the manna in the wilderness, yet they died. Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa.
50 This is the bread that comes down from heaven, so anyone may eat it and not die. Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe.
51 I am the living bread come down from heaven. Whoever eats this bread will live forever. The bread I will give is my flesh, for the life of the world." Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”
52 Then the Jews argued sharply among themselves, "How can this man give us his flesh to eat?" Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?”
53 Jesus told them, "Truly, truly, I tell you, unless you eat the flesh of the Son of Man and drink his blood, you have no life in yourselves. Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
54 Whoever feeds on my flesh and drinks my blood has eternal life, and I will raise him on the last day. Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
55 For my flesh is true food, and my blood is true drink. Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni.
56 Whoever feeds on my flesh and drinks my blood remains in me, and I in him. Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye.
57 As the living Father sent me and I live because of the Father, so whoever feeds on me will live because of me. Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.
58 This is the bread that came down from heaven. It is not like the bread your ancestors ate and still died. Whoever feeds on this bread will live forever." Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.”
59 He said these things while teaching in the synagogue at Capernaum. Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo.
60 On hearing it, many of his disciples said, "This is a hard teaching. Who can accept it?" Pakumva izi ambiri a ophunzira ake anati, “Ichi ndi chiphunzitso chovuta. Angachilandire ndani?”
61 Aware that his disciples were grumbling about this, Jesus said to them, "Does this offend you? Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani?
62 "Then what if you see the Son of Man ascending to where he was before? Nanga mutaona Mwana wa Munthu akukwera kupita kumene Iye anali poyamba!
63 The Spirit gives life; the flesh helps nothing. The words I have spoken to you are spirit and life. Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.
64 But some of you don't believe." For Jesus knew from the start who didn't believe, and who would betray him. Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye.
65 And he said, "This is why I told you: no one can come to me unless the Father enables him." Iye anapitiriza kunena kuti, “Ichi ndi chifukwa chake ndinakuwuzani kuti palibe wina angabwere kwa Ine pokhapokha Atate atamuthandiza.”
66 From this time many of his disciples turned back and no longer walked with him. Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.
67 So Jesus asked the Twelve, "Do you want to leave too?" Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, “Kodi inu mukufuna kuchokanso?”
68 Simon Peter answered him, "Lord, to whom should we go? You have the words of eternal life. Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha.
69 We have believed and known you are the Holy One of our Father." Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.”
70 Jesus answered them, "Have I not chosen you, the Twelve? Yet one of you is a devil." Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi Ine sindinakusankheni inu khumi ndi awiri? Komabe mmodzi wa inu ndi mdierekezi.”
71 He meant Judas, son of Simon Iscariot, one of the Twelve, who was about to betray him. (Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]