Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 52 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Wake up, wake up, put on your strength, Zion; put on your beautiful garments, Jerusalem, the holy city; for the uncircumcised and the unclean will never enter you again. Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni, vala zilimbe. Vala zovala zako zokongola, iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika. Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa sadzalowanso pa zipata zako.
2 Shake yourself from the dust and arise; take your throne, Jerusalem; free yourself from the bonds around your neck, captive daughter of Zion. Sasa fumbi lako; imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu. Inu omangidwa a ku Ziyoni, masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.
3 For this is what our Father says: "You were sold for nothing, and you will be redeemed without money." Pakuti Yehova akuti, “Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani, choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”
4 For this is what the Sovereign Father says: "At first my people went down to Egypt to live there as foreigners, and Assyria oppressed them for nothing. Pakuti Ambuye Yehova akuti, “Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto; nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”
5 "And now, what is this?" declares our Father, "seeing that my people are taken away for nothing? Their rulers wail," declares our Father, "and continually, all day long, my name is despised. Tsopano Ine Yehova ndikuti, “Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu, amene amawalamulira amawanyoza,” akutero Yehova. “Ndipo tsiku lonse, akungokhalira kuchita chipongwe dzina langa.
6 Therefore my people will know my name; therefore in that day they will know that it is I who speak; here I am." Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa; kotero adzadziwa kuti ndi Ine amene ndikuyankhula, Indedi, ndine.”
7 How beautiful on the mountains are the feet of the messenger who brings good news, who proclaims peace, who brings good news of good things, who proclaims salvation, who says to Zion, "Your Father reigns!" Ngokongoladi mapazi a amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri. Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere, chisangalalo ndi chipulumutso. Iwo akubwera kudzawuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wako ndi mfumu!”
8 Listen! Your watchmen lift up their voices; together they shout for joy, for with their own eyes they will see our Father returning to Zion. Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo; akuyimba pamodzi mwachimwemwe. Popeza akuona chamaso kubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.
9 Burst into song together, you ruins of Jerusalem, for our Father has comforted his people; he has redeemed Jerusalem. Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe, inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu.
10 Our Father has bared his holy arm in the sight of all the nations, and all the ends of the earth will see the salvation of our Father. Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika pamaso pa anthu a mitundu yonse, ndipo anthu onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
11 Leave! Leave! Go out from there; touch no unclean thing; go out from among them; purify yourselves, you who carry the vessels of our Father. Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko! Musakhudze kanthu kodetsedwa! Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova tulukanimo ndipo mudziyeretse.
12 For you will not go out in haste, nor will you flee; for our Father will go before you, and our Father will be your rear guard. Koma simudzachoka mofulumira kapena kuchita chothawa; pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.
13 See, my servant will act wisely; he will be raised and lifted up and highly exalted. Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake adzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
14 Just as many were appalled at him—his appearance was so disfigured beyond that of any man, and his form beyond that of any human being, Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu. Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
15 so he will sprinkle many nations; kings will shut their mouths because of him. For what they were not told, they will see, and what they had not heard, they will understand. Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye. Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona, ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]