Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Numbers 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Our Father spoke to Moses in the Sinai wilderness, in the tent of meeting, on the first day of the second month of the second year after they left the land of Egypt. He said: Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,
2 "Count the whole community of Israel's people, by clans and fathers' houses—every male, by name, head by head. “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi.
3 Register everyone in Israel twenty and older who can serve in the army—you and Aaron—by their divisions. Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali.
4 A man from each tribe is to be with you, each one the head of his family. Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi.
5 "Names of the men who will stand with you: from Reuben, Elizur son of Shedeur. Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,
6 "From Simeon, Shelumiel son of Zurishaddai; Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,
7 "From Judah, Nahshon son of Amminadab; Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,
8 "From Issachar, Nethanel son of Zuar; Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,
9 "From Zebulun, Eliab son of Helon; Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,
10 "From the sons of Joseph: from Ephraim, Elishama son of Ammihud; from Manasseh, Gamaliel son of Pedahzur; Mwa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi; kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;
11 "From Benjamin, Abidan son of Gideoni; Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,
12 "From Dan, Ahiezer son of Ammishaddai; Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,
13 "From Asher, Pagiel son of Ochran; Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,
14 "From Gad, Eliasaph son of Deuel; Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,
15 "From Naphtali, Ahira son of Enan. Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”
16 "These were the community's called ones, leaders of their ancestral tribes, heads of Israel's clans." Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.
17 So Moses and Aaron took these men who had been designated by name, Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa,
18 on the first day of the second month they gathered the whole community. The people registered their ancestry by clan and family—every male twenty years old and older, listed by name, one by one, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi
19 as our Father had commanded Moses. So Moses counted them in the wilderness of Sinai. monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:
20 From Reuben's descendants, Israel's firstborn: recorded by clan and family, name by name, every male twenty years old and up, able to serve in war. Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
21 Those counted from the tribe of Reuben were 46,500. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.
22 Simeon's descendants, by clans and families, counted by name, head by head: every male twenty years old and up, fit for the army. Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
23 Those counted from the tribe of Simeon were 59,300. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.
24 From Gad's descendants: by clans, families, and names, every man twenty and older fit for military service. Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
25 Those counted from the tribe of Gad were 45,650. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.
26 Judah's descendants, listed by clans and families, by name, every man twenty and older able to serve in the army: Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
27 those counted from the tribe of Judah were 74,600. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.
28 Issachar's descendants, listed by clan and family, by name, every man twenty years and older fit for war: Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
29 those counted from the tribe of Issachar were 54,400. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.
30 Zebulun's descendants: registered by clan and family, by name, every man twenty years old or older fit for military service. Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
31 Those counted from the tribe of Zebulun were 57,400. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.
32 Sons of Joseph, Ephraim's line: recorded by clan and family, by name, every man twenty and older fit for military service. Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
33 Those counted from the tribe of Ephraim were 40,500. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.
34 Manasseh's descendants, listed by clans and families, by name, each man twenty years or older able to serve in the army: Kuchokera mwa zidzukulu za Manase: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
35 those counted from the tribe of Manasseh were 32,200. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.
36 From Benjamin's descendants, recorded by clan and family, by name, every man twenty years old and older, fit for military service: Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
37 those counted from the tribe of Benjamin were 35,400. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.
38 From Dan's descendants, listed by clan and family, by name, every man twenty years old and older fit for war: Kuchokera mwa zidzukulu za Dani: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
39 those counted from the tribe of Dan were 62,700. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.
40 Asher's descendants, listed by clan and family, by name: every man twenty years old and up, fit for military service. Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
41 Those counted from the tribe of Asher were 41,500. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.
42 Naphtali's descendants: by clan and family, counted by name, every man twenty and older fit for war. Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali: Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
43 Those counted from the tribe of Naphtali were 53,400. Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.
44 Moses, Aaron, and Israel's twelve leaders counted these men, each for his family. Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake.
45 All Israel's people were counted by families, every man twenty years old and older, fit to serve in Israel's army. Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo.
46 All those counted came to 603,550. Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.
47 But the Levites were not counted among them by their ancestral tribe. Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena.
48 For our Father had said to Moses: Pakuti Yehova anawuza Mose kuti,
49 "Do not count the tribe of Levi or list them among the Israelites. “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli.
50 Instead, put the Levites in charge of the tabernacle of the testimony, all its furnishings, and everything belonging to it. They must carry the tabernacle and its furnishings, care for it, and camp around it. Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.
51 When the tabernacle sets out, Levites take it down; when it is pitched, Levites set it up. Any outsider who comes near is to be put to death. Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa.
52 Israel's people are to camp, each by his own camp, each under his own banner, by their companies. Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake.
53 The Levites must camp around the tabernacle of the testimony, so no wrath falls on the Israelite community; the Levites are to guard the tabernacle of the testimony." Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”
54 The people of Israel did everything our Father had commanded Moses; that is exactly what they did. Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]