Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

James 1 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 James, a servant of our Father and the Lord Jesus Christ, to the twelve tribes scattered among the nations: greetings. Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana. Landirani moni.
2 Consider it pure joy, my brothers and sisters, whenever you face trials of many kinds, Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu.
3 because you know that the testing of your faith produces perseverance. Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro.
4 Let perseverance finish its work so that you may be mature and complete, lacking nothing. Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse.
5 If any of you lacks wisdom, ask our Father, who gives freely to all without criticizing, and it will be given you. Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.
6 Ask in faith, without doubting, for the doubter is like a sea wave, driven and tossed by the wind. Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo.
7 That person should not expect to receive anything from our Father. Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye.
8 Such a person is double-minded and unstable in all their ways. Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.
9 Let the believer in humble circumstances take pride in their high position, Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa.
10 but let the rich boast in their low state, since they'll pass like a wildflower. Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo.
11 The sun rises with scorching heat and withers the grass. Its flower falls; its beauty vanishes. So the rich fade away amid their pursuits. Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.
12 Blessed is the one who endures trial, because once tested they'll receive the crown of life our Father promised to those who love him. Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.
13 When tempted, no one should say, "Our Father is tempting me." Evil can't tempt our Father, and he tempts no one. Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense.
14 But each person is tempted, dragged away and lured by their own evil desire. Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo.
15 Then desire conceives and gives birth to sin; sin, full-grown, gives birth to death. Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.
16 Don't be deceived, my dear brothers and sisters. Musanyengedwe abale anga okondedwa.
17 Every good and perfect gift is from above, coming down from the Father of lights, who never changes or casts a shifting shadow. Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.
18 By his choice, he gave us birth through the word of truth, so we'd be a kind of firstfruits of his creation. Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.
19 Know this, my dear brothers and sisters: everyone should be quick to listen, slow to speak, slow to anger, Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima.
20 because human anger does not produce the righteousness of our Father. Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu.
21 So strip off all moral filth and excess evil; humbly receive the word planted in you, able to save your souls. Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.
22 Do not merely listen to the word, and so deceive yourselves. Do what it says. Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.
23 Anyone who hears the word but doesn't act on it is like one who looks at his natural face in a mirror, Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi.
24 and, after looking at himself, goes away and immediately forgets what he looks like. Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera.
25 But whoever peers into the perfect law of freedom, continuing in it—not a forgetful hearer but a doer who acts—will be blessed in his doing. Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.
26 If anyone thinks himself religious but doesn't control his tongue, he deceives his own heart—his religion is worthless. Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe.
27 Pure and spotless religion before our Father is this: caring for orphans and widows in their distress, and keeping oneself unstained from the world. Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]