Skip to content
The Believer's Library

Nyanja Tanzania Bible Version

Jude 1 NTNYBL2025

Side by side with the Father's Heart Bible™

1Kalata ii ichoka kwa ine Yuda, mtumiki wa Yesu Kilisito, inenjho mbale wake Yakobo. nikulembelani kalata iyi anyiimwe mwatanidwa ni kukondedwa ni Mnungu Atate, ni kukusungani mbaka Kilisito Yesu yapo siwabwele.

2Nimpembha Mnungu wayendekele kukulengelani Lisungu ni wayendekele kukupachani mtendele ni kukondana kwanu kuyendekele kuchuluka.

Woyaluza onyenga

3Achabale wanga wokondedwa, nidakhumbila kupunda kukulembelani kwa nghani za mujha Mnungu watiombola ife taonjhe. Nambho nidaona kuti nifunika nikulembeleni kalata ino dala nikupembeni muyendekele kusunga chikhulupililo icho Mnungu wapacha wandhu wake oyela mala kamojhipe kwa ndhawi zonjhe. 4Pakuti kuli wandhu wina, yawo sadamkhulupile Mnungu, alowa kwa chisisi pakati panu. Wandhu amenewo ndande ya phindu lawo ang'anamula uthenga wa ubwino wa Mnungu pakuchita vichito vawo voipa, ni kumkana Yesu Kilisito uyo wali mchogolelo ni Ambuye wathu, nambho malembo ya Mnungu yadatholosa kuyambila kale nghani za lamulo ilo lalindila wandhu amenewo.

5Ata ngati mwajhiwa vonjhevi, nifuna nikukumbucheni kuti, Ambuye adaalamicha wandhu wake kuchokela mujhiko la Misili, nambho wadaayomwecha wandhu yawo sadakhulupilile. 6Nao atumiki akumwamba Amnungu yawo sadagwamike ni malo yawo, ni adayasiya malo yawo yayo amakhala, anyiyawa Mnungu wamanga mumdima ni maunyolo ya muyaya dala alamulidwe siku lijha lalikulu. 7Kumbukilani, mijhi ijha ya Sodoma ni Gomola ni mijhi ina ili pafupi pawo, wandhu amijhi imeneyo adachita ngati atumiki akumwamba Amnungu, ni adakomana chithupi kumbuyo kwa maumbidwe, adapachidwa lamulo la moto wamuyaya, dala ikhale chifani icho sichichokele kwa wandhu yao sachite chimwecho.

8Chimwecho nde umo ali wandhu amenewo, maganizo yawo yachogoza kudecha mathupi yawo, adelela ulamulilo wa Mnungu ni kuvitukwana voumbidwa va Mnungu vili kumwamba vili ni umoyo. 9Nambho ata Mikayeli, mtumiki wamkulu wa kumwamba wa Mnungu, siwadamukambile mawu yachipongwe Satana yapo amayambililana thupi la Musa, nambho wadakamba, “Ambuye wene ni akukalipile.” 10Nambho wandhu anyiyawa atukwana ata vindhu valivonjhe ivo savijhiwa. Sayomwechedwe kwa vindhu vivijha avijhiwa kwa maganizo yawo, ngati umo zili zinyama izo zilibe njelu. 11Savutike wandhu achameneo ndande yakuchata njila ya Kaini. Anyiiwo athamangila chuma, achita machimo yayajha ngati yajha wadachita Balamu. Akana kumvela Mnungu ngati umo wadachitila Kola. Chimwecho, Mnungu siwawanange. 12Kwamapokoso yawo yalibe ulemu, ni kwa kujhikondelela kwawo achina wene, wandhu amenewo ali ngati mabanga ya ukazuzu pa chakudya icho mkudya kwa kukondwela, Ali ngati mitambo yopande mvula iyo ivululuchidwa ni mbhepo. Ali ngati mitengo iyo yauma iyo ilibe vipacho iyo yazulidwa ni kufelatu. 13Anyiiwo ali ngati mafunde yakali ya panyanja ya mchele, nivichito vao vanjhoni yachoka ngati mathovu. Ali ngati ndhondwa izo ziyendayenda, Mnungu waakonjela malo yawo yamdima, uko iye siwaike kumeneko muyaya.

14Enoki, uyo wali mundhu wa mbadwa wasaba kuchoka Adamu, wadalosa nghani za wandhu achamenewo kuti, “Vechelani Ambuye atokujha ni gulu lalikulu la atumiki wake woyela akumwamba, 15kwalamula wandhu wonjhe, ni kwalanga wandhu wonjhe yawo samkhulupilila Mnungu, ndande ya vichito vawo voipa ivo adavichita ni, mawu yawo yoipa yayo amamkamba Mnungu.”

16Wandhu achamenewo kila ndhawi angong'olong'ota ni kumlalamikila Ambuye. Ndhawi zonjhe achata makumbhilo yao yoipa ni kuyachita. mawu yawo yakhala kujhitutumula ni kwayelekela kupunda wina kwa phindu lao achinawene.

Maonyo ni Maagizo

17Nambho kumbukilani achabwenjilanga, mawu yajha mdakambidwa ni atumwi wa Ambuye wathu Yesu Kilisito. 18Anyiiwo adakuuzilani kuti, “Mumasiku yothela siajhe wandhu yawo sakudeleleni, wandhu yawo achata makhumbilo yao yoipa.” 19Wandhu achamenewo ndeyawo apeleka kupatukana pakati panu, wandhu yawo achata mkhalidwe wa chijhiko, ni alibe Mzimu Woyela. 20Nambho anyiimwe achabale wanga wokondedwa, mjhitangatilana anyiimwe kwa anyiimwe dala muyendekele kumkhupilila Mnungu, ni mujhimpembha Mnungu kwa mthandizo wa Mzimu Woyela. 21Muendekele kulimba mu chikondi cha Mnungu uku nimwalindilila Ambuye wathu Yesu Kilisito yao kwa lisungu lao siwakupacheni umoyo wa muyaya.

22Alengeleni lisungu wandhu yawo akhaikila, 23apulumucheni wina kwa kwanyakula kuchokela ku moto wa lamulo. Nambho kwa wina mkhale ni lisungu uku nimujhipenyelela, nambho ipilani ata njhalu zawo izo zajhala mabanga ya machimo yawo.

Mapembhelo ya mayamiko

24Kwaiye Mnungu wakhoza kukusungani anyiimwe msadajha kusiya kukhulupilila ni kuchita machimo, ni kukupelekani anyiimwe popande cholakwa mbaka pachogolo pa ulemelelo wake, 25iye Mnungu yokha uyo wali mwombili wathu kwaiye kuli ni, ulemelelo ni ukulu ni mbhavu ni ulamulilo, kwa kupitila Ambuye wathu Yesu ilisito, kuyambila kale, ni chipano, ni mbaka muyaya! Ikhale chimwecho.

The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.
Nyanja Tanzania Bible Version · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]