Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Mark 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Once again Jesus entered the synagogue, and a man with a withered hand was there. Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo.
2 They watched closely to see if he'd heal the man on the Sabbath, to accuse Jesus. Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata.
3 Jesus said to the man with the withered hand, "Stand up and come forward." Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.”
4 Then he asked them, "Is it lawful on the Sabbath to do good or to do harm, to save life or to kill?" But they stayed silent. Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.
5 He looked around at them in anger, grieved by their hardness of heart, and told the man, "Stretch out your hand." He stretched it out, and his hand was restored. Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira.
6 Then the Pharisees went out and immediately began plotting with the Herodians how they might destroy him. Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.
7 Jesus withdrew with his disciples to the sea; a large crowd from Galilee followed, and from Judea, Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata.
8 from Jerusalem, Idumea, beyond the Jordan, and the region around Tyre and Sidon—hearing all he was doing, a great crowd came to him. Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni.
9 He told his disciples to keep a small boat ready, because of the crowd, so they wouldn't crush him. Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize.
10 For he had healed so many that all who had diseases were pressing forward to touch him. Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze.
11 Whenever the unclean spirits saw him, they fell before him, shouting, "You are the Son of God!" Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!”
12 But he firmly warned them not to reveal him. Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.
13 Jesus went up the mountain and called those he wanted; they came to him. Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye.
14 He appointed twelve, named apostles, so they could be with him and he could send them out to preach, Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira
15 and to have authority to drive out demons. ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda.
16 These are the twelve he appointed: Simon, to whom he gave the name Peter; Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro);
17 James son of Zebedee, and John his brother, whom he named Boanerges, meaning Sons of Thunder; Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu);
18 Andrew, Philip, Bartholomew, Matthew, Thomas, James son of Alphaeus, Thaddaeus, Simon the Zealot, Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote,
19 and Judas Iscariot, who betrayed him. ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
20 He went home; the crowd gathered again, so he and his disciples couldn't even eat. Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye.
21 When his family heard, they went out to restrain him, for they said, "He's out of his mind." Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”
22 The scribes who came down from Jerusalem said, "He has Beelzebul," and, "By the prince of demons he drives out demons." Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
23 So Jesus called them to him and spoke in parables: "How can Satan drive out Satan? Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana?
24 If a kingdom is divided against itself, that kingdom cannot stand. Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse.
25 And if a house is divided against itself, that house will not be able to stand. Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima.
26 And if Satan opposes himself and is divided, he cannot stand; his end has come. Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha.
27 No one can enter a strong man's house and take his goods without first tying up the strong man—then he can plunder the house. Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera.
28 Truly I tell you, all sins and insults against God will be forgiven children of mankind, whatever they say, Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa,
29 but whoever blasphemes against the Holy Spirit never has forgiveness; they are guilty of an eternal sin," koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”
30 for they were saying, "He has an unclean spirit." Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”
31 His mother and brothers arrived and, standing outside, sent to him, calling him. Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye.
32 A crowd sat around him and said to him, "Look, your mother and your brothers are outside, asking for you." Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”
33 He answered them, "Who are my mother and my brothers?" Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?”
34 Looking around at those sitting in a circle around him, he said, "Here are my mother and my brothers! Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga!
35 Whoever does the will of our Father is my brother and sister and mother." Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]