Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

James 5 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

Onyo kwa wandhu wopata

1Chipano, niveleni anyiimwa wandhu wopata, lilani ni kudandaula ndande ya mavuto yayo siyakukomaneni posachedwa! 2Chuma chanu chaola, ni njhalu zanu zamtengo waukulu zadyedwa ni viswe. 3Dahabu zanu ni madini yanu ya feza vawanangika, ni kuwanangika kwake sikulangize umo mtumila kuipa kupata kwanu, ni sikuwanage matupi yanu ngati moto umo ubuchila. Mwajhiunjikila chuma masikuyano yothela kwa. 4Simudaapache mkokolo wao wandhu yawo achita njhito mminda mwanu. Velani chipano mvekelo wa kulila kwawo! Ambuye Mnungu ambhavu avela chililo chao. 5Mwakhala pa pano jhiko lapanjhi kwa kujhikondwelecha mwachinawene ni kuchita kila chindhu icho muchifuna. Ni chipano mwakhala ngati zinyama izo zajhumbala izo zipita kuphedwa. 6Mwamlamula ni kumuipha mundhu osalakwe, uyo siwadakuchucheni.

Kulimbamtima ni kupembhela

7Chipano, achabale wanga, limbanimitima mbaka yapo saabwele Ambuye. Kumbukilani mlimi yapo walindilia vipacho vake mbaka vikule. Walindilila kwakulimbamtima kuyambila vula ya jhinja mbaka vula yammathelo. 8Chinchijha, namwenjho mukhale wolindilila kwakulimbamitima popande kulema. Pakuti siku la kujha Ambuye lawandikila.

9Achabale wanga msidatoolilana, dala simudalamulidwa ni Mnungu. Pakuti mlamuli wawandikila kul owa. 10Achabale wanga wokondedwa, kumbukilani nghani za alosi a wajha adakamba uthenga mmalo mwa Ambuye. Anyiiwo adalimbamtima ata ngati adakumana nimavuto yochuluka. Chimwecho, achabale yawo mumkhulupilila Yesu, namwenjho mwachatize anyiiwo. 11Tatana achamenewo, apachidwa mwawi adalimbamtima. Mudavela nghani za kulimbamtima kwa Ayubu, ni mujhiwa umo Ambuye adamchitila pothelapake. Pakuti Ambuye ajhala wabwino ni walisungu.

12Kupitilila vindhu vonjhe, achabale wanga, Musadalumbila pakuchula kumwamba, kapina jhiko lapanjhi, kapina kulumbilila kwa chindhu china chilichonjhe. “Yetu” yanu ni ikhale “Yetu” ya zene ni “notho” yanu ikhale notho zene. Mkasiya kuchita chimwecho Mnungu siwakulamuleni.

13Bwanji, walipo mundhu pakati panu uyo wali ni mavuto? Wafunika kupembhela. Bwanji, walipo uyo wokondwa pakati panu? Wfunika wayimbe nyimbo zakumtamanda Mnungu. 14Walipo wodwala pakati panu? Mwatane wakulu agulu lawomkhulupilila Yesu kuti ajhe kumpembhelela wodwalayo ni kumnyeka mafuta mjhina la Ambuye Yesu. 15Ndipo mapembhelo ilo lachitika kwa chikhulupi silimulamiche mundhu wodwalayo, ni Ambuye samchite swasangalale. Ngati wadachita machimo, Mnungu siwamlekelele. 16Chimwecho, lapilanani voipa vanu ivo mwachitilana dala mlekelelane, mujhipembhelelana kuti mulamichidwe. Mapembhelo ya mundhu wovomelezeka kwa Mnungu yali ni mbavu ni silipita pachajhe. 17Eliya wadali mundhu ngati umo tili ife. Iye wadapembhela popande kulema kuti vula siidanya pajhiko, ni vula siidanyedi kwa vyaka vitatu ni miezi sita. 18Ndipo wadapembhelanjho kuti mvula inye, vula idanya kuchokela kumlengalenga, jhiko lapanjhi lidamelecha mimela.

19Abale wanga, ngati mmojhi wanu wasokelela pakusiyana uthenga wa uzene, anyiimwe mbwezeni kwa Mnungu. 20Kumbukilani kuti iye uyo wambweza mundhu uyo wasokelelayo kuchokela ku njila zake zoipa, siwaupulumuche mzimu wa ochimwa mmeneyo kuchokela kunyifa. Ni Mnungu siwamlekelele machimo yake.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]