Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 40 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Comfort, comfort my people, says your Father. Atonthozeni, atonthozeni anthu anga, akutero Mulungu wanu.
2 Speak tenderly to Jerusalem, and proclaim to her that her hard service is completed, that her guilt is forgiven, that she has received from our Father's hand double for all her sins. Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu ndipo muwawuzitse kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha, tchimo lawo lakhululukidwa. Ndawalanga mokwanira chifukwa cha machimo awo onse.
3 A voice is calling out: In the wilderness, prepare the way of our Father; make a straight highway through the desert for our Father. Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti, “Konzani njira ya Yehova mʼchipululu; wongolani njira zake; msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
4 Every valley will be lifted up, and every mountain and hill made low; the uneven ground will become level, and the rough places will become a plain. Chigwa chilichonse achidzaze. Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse; Dziko lokumbikakumbika alisalaze, malo azitundazitunda awasandutse zidikha.
5 And the glory of our Father will be revealed, and all people will see it together, for the mouth of our Father has spoken. Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera, ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona, pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”
6 A voice says, "Call out!" And I said, "What should I call out?" All people are like grass, and all their faithfulness is like the flower of the field. Wina ananena kuti, “Lengeza.” Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani? “Pakuti anthu onse ali ngati udzu ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
7 The grass withers, the flower fades when the breath of our Father blows on it; surely the people are grass. Udzu umanyala ndipo maluwa amafota chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.” Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
8 The grass withers, the flower fades, but the word of our Father stands forever. Udzu umanyala ndipo maluwa amafota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
9 Go up on a high mountain, Zion, messenger of good news; lift up your voice with strength, Jerusalem, messenger of good news. Lift it up, do not be afraid; say to the cities of Judah, "Here is your Father!" Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni, kwera pa phiri lalitali. Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu, fuwula kwambiri, kweza mawu, usachite mantha; uza mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera!”
10 See, the Sovereign Father comes with strength, and his arm rules for him; see, his reward is with him, and his payment goes before him. Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu, ndipo dzanja lake likulamulira, taonani akubwera ndi mphotho yake watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
11 He will tend his flock like a shepherd; he will gather the lambs in his arms and carry them close to his heart; he will gently lead those that have young. Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa: Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
12 Who has measured the waters in the hollow of his hand, and marked off the heavens with the breadth of his hand, enclosed the dust of the earth in a measure, and weighed the mountains in scales and the hills in a balance? Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu, kapena kuyeza kulemera kwa mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
13 Who has directed the Spirit of our Father, or as his counselor has instructed him? Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
14 Whom did he consult, and who made him understand? Who taught him the path of justice, and taught him knowledge, and showed him the way of understanding? Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya, kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru? Iye anapempha nzeru kwa yani ndi njira ya kumvetsa zinthu?
15 The nations are like a drop from a bucket, and are counted as the dust on the scales; he takes up the islands like fine dust. Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko. Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo; mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
16 Lebanon is not enough to burn, nor its animals enough for a burnt offering. Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe, ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
17 All the nations are as nothing before him; they are regarded by him as less than nothing and emptiness. Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake; Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu ndi cha chabechabe.
18 To whom then will you liken our Father? Or what likeness will you compare to him? Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
19 An idol! A craftsman casts it, and a goldsmith overlays it with gold and casts silver chains for it. Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide naliveka mkanda wasiliva.
20 Anyone too poor for such an offering chooses wood that will not rot; he seeks out a skillful craftsman to set up an idol that will not topple. Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere amasankha mtengo umene sudzawola, nafunafuna mʼmisiri waluso woti amupangire fano limene silingasunthike.
21 Do you not know? Do you not hear? Has it not been told you from the beginning? Have you not understood from the foundations of the earth? Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe? Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
22 He sits enthroned above the vault of the earth, its people below like grasshoppers; he spreads the skies like a thin veil, pitching them as a tent to live in. Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi, Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala. Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga, nayikunga ngati tenti yokhalamo.
23 He brings princes to nothing, and makes the rulers of the earth as emptiness. Amatsitsa pansi mafumu amphamvu nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
24 They are barely planted, barely sown, their stem has barely taken root in the ground, when he blows on them and they wither, and the storm sweeps them away like chaff. Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene kapena kufesedwa chapompano, ndi kungoyamba kuzika mizu kumene ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
25 "To whom then will you compare me, that I should be like him?" says the Holy One. Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani? Kapena kodi alipo wofanana nane?”
26 Look up into the heavens and see: who created these? He who brings out their host by number, calling them all by name; because he is great in strength and mighty in power, not one is missing. Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani. Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi? Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo, nayitana iliyonse ndi dzina lake. Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri, palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
27 Why do you say, Jacob, and complain, Israel, "My way is hidden from our Father, and my Father disregards my right"? Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti, “Yehova sakudziwa mavuto anga, Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
28 Have you not known? Have you not heard? Our Father is the everlasting Father, the Creator of the ends of the earth. He does not faint or grow weary; no one can fathom his understanding. Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Yehova ndiye Mulungu wamuyaya, ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi. Iye sadzatopa kapena kufowoka ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
29 He gives power to the weary, and increases strength for the powerless. Iye amalimbitsa ofowoka ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
30 Even youths will grow faint and weary, and young men will fall exhausted; Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka, ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
31 but those who wait for our Father will renew their strength; they will soar on wings like eagles; they will run and not be weary; they will walk and not faint. koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]