Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 60 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Arise, shine, for your light has come, and the glory of our Father has risen upon you. “Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika, ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
2 For darkness will cover the earth, and thick darkness the peoples; but our Father will rise upon you, and his glory will be seen upon you. Taona, mdima waphimba dziko lapansi ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina, koma Yehova adzakuwalira iwe, ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
3 Nations will come to your light, and kings to the brightness of your dawning. Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.
4 Lift up your eyes all around and see: they all gather together, they come to you; your sons come from far away, and your daughters are carried on the hip. “Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika. Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe; ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
5 Then you will see and be radiant; your heart will throb and swell, because the abundance of the sea will turn toward you, the wealth of the nations will come to you. Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri, mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe; chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
6 A multitude of camels will cover you, the young camels of Midian and Ephah; all those from Sheba will come, bearing gold and frankincense, and they will proclaim the praises of our Father. Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako, ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai. Ndipo onse a ku Seba adzabwera atanyamula golide ndi lubani uku akutamanda Yehova.
7 All the flocks of Kedar will be gathered to you, the rams of Nebaioth will minister to you; they will be offered on my altar and accepted, and I will glorify my glorious house. Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu, nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani; zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe, ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
8 Who are these that fly like a cloud, and like doves to their windows? “Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo, ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?
9 Surely the coastlands wait for me, the ships of Tarshish first, to bring your sons from far away, with their silver and gold, for the name of your Father, the Holy One of Israel, because he has glorified you. Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali; patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi, zikubweretsa ana ako ochokera kutali, pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo, kudzalemekeza Yehova Mulungu wako, Woyerayo wa Israeli, pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
10 Foreigners will build up your walls, and their kings will serve you; for in my wrath I struck you, but in my favor my heart was moved with compassion for you. “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu awo adzakutumikira. Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo.
11 Your gates will stand open continually; day and night they will not be shut, so that the wealth of the nations may be brought to you, with their kings led in procession. Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse, sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku, kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo, akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
12 For the nation and kingdom that will not serve you will perish; those nations will be utterly laid waste. Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe; adzawonongeka kotheratu.
13 The glory of Lebanon will come to you—the cypress, the plane, and the pine together—to beautify the place of my sanctuary; and I will glorify the place of my feet. “Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini, mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanoni kuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika; ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
14 The children of those who oppressed you will come bowing before you; all who despised you will bow down at your feet. They will call you the City of our Father, the Zion of the Holy One of Israel. Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani; onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu. Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova; Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
15 Though you have been forsaken and hated, with no one passing through, I will make you an everlasting pride, a joy from generation to generation. “Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe, koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe cha anthu amibado yonse.
16 You will drink the milk of nations, and nurse at the breast of kings; and you will know that I, your Father, am your Savior and your Redeemer, the Mighty One of Jacob—your Father. Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthu ndi kuleredwa pa maere aufumu, motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako, Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo.
17 Instead of bronze I will bring gold, instead of iron I will bring silver, instead of wood, bronze, and instead of stones, iron. I will make peace your governor and righteousness your taskmaster. Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa, ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo. Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala. Olamulira ako adzakhala a mtendere. Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
18 Violence will no longer be heard in your land, nor ruin and destruction within your borders; but you will call your walls Salvation and your gates Praise. Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako, bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako, ndidzakhala malinga ako okuteteza ndipo udzanditamanda.
19 The sun will no longer be your light by day, nor will the moon give you its light; but our Father will be your everlasting light, and your Father your glory. Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire, kapena mwezi kuti uwunikire usiku, pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya, ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
20 Your sun will no longer set, and your moon will not wane; for our Father will be your everlasting light, and the days of your mourning will be ended. Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzazimiriranso; Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya, ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
21 Your people will all be righteous; they will possess the land forever—the branch of my planting, the work of my hands, that I may be glorified. Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya. Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala, ntchito ya manja anga, kuti aonetse ulemerero wanga.
22 The least one will become 1,000, and the smallest a mighty nation. I am your Father; when the time is right, I will make it happen quickly. Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko, kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu. Ine ndine Yehova, nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]