Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 49 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Listen to me, coastlands; pay attention, you peoples from afar. Our Father called me from the womb; from within my mother he named me. Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali: Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe, ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
2 He made my mouth like a sharp sword; in the shadow of his hand he hid me. He made me a polished arrow; in his quiver he concealed me. Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa, anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake; Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa ndipo anandibisa mʼchimake.
3 And he said to me, "You are my servant, Israel, in whom I will display my splendor." Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
4 But I said, "I have labored in vain; I have spent my strength for nothing and in futility. Yet surely my justice is with my Father, and my reward with my Father." Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe, koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova, ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
5 And now our Father says—he who formed me from the womb to be his servant, to bring Jacob back to him, that Israel might be gathered to him, for I am honored in his eyes, and my Father has become my strength, Yehova anandiwumba ine mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye, choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova, ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
6 he says: "It is too small a thing for you to be my servant to raise up the tribes of Jacob and to bring back those preserved in Israel; I will also make you a light for the nations, that my salvation may reach to the ends of the earth." Yehovayo tsono akuti, “Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobo ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka. Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira, udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”
7 This is what our Father says, the Redeemer of Israel, his Holy One, to the one deeply despised, abhorred by the nation, to the servant of rulers: Kings will see and rise; princes will bow down, because of your Father who is faithful, the Holy One of Israel, who has chosen you. Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula, Woyerayo wa Israeli akunena, amene mitundu ya anthu inamuda, amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti, “Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira. Akalonga nawonso adzagwada pansi. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
8 This is what our Father says: In a time of favor I answered you, and in a day of salvation I helped you; I will keep you and give you as a covenant for the people, to restore the land, to apportion the desolate inheritances, Yehova akuti, “Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza; ndinakusunga ndi kukusandutsa kuti ukhale pangano kwa anthu, kuti dziko libwerere mwakale ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
9 saying to the prisoners, 'Come out,' and to those in darkness, 'Show yourselves.' Along the roads they will feed, and on all the bare heights will be their pasture. Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke ndi a mu mdima kuti aonekere poyera. “Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira ndi msipu pa mʼmalo owuma.
10 They will not hunger or thirst, nor will scorching wind or sun strike them, for the one whose heart is moved with compassion for them will lead them, and by springs of water he will guide them. Iwo sadzamva njala kapena ludzu, kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza; chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
11 And I will turn all my mountains into a road, and my highways will be raised up. Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo, ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.
12 Look—these will come from far away; and look, these from the north and the west, and these from the land of Sinim. Taonani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kumadzulo, enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”
13 Sing for joy, heavens, and rejoice, earth; break out in singing, mountains! For our Father has comforted his people, and his heart is moved with compassion for his afflicted ones. Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga; kondwera, iwe dziko lapansi; imbani nyimbo inu mapiri! Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.
14 But Zion said, "Our Father has forsaken me; the Sovereign Father has forgotten me." Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya, Ambuye wandiyiwala.”
15 "Can a woman forget her nursing child, that her heart would not be moved with compassion for the son of her womb? Even these may forget, yet I will not forget you. “Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni? Ngakhale iye angathe kuyiwala, Ine sindidzakuyiwala iwe!
16 Look—I have engraved you on the palms of my hands; your walls are ever before me. Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga; makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
17 Your children hurry back; those who tore you down and laid you waste go away from you. Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira, ndipo amene anakupasula akuchokapo.
18 Look all around you and see: they all gather and come to you. As surely as I live, declares our Father, you will wear them all like an ornament; you will bind them on like a bride. Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe. Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo, anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
19 Surely your ruins and your desolate places and your devastated land—surely now you will be too cramped for your inhabitants, and those who swallowed you up will be far away. “Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa ndipo dziko lako ndi kusakazidwa, chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
20 The children born in your bereavement will yet say in your hearing, "This place is too narrow for me; make room for me to live." Ana obadwa nthawi yako yachisoni adzanena kuti, ‘Malo ano atichepera, tipatse malo ena woti tikhalemo.’
21 Then you will say in your heart, "Who bore these for me? I was bereaved and barren, exiled and cast aside—who has raised these? I was left all alone; where did these come from?" Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa? Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena; ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa. Ndani anawalera ana amenewa? Ndinatsala ndekha, nanga awa, achokera kuti?’ ”
22 This is what the Sovereign Father says: Look—I will lift up my hand to the nations and raise my signal to the peoples; and they will bring your sons in their arms, and your daughters will be carried on their shoulders. Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi, “Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere. Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere. Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
23 Kings will be your foster fathers, and their queens your nursing mothers. With faces to the ground they will bow down to you and lick the dust of your feet. Then you will know that I am your Father; those who wait for me will not be ashamed." Mafumu adzakhala abambo wongokulera ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera. Iwo adzagwetsa nkhope zawo pansi. Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova; iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”
24 Can the plunder be taken from the mighty, or the captives of a tyrant be rescued? Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo, kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?
25 But this is what our Father says: Even the captives of the mighty will be taken, and the plunder of the tyrant rescued; for I myself will contend with those who contend with you, and I will save your children. Koma zimene Yehova akunena ndi izi, “Ankhondo adzawalanda amʼndende awo, ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo; ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
26 I will make your oppressors eat their own flesh, and they will be drunk on their own blood as with sweet wine. Then all flesh will know that I am your Savior—your Father—and your Redeemer, the Mighty One of Jacob. Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe; adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu, Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]