Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 28 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Woe to the proud crown of the drunkards of Ephraim, and to the fading flower of its glorious beauty, which sits on the head of the lush valley of those overcome with wine! Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu. Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa limene lili pa mutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde.
2 Look, the Sovereign Father has one who is mighty and strong; like a hailstorm, a destroying tempest, like a storm of mighty, overflowing waters, he will hurl it down to the earth with his hand. Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga. Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga, ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho; ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
3 The proud crown of the drunkards of Ephraim will be trampled underfoot. Ulamuliro wa atsogoleri oledzera a ku Efereimu adzawuthetsa.
4 And the fading flower of its glorious beauty, which sits on the head of the lush valley, will be like a first-ripe fig before summer—whoever sees it swallows it as soon as it is in his hand. Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja, udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa imene munthu akangoyiona amayithyola nthawi yokolola isanakwane.
5 In that day the Father of heaven's armies will be a crown of glory and a diadem of beauty to the remnant of his people, Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse adzakhala ngati nkhata yaufumu, chipewa chokongola kwa anthu ake otsala.
6 and a spirit of justice to the one who sits in judgment, and strength to those who turn back the battle at the gate. Iye adzapereka mtima wachilungamo kwa oweruza, adzakhala chilimbikitso kwa amene amabweza adani pa zipata za mzinda.
7 These also reel with wine and stagger with strong drink: the priest and the prophet reel with strong drink, they are confused by wine, they stagger with strong drink, they reel when they see visions, they stumble in giving their rulings. Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo ndipo akusochera chifukwa cha mowa: ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo; akusochera chifukwa cha mowa, akudzandira pamene akuona masomphenya, kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
8 For all the tables are covered with filthy vomit, with no clean place left. Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.
9 "Whom will he teach knowledge, and to whom will he explain the message? Those just weaned from milk, those just taken from the breast? Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani? Uthengawu akufuna kufotokozera yani? Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa, kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
10 For it is order on order, order on order, line on line, line on line, a little here, a little there." Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”
11 Indeed, by people of strange lips and a foreign tongue he will speak to this people, Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino. Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
12 to whom he had said, "This is the rest; give rest to the weary; this is the resting place"—yet they were not willing to listen. anakuwuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo owusira ndi ano.” Koma inu simunamvere.
13 So the word of our Father will be to them rule on rule, rule on rule, line on line, line on line, a little here, a little there, that they may go and stumble backward, and be broken, and snared, and captured. Choncho Yehova adzakuphunzitsani pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo, adzapweteka ndi kukodwa mu msampha ndipo adzakutengani ku ukapolo.
14 Therefore hear the word of our Father, you scoffers who rule this people in Jerusalem! Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova, inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
15 Because you have said, "We have struck a covenant with death, and with the grave we have made an agreement; when the overwhelming flood passes through, it will not reach us, for we have made lies our refuge and hidden ourselves in falsehood", Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa, ife tachita mgwirizano ndi manda. Pamene mliri woopsa ukadzafika sudzatikhudza ife, chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.”
16 therefore this is what the Sovereign Father says: "Look, I am laying in Zion a stone, a tested stone, a precious cornerstone, a sure foundation: the one who believes will not panic. Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: “Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri ngati maziko mu Ziyoni, mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu; munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
17 And I will make justice the measuring line and righteousness the plumb line; hail will sweep away the refuge of lies, and waters will flood the hiding place. Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake, ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere; matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza, ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
18 Then your covenant with death will be wiped out, and your agreement with the grave will not stand; when the overwhelming flood passes through, you will be trampled down by it. Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa; mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa. Pakuti mliri woopsa udzafika, ndipo udzakugonjetsani.
19 As often as it passes through, it will seize you; for morning by morning it will pass through, by day and by night, and it will be sheer terror just to take in the news." Ndipo ukadzangofika udzakutengani. Udzafika mmawa uliwonse, usiku ndi usana.” Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu adzaopsedwa kwambiri.
20 For the bed is too short to stretch out on, and the blanket too narrow to wrap up in. Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo; ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.
21 For our Father will rise up as he did at Mount Perazim, he will be stirred as in the Valley of Gibeon, to do his work—strange is his work!—and to perform his task—foreign is his task! Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni; adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo, ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
22 Now therefore do not scoff, or your chains will grow tighter; for I have heard a decree of destruction from the Father of heaven's armies, against the whole land. Tsopano lekani kunyoza, mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri; Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”
23 Listen and hear my voice; pay attention and hear my words. Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga; mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.
24 Does the farmer plow all day to plant? Does he keep breaking up and tilling his ground? Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?
25 When he has leveled its surface, does he not scatter dill and sow cumin, and plant wheat in rows and barley in its plot, and spelt along the border? Pamene iye wasalaza mundawo, kodi samafesa mawere ndi chitowe? Kodi suja samadzala tirigu ndi barele mʼmizere yake, nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
26 His Father instructs him rightly; his Father teaches him. Mulungu wake amamulangiza ndi kumuphunzitsa njira yabwino.
27 Dill is not threshed with a sledge, nor is a cart wheel rolled over cumin; but dill is beaten out with a stick, and cumin with a rod. Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero, kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta; mawere amapuntha ndi ndodo ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.
28 Grain for bread must be crushed, but he does not thresh it forever; he drives his cart wheel and horses over it, yet does not crush it to powder. Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi, komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke. Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta, koma akavalo ake satekedza tiriguyo.
29 This too comes from the Father of heaven's armies; he is wonderful in counsel and magnificent in wisdom. Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]