Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 59 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Look, our Father's hand is not too short to save, nor his ear too dull to hear. Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa, kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.
2 But your wrongs have separated you from your Father, and your sins have hidden his face from you, so that he does not hear. Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva.
3 For your hands are defiled with blood, and your fingers with sin; your lips have spoken lies, your tongue mutters wickedness. Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi. Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu. Pakamwa panu payankhula zabodza, ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa.
4 No one calls for justice, and no one pleads with honesty. They trust in emptiness and speak lies; they conceive trouble and give birth to evil. Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama, palibe amene akupita ku mlandu moona mtima. Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza; amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.
5 They hatch the eggs of vipers and weave the spider's web; whoever eats their eggs dies, and when one is crushed, a viper breaks out. Iwo amayikira mazira a mamba ndipo amaluka ukonde wakangawude. Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa, ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri.
6 Their webs cannot become clothing, and they cannot cover themselves with what they make. Their works are works of wrongdoing, and their hands are full of violence. Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala; ndipo chimene apangacho sangachifunde. Ntchito zawo ndi zoyipa, ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
7 Their feet run to evil, and they hurry to shed innocent blood. Their thoughts are thoughts of wrongdoing; ruin and destruction lie along their every road. Amathamangira kukachita zoyipa; sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo awo ndi maganizo oyipa; kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
8 The way of peace they do not know, and there is no justice in their ways. They have made their paths crooked; no one who walks in them knows peace. Iwo sadziwa kuchita za mtendere; zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo. Njira zawo zonse nʼzokhotakhota; aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere.
9 Therefore justice is far from us, and righteousness does not reach us. We wait for light, but there is only darkness; for brightness, but we walk in gloom. Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira; ndipo chipulumutso sichitifikira. Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha; tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
10 We grope along the wall like the blind; like those without eyes we grope. We stumble at noon as if in twilight; among the strong we are like the dead. Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona, kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso. Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku; timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.
11 We all growl like bears and moan mournfully like doves. We wait for justice, but there is none; for salvation, but it stays far from us. Tonse timabangula ngati zimbalangondo: Timalira modandaula ngati nkhunda. Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza. Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.”
12 For our rebellions are many before you, and our sins testify against us. Our rebellions are with us, and our wrongdoing we know: Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu, ndipo machimo athu akutsutsana nafe. Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonse ndipo tikuvomereza machimo athu:
13 rebelling and denying our Father, turning back from following our Father, speaking oppression and revolt, conceiving and muttering lying words from the heart. Tawukira ndi kumukana Yehova. Tafulatira Mulungu wathu, pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova, ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu.
14 So justice is driven back, and righteousness stands far off; for truth has stumbled in the public square, and integrity cannot enter. Motero kuweruza kolungama kwalekeka ndipo choonadi chili kutali ndi ife; kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu, ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo.
15 Truth is missing, and whoever turns from evil is plundered. Our Father saw it and was displeased that there was no justice. Choonadi sichikupezeka kumeneko, ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto. Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansa kuti panalibe chiweruzo cholungama.
16 He saw that there was no one, and was appalled that no one would intervene; so his own arm brought salvation, and his righteousness upheld him. Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe, Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera; Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza, ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;
17 He put on righteousness like a breastplate, and a helmet of salvation on his head; he clothed himself in garments of vindication and wrapped himself in zeal like a cloak. Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso; anavala kulipsira ngati chovala ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.
18 According to their deeds, so he will repay: wrath to his adversaries, repayment to his enemies; to the distant coastlands he will give them what they deserve. Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake molingana ndi zimene anachita, adzaonetsa ukali kwa adani ake ndi kubwezera chilango odana naye. Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
19 So they will fear the name of our Father from the west, and his glory from the rising of the sun; for he will come like a rushing river, driven by the wind of our Father. Choncho akadzabwera ngati madzi oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho. Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
20 Then the Redeemer will come to Zion, to those in Jacob who turn from their sins, declares our Father. “Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,” akutero Yehova.
21 "As for me, this is my covenant with them," says our Father: "My Spirit who is upon you, and my words that I have put in your mouth, will not depart from your mouth, or from the mouth of your children, or from the mouth of your children's children," says our Father, "from now on and forever." Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]