Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 38 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 In those days Hezekiah fell mortally ill. The prophet Isaiah son of Amoz came to him and said, "This is what our Father says: Put your house in order, for you will die; you will not recover." Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”
2 Then Hezekiah turned his face to the wall and prayed to our Father, Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti,
3 and said, "Please, my Father, remember how I walked faithfully before you with a whole heart, and did what was good in your eyes." Hezekiah wept bitterly. “Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.
4 Then the word of our Father came to Isaiah: Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti:
5 "Go tell Hezekiah, 'This is what our Father says, the Father of your ancestor David: I have heard your prayer and seen your tears. I am adding fifteen years to your life.' “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako.
6 I will rescue you and this city from the king of Assyria; I will defend this city. Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.
7 "This is your sign from our Father that he will do what he has promised: “ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza:
8 Look, I'll turn back the shadow ten steps the sun has descended on Ahaz's stairway." So the sun turned back the ten steps it had gone down. Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.
9 A writing of Hezekiah king of Judah, after his illness and recovery: Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:
10 I said, "In the middle of my days I must go through the gates of the grave; I am robbed of the rest of my years." Ine ndinaganiza kuti ndidzapita ku dziko la akufa pamene moyo ukukoma.
11 I said, "I will not see our Father himself in the land of the living; I will look on humanity no longer, among those who dwell in this passing world. Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova, mʼdziko la anthu amoyo, sindidzaonanso mtundu wa anthu kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
12 My dwelling is pulled up and carried off from me like a shepherd's tent. I have rolled up my life like a weaver; he cuts me off from the loom; from day to night you bring me to an end. Nyumba yanga yasasuka ndipo yachotsedwa. Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga, ngati munthu wowomba nsalu; kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
13 I waited quietly until morning, but like a lion he breaks all my bones; from day to night you bring me to an end. Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa; koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango, ndipo mwakhala mukundisiya.
14 Like a swift or a crane I chirp; I moan like a dove. My eyes grow weary looking upward. O Sovereign Father, I am hard-pressed; be my guarantee of safety!" Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba, ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula. Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga. Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”
15 What can I say? He has spoken to me, and he himself has done it. I will walk slowly all my years because of the bitterness of my soul. Koma ine ndinganene chiyani? Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi. Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga, ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
16 O Sovereign Father, by such things people live, and in all of them is the life of my spirit. So restore me to health and let me live! Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu. Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu. Munandichiritsa ndi kundikhalitsa ndi moyo.
17 Surely it was for my own good that I suffered such bitterness. In your love you held back my life from the pit of destruction, for you have thrown all my sins behind your back. Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere kuti ndikhale ndi moyo; Inu munandisunga kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko chifukwa mwakhululukira machimo anga onse.
18 For the grave cannot praise you; death cannot sing your praise. Those who go down to the pit cannot hope for your faithfulness. Pakuti akumanda sangathe kukutamandani, akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani. Iwo amene akutsikira ku dzenje sangakukhulupirireni.
19 The living, the living—they praise you, as I do this day; the father makes your faithfulness known to the children. Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani, monga mmene ndikuchitira ine lero lino; abambo amawuza ana awo za kukhulupirika kwanu.
20 Our Father will save me, and we will play my songs on stringed instruments all the days of our lives, in the house of our Father. Yehova watipulumutsa. Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe masiku onse a moyo wathu mʼNyumba ya Yehova.
21 Isaiah had said, "Let them take a fig cake, apply it to the boil, and he'll recover." Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”
22 Hezekiah had asked, "What is the sign that I will go up to the house of our Father?" Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]