Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Isaiah 29 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Woe to Ariel, Ariel, the city where David encamped! Add year to year; let the feasts keep coming round. Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli, mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo! Papite chaka chimodzi kapena ziwiri ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
2 Yet I will press hard on Ariel, and there will be mourning and lament; she will become to me like an altar hearth. Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula, mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
3 I will encamp against you all around; I will besiege you with a wall and raise up siegeworks against you. Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo; ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
4 You will be brought low; from the ground you will speak, and your words will be muffled in the dust. Your voice will come from the earth like a ghost's, and your speech will whisper out of the dust. Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka, mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi, adzamveka ngati a mzukwa. Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
5 But the horde of your enemies will become like fine dust, and the horde of the ruthless like blowing chaff. And it will happen in an instant, suddenly. Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti. Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo. Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
6 You will be visited by the Father of heaven's armies with thunder and earthquake and a great roar, with whirlwind and storm and the flame of a devouring fire. Yehova Wamphamvuzonse adzabwera ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu, kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
7 And the horde of all the nations that wage war against Ariel, all who fight against her and her stronghold and press hard on her, will be like a dream, a vision of the night. Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga, chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto, gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
8 It will be as when a hungry man dreams he is eating, and wakes with his hunger unsatisfied; or as when a thirsty man dreams he is drinking, and wakes faint, his thirst unquenched. So will it be with the horde of all the nations that fight against Mount Zion. Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya, koma podzuka ali nayobe njala; kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa, koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa. Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
9 Be dumbfounded and stunned; blind yourselves and be blind! They are drunk, but not with wine; they stagger, but not from strong drink. Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa. Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya, ledzerani, koma osati ndi vinyo, dzandirani, koma osati ndi mowa.
10 For our Father has poured out on you a spirit of deep sleep; he has shut your eyes, the prophets, and covered your heads, the seers. Yehova wakugonetsani tulo tofa nato. Watseka maso anu, inu aneneri; waphimba mitu yanu, inu alosi.
11 The whole vision is to you like words of a sealed scroll. When they give it to one who can read, saying, "Read this, please," he says, "I can't; it's sealed." Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”
12 When the scroll is given to one who cannot read, saying, "Read this," he says, "I can't read." Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
13 The Sovereign Father said: "Because this people comes near with its mouth and honors me with its lips, but its heart is far from me; their fear of me is a rule taught by men, Ambuye akuti, “Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo, ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso. Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
14 therefore, look, I will again do wonders with this people, wonder upon wonder; the wisdom of their wise men will perish, and the understanding of their discerning ones will vanish." Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira kuwachitira ntchito zodabwitsa; nzeru za anthu anzeru zidzatha, luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
15 Woe to those who go deep to hide their plans from our Father, whose deeds are done in the dark, who say, "Who sees us? Who knows us?" Tsoka kwa amene amayesetsa kubisira Yehova maganizo awo, amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti, “Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
16 How you twist everything around! Should the potter be treated like his clay—as if the thing made could tell its maker, "He didn't make me," or the thing shaped could tell the one who formed it, "He knows nothing"? Inu mumazondotsa zinthu ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya. Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti “Sunandipange ndi iwe?” Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti, “Iwe sudziwa chilichonse?”
17 Is it not just a little while before Lebanon will be turned into a fruitful field, and the fruitful field counted as a forest? Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde, ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?
18 On that day the deaf will hear the words of a scroll, and out of gloom and darkness the eyes of the blind will see. Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku, ndipo anthu osaona amene ankakhala mu mdima adzapenya.
19 The humble will find fresh joy in our Father, and the poor among mankind will rejoice in the Holy One of Israel, our Father. Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova; ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.
20 For the ruthless will be no more and the scoffer will be finished; all who are bent on evil will be cut off, Koma anthu ankhanza adzazimirira, oseka anzawo sadzaonekanso, ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.
21 those who with a word make a man out to be a sinner, who lay a snare for the one who defends justice at the gate, and with empty arguments turn aside the one in the right. Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa, kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.
22 Therefore this is what our Father says, who redeemed Abraham, concerning the house of Jacob: "No longer will Jacob be ashamed, no longer will his face grow pale. Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti, “Anthu anga sadzachitanso manyazi; nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
23 For when he sees his children, the work of my hands among them, they will keep my name holy; they will keep holy the Holy One of Jacob and stand in awe of our Father. Akadzaona ana awo ndi ntchito ya manja anga pakati pawo, adzatamanda dzina langa loyera; adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo, ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
24 Those who wander in spirit will come to understanding, and those who grumble will accept instruction." Anthu opusa adzapeza nzeru; onyinyirika adzalandira malangizo.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]