Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Mark 4 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Jesus again taught by the sea. So large a crowd gathered around him that he got into a boat on the water and sat, while the whole crowd was on land by the sea. Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi.
2 He taught them many things in parables, and in his teaching he said to them: Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati:
3 "Listen! A sower went out to sow. “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake.
4 And as he sowed, some seed fell along the path, and the birds came and devoured it. Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya.
5 Other seed fell on rocky ground, lacking much soil, and sprang up at once since the soil had no depth. Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri.
6 When the sun rose, the plants were scorched, and since they had no root, they withered. Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu.
7 Other seed fell among thorns, and the thorns grew up and choked it, yielding no grain. Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula.
8 Other seed fell into good soil, producing grain that sprouted, grew, and yielded thirty, sixty, one hundred times what was sown." Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”
9 And he said, "Whoever has ears to hear, let him hear." Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
10 When he was alone, those around him, together with the Twelve, asked him about the parables. Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo.
11 He said to them, "To you is given the secret of the kingdom of our Father, but to those outside, everything comes in parables, Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo:
12 so that 'they may look but not perceive, and hear but not understand, and not turn and be forgiven.'" kotero kuti, “ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu, kumva mudzamva koma osamvetsetsa, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”
13 He said to them, "You don't understand this parable? Then how will you understand all the parables? Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse?
14 The sower sows the word. Wofesa amafesa mawu.
15 These are the ones on the path where the word is sown: once they hear, Satan comes immediately and takes away the word sown in them. Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo.
16 These are the ones sown on rocky ground, who hear the word and immediately receive it with joy. Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe.
17 But they have no root in themselves, lasting only briefly; when trouble or persecution comes because of the word, they fall away at once. Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira.
18 And others are the ones sown among thorns. These are those who hear the word, Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu;
19 but worries of this age, the deceit of wealth, and desires for other things enter and choke the word, and it produces no fruit. koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso.
20 And these are the ones sown on good soil: they hear the word, accept it, and produce fruit—thirty, sixty, one hundred times over." Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”
21 He told them, "Does anyone bring in a lamp to put it under a basket or bed—not on a stand? Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake?
22 Nothing is hidden except to be revealed; nothing is secret except to surface. Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera.
23 If anyone has ears to hear, let him hear." Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”
24 He told them, "Watch what you hear. The measure you use will be measured to you—and more added. Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri.
25 For whoever has will be given more; whoever doesn't, even what he has will be taken from him." Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”
26 He said, "This is what the kingdom of our Father is like: a man scatters seed on the ground. Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka.
27 Night and day, asleep or awake, the seed sprouts and grows, though he doesn't know how. Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira.
28 The soil yields grain on its own—first blade, then head, then full kernel in the head. Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo.
29 But when the grain ripens, he immediately sends the sickle, since harvest has come." Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
30 He said, "What can we compare the kingdom of our Father to, or what parable can we use for it? Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera?
31 It's like a mustard seed, the smallest of all seeds when sown on the ground. Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka.
32 Yet once sown, it grows up and becomes the largest of all garden plants, producing branches so big that birds of the air can nest in its shade." Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
33 With many such parables he spoke the word to them, as they were able to hear. Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa.
34 He spoke to them only in parables, but privately explained everything to his own disciples. Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.
35 That day, when evening came, he said to them, "Let us cross over to the other side." Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.”
36 They left the crowd and took him along, just as he was, in the boat, other boats accompanying him. Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye.
37 A fierce windstorm came up. Waves broke over the boat, so that it was already being swamped. Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira.
38 But Jesus was asleep in the stern on the cushion. They woke him and said, "Teacher, don't you care that we're dying?" Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
39 He got up, rebuked the wind, and told the sea, "Peace! Be still!" The wind stopped, and it grew totally calm. Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
40 He said to them, "Why are you so afraid? Do you still have no faith?" Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”
41 They were terrified and asked one another, "Who then is this, that even the wind and the sea obey him?" Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]