Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Numbers 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then our Father spoke to Moses and Aaron, saying: Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni:
2 "The Israelites are to camp, each by his standard, with banners of their ancestral houses, facing the tent of meeting all around, they are to camp. “Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.”
3 "To the east, toward sunrise: the camp of Judah, by their divisions, under its standard. Leader of Judah's people: Nahshon son of Amminadab. Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu.
4 His division, those counted, numbered 74,600. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.
5 "Camping next to him: the tribe of Issachar; the leader of Issachar's sons is Nethanel son of Zuar. Fuko la Isakara lidzamanga pafupi ndi Yuda. Mtsogoleri wa gulu la Isakara ndi Netanieli mwana wa Zuwara.
6 His division, those counted, numbered 54,400. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 54,400.
7 "Then the tribe of Zebulun; leader of Zebulun's sons: Eliab son of Helon. Lotsatira lidzakhala fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa gulu la Zebuloni ndi Eliabu mwana wa Heloni.
8 His division, those counted, numbered 57,400. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400.
9 "All counted in Judah's camp: 186,400, by their divisions. They set out first. Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka.
10 "South side: the banner of Reuben's camp, by divisions. Leader of Reuben's people: Elizur son of Shedeur. Kummwera kudzakhala magulu a msasa wa Rubeni pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri.
11 His division, those counted, numbered 46,500. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500.
12 "Camping beside him: the tribe of Simeon; leader of Simeon's people, Shelumiel son of Zurishaddai. Fuko la Simeoni lidzamanga pafupi ndi Rubeni. Mtsogoleri wa gulu la Simeoni ndi Selumieli mwana wa Zurisadai.
13 His division, those counted, numbered 59,300. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 59,300.
14 "Then the tribe of Gad: leader of Gad's people, Eliasaph son of Deuel. Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli.
15 His division, those counted, numbered 45,650. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650.
16 "Those counted in Reuben's camp, by their divisions: 151,450. They set out second. Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka.
17 "Then the tent of meeting sets out, with the Levites' camp in the middle of the camps. They set out in the order they camp, each in place, under their banners. Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake.
18 "West side: Ephraim's camp standard, by their divisions; leader of Ephraim's people is Elishama son of Ammihud. Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi.
19 His division, those counted, numbered 40,500. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500.
20 "Beside him: the tribe of Manasseh, led by Gamaliel son of Pedahzur. Fuko la Manase lidzakhala pafupi ndi Efereimu. Mtsogoleri wa Amanase ndi Gamalieli mwana wa Pedazuri.
21 His division, those counted, numbered 32,200. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 32,200.
22 "Then the tribe of Benjamin, led by Abidan son of Gideoni. Lotsatira lidzakhala fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa Abenjamini ndi Abidani mwana wa Gideoni.
23 His division, those counted, numbered 35,400. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400.
24 "All counted in Ephraim's camp: 108,100, by their divisions. They set out third. Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka.
25 "Dan's camp standard stands on the north side, by divisions. Ahiezer son of Ammishaddai leads Dan's people. Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
26 His division, those counted, numbered 62,700. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700.
27 "Camping next to it: the tribe of Asher, its leader Pagiel son of Ochran. Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani.
28 His division, those counted, numbered 41,500. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500.
29 "Then the tribe of Naphtali; Naphtali's leader is Ahira son of Enan. Lotsatira lidzakhala fuko la Nafutali. Mtsogoleri wa Anafutali ndi Ahira mwana wa Enani.
30 His division, those counted, numbered 53,400. Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400.
31 "All counted in Dan's camp: 157,600. They set out last, by their standards." Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo.
32 These are Israelites counted by their clans, all camp divisions: 603,550. Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo.
33 But the Levites were not counted among the Israelites, just as our Father had commanded Moses. Koma Alevi sanawawerenge pamodzi ndi Aisraeli enawo monga momwe Yehova analamulira Mose.
34 So the Israelites did all our Father commanded Moses. So they camped by their standards, and so they set out, each by clan, by ancestral family. Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]