Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 37 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 When King Hezekiah heard it, he tore his clothes, put on mourning clothes, and went into the house of our Father. Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova.
2 He sent Eliakim the palace administrator, Shebna the scribe, and senior priests in sackcloth to the prophet Isaiah son of Amoz. Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi.
3 They told him, "Hezekiah says: Today is a day of distress, reproof, and contempt. Children have come to birth, but no strength to deliver them. Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’
4 Perhaps your Father will hear the words of the Rabshakeh, whom his master the king of Assyria sent to mock the living Father, and will rebuke the words he heard. So lift up a prayer for the surviving remnant." Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”
5 When the servants of King Hezekiah came to Isaiah, Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya,
6 Isaiah told them, "Tell your master: our Father says: Don't fear the words you heard, with which the king of Assyria's servants insulted me. Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine.
7 Look, I will put a spirit in him, so he hears a report, returns to his own land, and there I will make him fall by the sword." Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
8 The Rabshakeh returned and found the Assyrian king fighting Libnah, having heard the king had left Lachish. Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9 The king heard about Tirhakah king of Cush: "He has come out to fight you." Hearing this, he sent messengers to Hezekiah: Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa:
10 "Tell Hezekiah king of Judah: Don't let the God you trust deceive you, saying, 'Jerusalem won't fall to Assyria's king.' “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’
11 You have heard what the kings of Assyria did to all lands, destroying them completely. And you—will you be rescued? Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka?
12 Did the nations' gods rescue those my fathers destroyed: Gozan, Haran, Rezeph, and Eden's people in Telassar? Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi?
13 Where is the king of Hamath, the king of Arpad, the king of Sepharvaim, Hena, and Ivvah?" Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”
14 Hezekiah took the letter from the messengers, read it, went up to our Father's house, and spread it out before our Father. Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova.
15 And Hezekiah prayed to our Father, saying: Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova:
16 "Father of heaven's armies, the Father of Israel, enthroned above the cherubim—you alone are our Father over all earth's kingdoms; you made the heavens and the earth. “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
17 Bend down, our Father, and hear; open your eyes, our Father, and see; hear all Sennacherib's words sent to mock the living Father. Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.
18 True, our Father, the kings of Assyria have destroyed all the nations and their lands, “Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo.
19 and threw their gods into the fire—not gods but work of human hands, wood and stone; so they destroyed them. Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu.
20 Now, our Father, save us from his hand, so all earth's kingdoms may know you alone are our Father." Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”
21 Then Isaiah son of Amoz sent to Hezekiah: This is what the Father of Israel says: Because you prayed to me about Sennacherib king of Assyria, Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.
22 this is the word that our Father has spoken against him: "She despises you, she scorns you—the virgin daughter of Zion; behind you she shakes her head—the daughter of Jerusalem. Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa: “Mwana wamkazi wa Ziyoni akukunyoza ndi kukuseka. Mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
23 Whom have you mocked and reviled? Against whom have you raised your voice and lifted your eyes in pride? Against the Holy One of Israel! Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani? Kodi iwe wafuwulira ndi kumuyangʼana monyada ndani? Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!
24 By your servants you have mocked the Sovereign Father, and you have said, 'With my many chariots I have gone up to the heights of the mountains, to the far reaches of Lebanon. I cut down its tallest cedars, its choicest cypresses; I came to its remotest height, its densest forest. Kudzera mwa amithenga ako iwe wanyoza Ambuye. Ndipo wanena kuti, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndafika pamwamba pa mapiri, pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni. Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri, ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini. Ndafika pa msonga pake penipeni, nkhalango yake yowirira kwambiri.
25 I dug wells and drank water; with the sole of my foot I dried up all the streams of Egypt.' Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo ndi kumva madzi akumeneko ndi mapazi anga ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’
26 Have you not heard? Long ago I did it; from days of old I planned it. Now I have made it happen, that you should turn fortified cities into heaps of ruins. “Kodi sunamvepo kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale? Ndinazikonzeratu masiku amakedzana; tsopano ndazichitadi, kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa kukhala milu ya miyala.
27 Their inhabitants, stripped of their strength, were dismayed and put to shame; they were like plants of the field, like tender grass, like grass on the rooftops, withered before it can grow. Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu, ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi. Anali ngati mbewu za mʼmunda, ngati udzu wanthete, ali ngati udzu omera pa denga, umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.
28 But I know when you sit down, when you go out, and when you come in, and when you rage against me. “Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe; ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa, ndiponso momwe umandikwiyira Ine.
29 Because you rage against me, and your arrogance has reached my ears, I will put my hook in your nose and my bridle in your mouth, and I will turn you back by the way you came. Chifukwa umandikwiyira Ine ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako, ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa njira yomwe unadzera pobwera.
30 "This is your sign: this year you'll eat what grows on its own, the second year what springs from that, the third year sow and reap, plant vineyards and eat their fruit. “Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi: “Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha, ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha, koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola, mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.
31 And the surviving remnant of the house of Judah will again take root downward and bear fruit upward. Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.
32 For out of Jerusalem will go a remnant, and out of Mount Zion a band of survivors. The zeal of the Father of heaven's armies will accomplish this. Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala, ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka. Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
33 So our Father says about Assyria's king: He will not enter this city or shoot an arrow here, confront it with a shield, or build a siege ramp against it. “Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya: “Iye sadzalowa mu mzinda umenewu kapena kuponyamo muvi uliwonse. Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
34 He will return the way he came; he will not come into this city, declares our Father. Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera; sadzalowa mu mzinda umenewu,” akutero Yehova.
35 For I will defend this city to save it, for my own sake and for the sake of David my servant." “Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu, chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”
36 Then our Father's messenger went out and struck down 185,000 in the Assyrian camp; when people rose early in the morning, there were dead bodies everywhere. Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse!
37 So Sennacherib king of Assyria broke camp and went home, and he stayed at Nineveh. Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.
38 As he worshiped in the temple of his god Nisroch, his sons Adrammelech and Sharezer struck him with the sword and fled to Ararat. His son Esarhaddon ruled in his place. Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]