Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 41 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Listen to me in silence, coastlands; let the peoples renew their strength. Let them come near and speak; let us together draw near for judgment. “Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja! Alekeni ayandikire ndi kuyankhula; tiyeni tikhale pamodzi kuti atiweruze.
2 Who stirred up one from the east, calling him in righteousness to follow him? He hands nations over to him and subdues kings before him; he turns them to dust with his sword, to wind-driven stubble with his bow. “Ndani anadzutsa wochokera kummawa uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita? Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
3 He pursues them and passes on safely, by a path his feet have never traveled. Amawalondola namayenda mosavutika, mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
4 Who has performed and done this, calling the generations from the beginning? I am the Father—the first, and with the last; I am he. Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza, si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu? Ine Yehova, ndine chiyambi ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
5 The coastlands have seen it and are afraid; the ends of the earth tremble; they draw near and come. Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa; anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera. Akuyandikira pafupi, akubwera;
6 Each one helps his neighbor and says to his brother, "Take courage!" aliyense akuthandiza mnzake ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
7 The craftsman encourages the goldsmith, and the one who smooths with the hammer him who strikes the anvil, saying of the soldering, "It is good"; and they fasten it with nails so it cannot be moved. Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide, ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala. Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.” Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
8 But you, Israel, my servant, Jacob, whom I have chosen, the offspring of Abraham, my friend, “Koma Iwe Israeli mtumiki wanga, Yakobo amene ndakusankha, Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
9 you whom I took from the ends of the earth, and called from its farthest corners, saying to you, "You are my servant; I have chosen you and not rejected you". Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi. Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’ Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
10 "Fear not, for I am with you; do not be dismayed, for I am your Father. I will strengthen you, I will help you, I will uphold you with my righteous right hand. Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
11 See, all who rage against you will be ashamed and disgraced; those who oppose you will be as nothing and perish. “Onse amene akupsera mtima adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa; onse amene akukangana nawe sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
12 You will look for those who war against you, but you will not find them; those who battle against you will be as nothing at all." Udzafunafuna adani ako, koma sadzapezeka. Iwo amene akuchita nawe nkhondo sadzakhalanso kanthu.
13 For I, your Father, take hold of your right hand; I am the one who says to you, "Fear not, I am the one who helps you." Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako, amene ndikukugwira dzanja lako lamanja ndipo ndikuti, usaope; ndidzakuthandiza.
14 Fear not, you worm Jacob, you men of Israel! I am the one who helps you, declares our Father; your Redeemer is the Holy One of Israel—your Father. Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi, iwe wochepa mphamvu Israeli, chifukwa Ine ndidzakuthandiza,” akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
15 "See, I make you into a threshing sledge, new and sharp, with many teeth; you will thresh the mountains and crush them, and make the hills like chaff. “Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri. Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya, ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
16 You will winnow them, and the wind will carry them away, and the storm will scatter them. But you will rejoice in our Father; in the Holy One of Israel you will glory. Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso adzamwazika ndi kamvuluvulu. Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako, ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
17 When the poor and needy seek water, and there is none, and their tongues are parched with thirst, I, your Father, will answer them; I, the Father of Israel, will not forsake them. “Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi, koma sakuwapeza; ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu. Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo; Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
18 I will open rivers across the barren heights, and springs down in the valleys; I will make the desert pools of water, and dry ground flowing springs. Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma, ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
19 I will plant in the wilderness the cedar, the acacia, the myrtle, and the olive; I will set in the desert the cypress, the plane, and the pine together, Mʼchipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi. Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
20 that they may see and know, may consider and understand together, that my hand has done this, that I, the Holy One of Israel, have created it." kuti anthu aone ndi kudziwa; inde, alingalire ndi kumvetsa, kuti Yehova ndiye wachita zimenezi; kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
21 Set forth your case, says our Father; bring your proofs, says the King of Jacob. “Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’ Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
22 Let them bring them, and tell us what is to happen. Tell us the former things, what they were, that we may consider them and know their outcome; or declare to us the things to come. Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze zomwe zidzachitike mʼtsogolo. Tifotokozereni zinthu zamakedzana tiziganizire ndi kudziwa zotsatira zake. Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
23 Tell us what is to come hereafter, that we may know that you are gods; do good, or do harm, that we may be dismayed and filled with fear together. tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani, ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu. Chitani chinthu chabwino kapena choyipa, ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
24 Look, you are nothing, and your work is less than nothing; whoever chooses you is an abomination. Koma inu sindinu kanthu ndipo zochita zanu nʼzopandapake; amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.
25 I stirred up one from the north, and he has come, from the rising of the sun one who calls on my name; he tramples rulers like mortar, like a potter treading clay. “Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera, munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana. Amapondaponda olamulira ngati matope, ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
26 Who declared it from the beginning, that we might know, and beforehand, that we might say, "He is right"? There was no one who declared it, no one who proclaimed, no one who heard your words. Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe, kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’ Palibe amene ananena, palibe analengeza zimenezi, palibe anamva mawu anu.
27 I was the first to say to Zion, "Look, here they are!" and I gave to Jerusalem a herald of good news. Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’ Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
28 "But when I look, there is no one; among these there is no counselor who, when I ask, can give an answer. Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu, palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
29 See, they are all a delusion; their works are nothing; their cast idols are empty wind." Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo! Zochita zawo si kanthu konse; mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]